Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumwetulira Ndi Mphatso Yofunika Kugawana

Kumwetulira Ndi Mphatso Yofunika Kugawana

KODI mumatani munthu wina akamakumwetulirani? Mwachidziwikire nanunso mumamwetulira ndipo mumasangalala. Kumwetulira n’kopatsirana moti anzathu kapena anthu amene sitikuwadziwa akatimwetulira, timamva bwino ndipo nafenso timawamwetulira. Mayi wina dzina lake Magdalena ananena kuti: “Mwamuna wanga Georg adakali moyo ankamwetulira mosangalatsa. Akamandiyang’ana akumwetulira ndinkamva bwino ndipo ndinkasangalala.”

Munthu akamamwetulira amasonyeza kuti wasangalala komanso kuti zinthu zikumuyendera bwino. Magazini ina ya akatswiri a zamaganizo inanena kuti: “Zikuoneka kuti kumwetulira n’kwachibadwa.” Magaziniyi inanenanso kuti ngakhale mwana wobadwa kumene amatha “kuzindikira mosavuta ngati munthu akusangalala kapena ayi akangoona nkhope yake.” Inanenanso kuti: “Munthu akamamwetulira, anthu ena amatha kudziwa mmene akumvera mumtima mwake ndipo zimawathandiza kudziwa mmene angachitire zinthu ndi munthuyo.”Observer.

Akatswiri a pa yunivesite ya Harvard ku United States anasankha anthu okalamba pochita kafukufuku wofuna kudziwa mmene anthu amamvera akaona mmene nkhope za amene akuwasamalira zikuonekera. Ochita kafukufukuwo ananena kuti anthuwo akaona kuti amene akuwasamalirawo “akuoneka ansangala, achifundo komanso achikondi” ankamva bwino ndipo ankayamba kupezako bwino. Koma owasamalirawo akamaoneka osasangalala, nawonso ankakhala okhumudwa ndipo matenda awo ankakula.

Mukamamwetulira nanunso zimakuyenderani bwino. Mwachitsanzo, kafukufuku amasonyeza kuti munthu akamamwetulira amasiya kudzikayikira, amasangalala ndiponso amachepetsa nkhawa. Koma munthu akamangokhala ndwii zinthu sizimuyendera bwino.

“NDINKALIMBIKITSIDWA” NDIKAONA ENA AKUMWETULIRA

Magdalena amene tamutchula kale uja anali wa Mboni za Yehova pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Iye limodzi ndi achibale ake ena anatumizidwa kumsasa wozunzirako anthu ku Germany chifukwa chokana kutsatira mfundo za chipani cha Nazi. Iye ananena kuti: “Nthawi zina oyang’anira ndende sankatilola kuti tizilankhulana ndi akaidi anzathu. Komabe sakanatha kutiletsa kulankhulana pogwiritsa ntchito nkhope. Ndinkati ndikaona amayi komanso mchemwali wanga akumwetulira zinkandilimbikitsa kwambiri ndipo ndinkaona kuti ndikwanitsa kupirira zivute zitani.”

Koma mwina inuyo mumaona kuti simungakwanitse kumamwetulira nthawi zonse chifukwa cha mavuto amene mukukumana nawo. Ngati ndi choncho, muyenera kukumbukira kuti timasangalala kapena kukhumudwa chifukwa cha zimene tikuganiza. (Miyambo 15:15; Afilipi 4:8, 9) Choncho ngakhale kuti zingaoneke ngati zovuta, mungachite bwino kumaganizira zinthu zosangalatsa. * Pali anthu ambiri amene akwanitsa kuchita zimenezi chifukwa chowerenga Baibulo komanso kupemphera kwa Mulungu. (Mateyu 5:3; Afilipi 4:6, 7) Ndipotu m’Baibulo mawu akuti “kusangalala” komanso “chimwemwe” amapezeka maulendo ambirimbiri. Choncho muziyesetsa kumawerenga chaputala chimodzi kapena awiri tsiku lililonse. Ngati mutayesetsa kuchita zimenezi nanunso mukhoza kukhala ndi chizolowezi chomwetulira.

Komanso musamadikire kuti ena ayambe kukumwetulirani. Muziyamba ndinuyo. Muziona kuti kumwetulira ndi mphatso imene Mulungu anakupatsani n’cholinga choti muzisangalala komanso kuti muzithandiza anthu ena kukhala osangalala.

^ ndime 8 Onani nkhani yakuti “Kodi Mumachita ‘Phwando Nthawi Zonse’?” mu Galamukani! ya November 2013.