Mawu a Mulungu Amatithandiza Kuti Tizichita Zinthu Mwadongosolo
“Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru. Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.”—MIY. 3:19.
NYIMBO: 105, 107
1, 2. (a) Kodi anthu ena ali ndi maganizo otani pa nkhani yoti Mulungu ali ndi gulu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
KODI Mulungu ali ndi gulu? Anthu ena amanena kuti: “Munthu safunika kukhala m’gulu linalake kuti azilambira Mulungu. Amati chofunika ndi kungokhala pa ubwenzi ndi Mulunguyo.” Koma kodi maganizo amenewa ndi olondola? Pali umboni wosonyeza kuti tiyenera kukhala m’gulu la Mulungu kuti tizimulambira bwino.
2 M’nkhaniyi tiona kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo ndipo amathandiza anthu ake kuti azichita zinthu mogwirizana. Tionanso zimene tiyenera kuchita tikalandira malangizo a Yehova ndi gulu lake. (1 Akor. 14:33, 40) Kuyambira nthawi ya atumwi, Malemba akhala akuthandiza Akhristu kuti azigwira bwino ntchito yolalikira uthenga wabwino. Tikamatsatira Mawu a Mulungu komanso malangizo a gulu lake, timathandiza kuti mpingo ukhale woyera, wamtendere komanso wogwirizana.
YEHOVA NDI MULUNGU WADONGOSOLO
3. Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo?
3 Chilengedwe chimasonyeza kuti Mulungu ndi wadongosolo. Baibulo limati: “Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru. Miy. 3:19) Anthufe timangodziwa “kambali kakang’ono chabe ka zochita za [Mulungu], ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Komabe zochepa zimene timadziwazi, zimatithandiza kuzindikira kuti mapulaneti, nyenyezi komanso milalang’amba zinapangidwa mwadongosolo kwambiri. (Sal. 8:3, 4) Milalang’amba ili ndi nyenyezi mamiliyoni ambirimbiri koma zonse zimayenda mwadongosolo. Pulaneti iliyonse ili ndi malo amene imayenda mozungulira dzuwa ndipo zimakhala ngati mapulanetiwa akutsatira malamulo apamsewu. Zonsezi zimatheka chifukwa Yehova ndi amene anakonza zoti mapulaneti ndi nyenyezi ziziyenda mwadongosolo. Iye anapanga kumwamba ndi dziko lapansi “mwanzeru.” Choncho tiyenera kumutamanda, kumulambira komanso kukhala okhulupirika kwa iye.—Sal. 136:1, 5-9.
Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.” (4. N’chifukwa chiyani asayansi alephera kupeza mayankho a mafunso ambiri?
4 Asayansi agwiritsa ntchito zinthu zimene adziwa zamlengalenga komanso zapadzikoli popanga zinthu zomwe zathandiza anthu m’njira zosiyanasiyana. Komabe iwo sanathe kupeza mayankho a mafunso ambiri. Mwachitsanzo, sangatiuze kuti chilengedwe chinakhalapo bwanji komanso kuti n’chifukwa chiyani anthufe ndiponso zinthu zina zamoyo zili padzikoli. Komanso anthu sangafotokoze chomwe chimachititsa kuti tizifuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlal. 3:11) N’chifukwa chiyani amalephera kuyankha mafunso ngati amenewa? Chifukwa china n’choti asayansi ndi anthu ena amati kulibe Mulungu ndipo amalimbikitsa mfundo yoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma Baibulo limapereka mayankho ogwira mtima a mafunso ofunikawa.
5. Kodi malamulo a m’chilengedwe amatithandiza bwanji?
5 Yehova anaika malamulo osiyanasiyana m’chilengedwe ndipo malamulowo sasintha. Anthu ogwira ntchito zamagetsi, mapulambala, mainjiniya, oyendetsa ndege komanso ochita opaleshoni amadalira malamulo a m’chilengedwewa. Mwachitsanzo, munthu aliyense amakhala ndi mtima pamalo ofanana. Izi zimathandiza kuti madokotala akamapanga munthu opaleshoni, asamachite kung’amba malo osiyanasiyana pofufuza mtima. Tonsefe timadziwanso kuti ngati titadumpha pamwamba kwambiri tikhoza kugwa n’kufa. Mwachidule tingati kutsatira malamulo a m’chilengedwe kumathandiza kuti tikhalebe ndi moyo.
MULUNGU AMATHANDIZA ANTHU AKE KUTI AZICHITA ZINTHU MWADONGOSOLO
6. Tikudziwa bwanji kuti Mulungu amafuna kuti gulu la anthu ake lizichita zinthu mwadongosolo?
6 Monga taonera, Yehova analenga zinthu mwadongosolo. Izi zikusonyeza kuti iye amafunanso kuti anthu ake azichita zinthu mwadongosolo. Choncho anatipatsa Baibulo kuti lizititsogolera. Munthu amene satsatira mfundo za Mulungu komanso malangizo a gulu lake amakumana ndi mavuto ambiri ndipo sasangalala.
7. N’chiyani chimasonyeza kuti mabuku a m’Baibulo ndi ogwirizana?
7 Baibulo ndi buku lapadera lochokera kwa Mulungu. Anthu ena amati Baibulo ndi buku lolembedwa ndi anthu ndipo limangonena za Ayuda ndi Akhristu. Koma izi si zoona chifukwa Mulungu ndi amene anasankha anthu oti alembe Baibulo, mfundo zoti alembe komanso nthawi yoyenera kuzilemba. N’chifukwa chake mabuku onse a m’Baibulo ndi ogwirizana. Nkhani yaikulu kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso ndi yoti Yehova ndiye woyenera Genesis 3:15; Mateyu 6:10; Chivumbulutso 11:15.
kulamulira komanso kuti adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokwaniritsa cholinga chake. Mfumu ya Ufumuwu ndi Khristu amenenso ndi “mbewu” yolonjezedwa.—Werengani8. N’chiyani chikusonyeza kuti Aisiraeli ankachita zinthu mwadongosolo?
8 Aisiraeli ankatsatira Chilamulo cha Mulungu ndipo ankachita zinthu mwadongosolo. Mwachitsanzo, panali akazi “amene anali kutumikira mwadongosolo pachipata cha chihema chokumanako.” (Eks. 38:8) Komanso pamene Asiraeli ankachoka ku Iguputo ankachita zinthu mwadongosolo pochoka pamalo komanso ponyamula chihema. Kenako Mfumu Davide inakonza zoti Alevi ndi ansembe azigwira ntchito zosiyanasiyana pakachisi. (1 Mbiri 23:1-6; 24:1-3) Ndipotu Asiraeli akamamvera Yehova ankakhala mogwirizana komanso mwamtendere.—Deut. 11:26, 27; 28:1-14.
9. N’chiyani chikusonyeza kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachita zinthu mwadongosolo?
9 M’nthawi ya atumwi, Yehova anathandizanso kuti mipingo izichita zinthu mwadongosolo. Panali bungwe lolamulira limene linkapereka malangizo oti mipingoyo izitsatira. (Mac. 6:1-6) Poyamba atumwi ndi amene anali m’bungwe lolamulira koma kenako abale ena anasankhidwa kuti akhalenso m’bungweli. (Mac. 15:6) Mipingo inkalandiranso malangizo kudzera m’makalata ouziridwa olembedwa ndi abale a m’bungwe lolamulira komanso abale ena amene ankagwira ntchito mogwirizana ndi bungwe lolamuliralo. (1 Tim. 3:1-13; Tito 1:5-9) Kodi mipingo inkapindula bwanji ikamatsatira malangizo a bungwe lolamulira?
10. Kodi chinkachitika n’chiyani mipingo ikamatsatira malamulo ochokera ku bungwe lolamulira? (Onani chithunzi patsamba 9.)
10 Werengani Machitidwe 16:4, 5. Abale amene ankatumidwa ndi bungwe lolamulira ankapereka ku mipingo “malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula.” Mipingo ikamatsatira malamulowo, ‘inkalimba m’chikhulupiriro ndipo chiwerengero chinkapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.’ Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani?
KODI INUYO MUMATSATIRA MALANGIZO?
11. Kodi abale audindo ayenera kuchita chiyani akalandira malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa?
11 Kodi abale amene ali m’Makomiti a Nthambi, Makomiti a Dziko komanso oyang’anira madera ndi akulu ayenera kuchita chiyani akalandira malangizo ochokera ku gulu la Yehova? Mawu a Yehova amatilimbikitsa kuti tizimvera amene akutsogolera komanso tiziwagonjera. (Deut. 30:16; Aheb. 13:7, 17) Mtima wopezera ena zifukwa komanso wosafuna kuuzidwa zochita sufunika m’gulu la Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti mtima umenewu ungachititse kuti mumpingo musakhalenso mtendere, mgwirizano komanso chikondi. M’bale wokhulupirika sangafune kukhala ndi mtima wopanda ulemu komanso wosakhulupirika ngati wa Diotirefe. (Werengani 3 Yohane 9, 10.) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi ineyo ndimalimbikitsa abale ndi alongo kuti akhale okhulupirika kwa Yehova? Nanga kodi ndimatsatira mwamsanga malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa?
12. Kodi akulu ndi atumiki othandiza amaikidwa bwanji masiku ano?
12 Bungwe Lolamulira linasintha njira yoikira akulu komanso atumiki othandiza pa udindo. Mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2014 munali nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” yofotokoza za kusinthaku. Nkhaniyo inanena kuti m’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulira linkapatsa oyang’anira oyendayenda udindo wovomereza kuti abale akhale akulu kapena atumiki. Choncho kuyambira pa September 1, 2014, oyang’anira madera akhala akuika pa udindo akulu ndi atumiki othandiza. Woyang’anira dera amayesetsa kuwadziwa bwino abale amene akuganiziridwawo ndipo ngati n’kotheka amayenda nawo mu utumiki. Amaonanso mmene mabanja awo akuchitira zinthu. (1 Tim. 3:4, 5) Ndiyeno bungwe la akulu limodzi ndi woyang’anira derayo amaona mfundo za m’Malemba pokambirana ngati m’bale akuyeneradi kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza.—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; 1 Pet. 5:1-3.
13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamvera malangizo a akulu?
13 Ndi bwino kutsatira malangizo ochokera m’Malemba amene akulu amatipatsa. Akulu amapereka malangizo chifukwa choti amatikonda ndipo amafuna kuteteza mpingo. (1 Tim. 6:3) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi malangizo amene Paulo anapereka kumpingo wa Atesalonika okhudza anthu oyenda mosalongosoka. Pa nthawiyo panali anthu ena amene ‘sankagwira ntchito koma ankangokonda kulowerera nkhani zosawakhudza.’ Akulu anawapatsa malangizo koma anthuwo sanamvere. Ndiyeno Paulo anauza mpingowo kuti anthu oterowo ndi ofunika ‘kuwaika chizindikiro n’kusiya kuchitira nawo zinthu limodzi.’ Komabe apa Paulo sankatanthauza kuti aziwaona ngati adani awo. (2 Ates. 3:11-15) Masiku ano, akulu angakambe nkhani yochenjeza anthu za munthu wina mumpingo amene akupitirizabe kuchita khalidwe loipa, monga kuchita chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira. (1 Akor. 7:39) Kodi inuyo mumatani akulu akakamba nkhani yotereyi? Ngati mwadziwa munthu amene wachita zimene zikunenedwazo, kodi mumasiyadi kuchita naye zinthu? Zimenezi zingamuthandize kuti azindikire kulakwa kwake n’kusintha. [1]
MUZITHANDIZA KUTI MPINGO UKHALEBE WOYERA, WAMTENDERE KOMANSO WOGWIRIZANA
14. Kodi tingathandize bwanji kuti mpingo ukhalebe woyera?
14 Tikamatsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu tingathandize kuti mpingo ukhale woyera. Taganizirani zimene zinachitika mumpingo wa Korinto wakale. Paulo anadzipereka kwambiri kulalikira mumzinda wa Korinto komanso ankakonda Akhiristu akumeneko. (1 Akor. 1:1, 2) Ndiye mukuganiza kuti anamva bwanji atazindikira kuti m’bale wina ankachita chiwerewere ndipo akulu ankangomulekerera? Paulo analangiza akuluwo kuti apereke munthuyu kwa Satana kapena kuti amuchotse mumpingo. Kuti mpingo ukhalebe woyera akuluwo anayenera kuchotsa “chofufumitsa.” (1 Akor. 5:1, 5-7, 12) Tikamatsatira malangizo a Yehova pa nkhani ya ochotsedwa, timathandiza kuti mpingo ukhale woyera. Izi zimathandizanso kuti munthuyo alape n’kupempha Yehova kuti amukhululukire.
15. Kodi tingatani kuti tisasokoneze mtendere wamumpingo?
15 Koma mumpingo wa Korinto munalinso vuto lina. Abale ena ankatengera Akhiristu anzawo kukhoti. Ndiyeno Paulo anawafunsa kuti: “Bwanji osangolola kulakwiridwa?” (1 Akor. 6:1-8) Zoterezi zimachitikanso masiku ano. Nthawi zina abale amayambana chifukwa choti nkhani za bizinesi zimene anagwirizana sizinayende bwino ndipo ndalama zalowa m’madzi. Mwinanso chingakhale chifukwa choti wina akuganiza kuti mnzake wamubera ndalama. Zikatere ena amatengera anzawo kukhoti. Koma Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ndi bwino kulola kulakwiridwa kusiyana ndi kunyozetsa dzina la Mulungu kapena kusokoneza mtendere wampingo. [2] Choncho pakakhala mavuto kapena kusamvana, ndi bwino kutsatira malangizo a Yesu. (Werengani Mateyu 5:23, 24; 18:15-17.) Tikamachita zimenezi timalimbikitsa mtendere m’gulu la Yehova.
16. N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu amagwirizana?
16 Baibulo limafotokoza chifukwa chake anthu a Mulungu ayenera kukhala ogwirizana. Paja wamasalimo anaimba kuti: “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” (Sal. 133:1) Aisiraeli akamamvera Yehova, ankakhala ogwirizana ndipo ankachita zinthu mwadongosolo. Yehova analoseranso za anthu ake kuti: “Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola.” (Mika 2:12) Iye anauziranso Zefaniya kulosera kuti: “Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera [kutanthauza choonadi cha m’Malemba] kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.” (Zef. 3:9) Ndi mwayi waukulu kulambira Yehova mogwirizana.
17. Ngati munthu wina wachimwa, kodi akulu ayenera kuchita chiyani kuti mpingo ukhalebe woyera komanso wogwirizana?
17 Kuti mpingo ukhale woyera ndiponso wogwirizana, akulu ayenera kuthandiza mwamsanga komanso mwachikondi munthu amene wachita tchimo. Paulo ankadziwa kuti Mulungu ndi wachikondi koma sachita zinthu mongotengeka ndipo salekerera zoipa. (Miy. 15:3) Choncho Paulo analemba kalata yoyamba yopita kwa Akorinto ndipo m’kalatayo munali malangizo achikondi koma amphamvu. Patapita miyezi, anawalembera kalata yachiwiri yomwe imasonyeza kuti akulu anatsatira malangizo ake ndipo zinthu zinayamba kuyenda bwino. Munthu akayamba kusochera mosazindikira, abale oyenerera mwauzimu ayenera kumuthandiza ndi mzimu wofatsa.—Agal. 6:1.
18. (a) Kodi malangizo a m’Mawu a Mulungu anathandiza bwanji mipingo m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Apa zikuonekeratu kuti malangizo a m’Malemba anathandiza mpingo wa ku Korinto komanso mipingo ina kuti ikhale yoyera, yamtendere komanso yogwirizana. (1 Akor. 1:10; Aef. 4:11-13; 1 Pet. 3:8) Izi zinathandiza kuti abale ndi alongo alalikire uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Masiku anonso, anthu a Mulungu ndi ogwirizana ndipo izi zikuchititsa kuti azitha kulalikira uthenga wabwino padziko lonse. Nkhani yotsatira ikusonyeza kuti anthu a Mulunguwa amaona kuti Baibulo ndi buku lapadera ndipo amafunitsitsa kulemekeza Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.—Sal. 71:15, 16.
^ [1] (ndime 13) Onani m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 134 mpaka 136.
^ [2] (ndime 15) Kuti mudziwe zinthu zimene zingachititse Mkhristu kuganiza zotengera Mkhristu mnzake kukhoti, onani buku lakuti, Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’? tsamba 223, mawu a m’munsi.