Miyambo 15:1-33

  • Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo (1)

  • Maso a Yehova ali paliponse (3)

  • Pemphero la munthu wowongoka mtima limasangalatsa Mulungu (8)

  • Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana (22)

  • Kuyamba waganiza usanayankhe (28)

15  Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+  2  Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+Koma pakamwa pa zitsiru pamangolankhula mawu opusa.  3  Maso a Yehova ali paliponse,Amaona anthu oipa ndi abwino omwe.+  4  Lilime lodekha* lili ngati mtengo wa moyo,+Koma mawu achinyengo amachititsa kuti anthu ataye mtima.  5  Munthu wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+Koma munthu wochenjera amamvera ena akamudzudzula.+  6  Mʼnyumba ya munthu wolungama muli chuma chambiri,Koma zokolola za munthu woipa zimamubweretsera mavuto.+  7  Milomo ya munthu wanzeru imafalitsa zimene akudziwa,+Koma mtima wa munthu wopusa suchita zimenezo.+  8  Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa kwa Yehova,+Koma pemphero la munthu wowongoka mtima limamusangalatsa.+  9  Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+Koma amakonda munthu amene amachita chilungamo.+ 10  Chilango chimaoneka choipa* kwa munthu amene wasiya njira yabwino,+Koma aliyense amene amadana ndi kudzudzulidwa adzafa.+ 11  Ngati Yehova amaona bwinobwino amene ali mʼManda* ndiponso malo achiwonongeko,*+ Ndiye kuli bwanji zimene zili mʼmitima ya anthu?+ 12  Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akumudzudzula.+ Iye sadzapempha malangizo kwa anthu anzeru.+ 13  Mtima wachimwemwe umapangitsa kuti nkhope izioneka yosangalala,Koma munthu sasangalala ngati mtima ukumupweteka.+ 14  Anthu anzeru* amayesetsa kuti adziwe zinthu,+Koma pakamwa pa anthu opusa pamasangalala ndi zinthu zopusa.+ 15  Masiku onse a munthu amene akukumana ndi mavuto amakhala oipa,+Koma munthu amene ali ndi mtima wosangalala* amachita phwando nthawi zonse.+ 16  Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+Kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri koma uli ndi nkhawa.*+ 17  Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+Kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa* koma pali chidani.+ 18  Munthu wosachedwa kupsa mtima amayambitsa mkangano,+Koma munthu amene sakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+ 19  Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+Koma njira ya munthu wowongoka mtima ili ngati msewu wosalazidwa bwino.+ 20  Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma munthu wopusa amanyoza mayi ake.+ 21  Munthu wopanda nzeru amasangalala ndi uchitsiru,+Koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+ 22  Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana,*Koma alangizi akachuluka zinthu zimayenda bwino.+ 23  Munthu amasangalala akapereka yankho labwino,*+Ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+ 24  Munthu amene ndi wozindikira ali panjira yokwezeka yopita kumoyo,+Ndipo amapewa kuyenda mʼnjira yotsikira ku Manda.*+ 25  Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+Koma adzateteza malire a malo a mkazi wamasiye.+ 26  Yehova amadana ndi ziwembu za munthu woipa,+Koma mawu osangalatsa ndi oyera kwa iye.+ 27  Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake,+Koma amene amadana ndi ziphuphu adzakhalabe ndi moyo.+ 28  Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamangolankhula zoipa. 29  Yehova ali kutali ndi anthu oipa,Koma amamva pemphero la anthu olungama.+ 30  Maso owala amapangitsa* kuti mtima usangalale.Uthenga wabwino umachititsa kuti mafupa akhale amphamvu.*+ 31  Munthu amene amamvetsera chidzudzulo chopatsa moyo,Amakhala pakati pa anthu anzeru.+ 32  Aliyense amene amakana malangizo amanyoza moyo wake,+Koma amene amamvetsera akadzudzulidwa amakhala wozindikira.+ 33  Kuopa Yehova nʼkumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+Ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “moleza mtima.”
^ Kapena kuti, “Lilime lochiritsa.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
^ Kapena kuti, “chowawa kwambiri.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndiponso Abadoni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wanzeru.”
^ Kapena kuti, “wabwino.”
^ Kapena kuti, “koma uli wosokonezeka maganizo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “yodyetsedwa bwino.”
^ Kapena kuti, “sakambirana moona mtima.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “manyazi.”
^ Kapena kuti, “Kuyangʼana munthu ndi nkhope yachimwemwe kumapangitsa.”
^ Kapena kuti, “umanenepetsa mafupa.”