Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?
  • :-) Ngati mukuchita zinthu mwanzeru, kutumizirana mameseji kumakhala njira yothandiza kwambiri pa nkhani yolankhulana.

  • :-( Koma ngati simukuchita zinthu mwanzeru, kutumizirana mameseji kukhoza kuwononga mbiri yanu komanso kungachititse kuti anthu ena asiye kucheza nanu.

 Amene mumalemberana nawo

 Achinyamata ambiri amaona kuti kutumizirana mameseji pafoni ndi njira yabwino kwambiri yolankhulirana. Mameseji a pafoni amathandiza kuti muzicheza ndi aliyense amene muli ndi nambala yake. Izi zimadalira ngati makolo anu amakulolani kucheza ndi aliyense.

 Mtsikana wina dzina lake Lenore ananena kuti: “Bambo anga safuna kuti ineyo ndi mchemwali wanga tizicheza ndi anyamata pafoni tili tokha. Iwo amafuna kuti ngati tikufuna kucheza ndi anyamata, tiziimbirana nawo foni yam’chipinda chochezera anthu ena akumva zimene tikulankhulana.”

 Zimene muyenera kudziwa: Mukamangopereka nambala ya foni yanu kwa aliyense mukhoza kudziitanira mavuto.

 Mnyamata wina dzina lake Scott ananena kuti: “Munthu ukamangopereka nambala ya foni yako kwa aliyense umapezeka kuti ukulandira mameseji kapena zithunzi zimene sukuzifuna.”

 Mnyamata winanso dzina lake Steven ananena kuti: “Ukamakonda kulemberana mameseji ndi munthu yemwe si mtsikana kapena mnyamata mnzako, umayamba kukopeka naye mwachangu kwambiri.

 Baibulo limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Choncho muzigwiritsa ntchito foni mochenjera kuti musadzilowetse m’mavuto.

 Zimene zinachitikadi: Mtsikana wina dzina lake Melinda ananena kuti: “Mnyamata wina anali mnzanga ndipo tinkalemberana mameseji kwambiri. Ndinkaganiza kuti timangogwirizana kwambiri basi ndipo ndinkaona kuti panalibe vuto lililonse. Koma ndinadabwa tsiku lina akundiuza kuti wayamba kukopeka nane. Ndimaona kuti ndikanachita bwino ndikanapanda kumacheza naye kwambiri komanso kumamulembera mameseji ambiri ngati mmene ndinkachitiramo.”

 Taganizirani izi: Kodi mukuganiza kuti zimenezi zinakhudza bwanji ubwenzi wa Melinda ndi mnyamatayu?

 Lembani zimene Melinda akanachita. Kodi Melinda akanachita chiyani kuti mnyamata uja angokhala nzake popanda kukopana kapena kufunana?

 Zimene mumatumizirana

 Mameseji ndi osavuta kutumiza komanso amasangalatsa kulandira. Choncho zimakhala zosavuta kuiwala kuti anthu amatha kutanthauzira meseji molakwika.

 Zimene muyenera kudziwa: Mameseji a pa foni amatha kutanthauziridwa molakwika.

 “Ukamacheza pa mameseji sudziwa mmene munthu wakhudzidwira komanso mmene mawu ake akumvekera ngakhale utalemba zizindikiro zosonyeza kukhudzika. Zimenezi zingapangitse kuti musamvetsetsane.”​—Anatero mtsikana wina dzina lake Briana.

 Mtsikana winanso dzina lake Laura ananena kuti: “Ndikudziwa atsikana ena amene anawononga mbiri yawo ndipo amadziwika monga okopa amuna chifukwa cha mameseji amene amalembera anyamata.”

 Baibulo limanena kuti: “Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.” (Miyambo 15:28) Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Muziwerenganso meseji imene mwalemba musanaitumize.

 Nthawi imene mumatumizirana

 Mungachite bwino kudziikira malamulo okhudza nthawi imene mumatumizirana mameseji ndi anthu.

 Zimene muyenera kudziwa: Ngati simusamala ndi mmene mumalembera mameseji, anthu adzakuonani ngati wamwano ndipo akhoza kumadana nanu m’malo mofuna kucheza nanu.

 Mtsikana wina dzina lake Allison ananena kuti: “Zimakhala zosavuta kuyamba kutumizirana mameseji malo ndi nthawi yolakwika. Ineyo nthawi zina ndimapezeka kuti ndikucheza ndi munthu wina kapena tikudya koma nthawi yomweyonso n’kumatumizirana mameseji ndi munthu wina.”

 Mtsikana winanso dzina lake Anne ananena kuti: “N’zoopsa kumalemberana mameseji kwinaku ukuyendetsa galimoto. Umakhala wotanganidwa ndi mameseji moti suona bwino pamsewu ndipo zimenezi zingachititse ngozi.”

 Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:​1, 7) Choncho muyenera kukhala ndi nthawi yosiya kulemba mameseji monga mmene mumachitira ndi nthawi yosiya kaye kulankhula.

 Zofunika kukumbukira pa nkhani ya mameseji

Amene mumalemberana nawo

  •  ;-) Muzimvera malangizo amene makolo anu anakupatsani.​—Akolose 3:20.

  •  ;-) Musamangopereka nambala ya foni yanu kwa aliyense. Mukamakana mwaulemu kuuza munthu zinthu zimene simukufuna kuti azidziwe monga nambala ya foni yanu, mumaphunzira kuchita zinthu mwanzeru. Zimenezi zidzakuthandizani mukadzakula.

  •  ;-) Musachite kutchuka ndi nkhani yotumizira ena mameseji okopa. Ngati mutayamba kukopana, mukhoza kugwa m’mavuto.

 Briana ananena kuti: “Makolo anga amaona kuti ndimagwiritsa ntchito foni mwanzeru. Zimenezi zapangitsa kuti azindikhulupirira kwambiri moti amandilola kusankha ndekha anthu amene ndikufuna kukhala ndi manambala a foni yawo.”

Zimene mumatumizirana

  •  ;-)Musanayambe kulemba meseji, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi ndi zofunika kuti ndimuuze pomulembera meseji?’ Mukapeza yankho lakuti ayi, zingakhale bwino kumuuza pomuimbira foni kapena kudikira kuti mudzalankhulane pamasom’pamaso.

  •  ;-)Musamalembe zinthu zomwe mukuona kuti simukanamasuka kunena mukanakhala kuti mukulankhulana pamasom’pamaso. Pa nkhaniyi mtsikana wina wa zaka 23 dzina lake Sarah ananena kuti: “Ngati munthu ukuuma pakamwa kunena zinthuzo ndiye sukuyeneranso kuzilemba.”

 Mnyamata wina dzina lake Sirvan ananena kuti: “Munthu wina akakutumizira meseji yokhala ndi chithunzi choipa, ndibwino kuuza makolo ako. Zimenezi zingakuteteze komanso zingachititse kuti makolowo azikukhulupirira.”

Nthawi imene mumatumizirana

  •  ;-)Muzisankhiratu nthawi imene simufunika kugwiritsa ntchito foni. Pa mfundo imeneyi mtsikana wina dzina lake Olivia ananena kuti: “Ndimaonetsetsa kuti ndisakhale ndi foni nthawi ya chakudya kapena ndikamawerenga. Ndimaithimitsanso nthawi ya misonkhano yachikhristu n’cholinga choti ndisamalakelake kuona mameseji.”

  •  ;-)Muzichita zinthu moganizira ena. (Afilipi 2:4) Musamalemberane mameseji ndi munthu wina nthawi imene mukucheza pamasom’pamaso ndi munthu winanso.

 Mtsikana wina dzina lake Janelly ananena kuti: “Ndinadziikira lamulo lakuti ndisamalemberane mameseji ndi anthu ena nthawi imene ndikucheza ndi anzanga pokhapokha ngati mesejiyo ili yofunika kwambiri. Sindimaperekanso nambala yanga ya foni kwa anthu amene sindicheza nawo kwambiri.”