NKHANI YA PACHIKUTO
N’zotheka Kumasangalalabe Ngakhale Muli Ndi Mavuto!
Pa mfundo zitatu zili m’munsizi, kodi ndi iti yomwe mukuona kuti ingakuthandizeni kuti muzisangalala?
-
mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanu
-
chibadwa chanu
-
mmene mumaonera zinthu
ENA akhoza kusankha choyambacho n’kumaganiza kuti angamasangalale pokhapokha . . .
-
“atakhala ndi ndalama zambiri”
-
“atakhala ndi banja losangalala”
-
“atakhala ndi moyo wathanzi”
Koma kunena zoona, munthu akhoza kukhala wosangalala ngati amaona zinthu moyenera. Tikunena zimenezi chifukwa tingathe kusintha mmene timaonera zinthu n’kumasangalala. Koma n’zovuta, mwinanso n’zosatheka kusintha chibadwa chathu ndiponso zinthu zimene zikutichitikira pa moyo wathu.
“MANKHWALA OCHIRITSA”
Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” (Miyambo 17:22) M’mawu ena tinganene kuti, munthu amene amaona zinthu moyenera, akakumana ndi mavuto, safulumira kuimika manja, koma amaphunzirapo kanthu n’kumayesetsa kuchita zinthu zabwino. Koma munthu amene saona zinthu moyenera amafulumira kugwa mphwayi n’kumaona kuti palibenso chanzeru chimene angachite.
Koma anthu ena sangagwirizane ndi mfundo imeneyi ndipo angamanene kuti:
-
‘Sindingamadzivutitse n’kumamwetulira kuti ena aziona ngati zikundiyendera chonsecho mavuto ali tho.’
-
‘Palibe chimene chingasinthe pa moyo wanga ngakhale nditamaganizira zinthu zabwino.’
-
‘Kuli bwino ndizilimbana ndi mavuto enieniwo m’malo momangolota kuti atha.’
Maganizo amenewa angaoneke ngati omveka ndithu. Komabe muyenera kudziwa kuti kukhala ndi maganizo oyenera n’kothandiza kwambiri. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tione zitsanzo zotsatirazi.
Alex ndi Brian akugwira ntchito pakampani imodzi ndipo abwana awo awapatsa ntchito zosiyana. Onsewo akugwira ntchitozo molimbikira ndipo atamaliza abwanawo akuuza aliyense zimene analakwitsa pogwira ntchito yake.
-
Alex: “Komatu osanama, munthune ndinayesetsa kugwira ntchitoyi ndi mtima wonse. Koma ayi ndithu zandikanikanso. Ine ndiye basi, ntchito imeneyi sindingaikwanitse. Palibe chifukwa choti ndizivutika n’kuyeseranso.”
-
Brian: “Abwana anga andiuza kuti ndachita bwino, koma andiuzanso zina zimene ndalakwitsa. Ndaphunzirapo kanthu pa zimene andiuzazi ndipo ndiyesetsa kuti ntchitoyi ndidzaigwire bwino ulendo wina.”
KODI MUKUGANIZA BWANJI?
-
Kodi mukuganiza kuti pakatha miyezi 6, ndi ndani pakati pa Alex ndi Brian amene angakhale waluso pa ntchito yake?
-
Tiyerekeze kuti inuyo ndi bwana, kodi ndi ndani pakati pa awiriwa amene mungakonde kuti azigwirabe ntchito pakampani yanu?
-
Nanga kodi inuyo mukalephera kuchita zomwe mumafuna, mumaganiza ngati Alex kapena Brian?
Alice ndi Brenda amasowa ocheza nawo. Tiyeni tione zimene aliyense amachita pofuna kuthetsa vuto lake.
-
Alice amangochita zake basi ndipo sakonda kuthandiza ena. Amachitira ena zabwino pokhapokha nawonso akamuchitira zinazake. Amakonda kunena kuti, ‘Ndizivutikiranji n’kuthandiza anthu oti sandichitira china chilichonse?’
-
Brenda amayesetsa kukonda komanso kuthandiza ena ngakhale anthuwo atakhala osayamika. Amayesetsa kutsatira mfundo yofunika kwambiri yomwe Yesu ananena yoti anthufe tiyenera kumachitira ena zimene tingafune kuti enawo atichitire. (Luka 6:31) Brenda amaona kuti chofunika kwambiri n’kuchitira ena zabwino ngakhale iwowo asamuchitire zabwino.
KODI MUKUGANIZA BWANJI?
-
Kodi pakati pa Alice ndi Brenda, ndi ndani amene mungakonde kuti akhale mnzanu?
-
Kodi mukuganiza kuti ndi ndani amene akuoneka kuti amasangalala?
-
Ngati nanunso mumasowa wocheza naye, kodi mumachita zinthu ngati Alice kapena Brenda?
Mwina mumadziwa anthu ena amene ali ndi maganizo abwino angati a Brian ndi Brenda. N’kutheka kuti nanunso mumaganiza choncho. N’zosakayikitsa kuti mumadziwa zoti munthu akhoza kukhala wosangalala kapena wosasangalala chifukwa cha mmene amaonera zinthu. Koma bwanji ngati mumachita zinthu ngati Alex komanso Alice? Onani mfundo zitatu za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuti muziona zinthu moyenera mukakumana ndi mavuto.
1 MUSAMANGOGANIZIRA ZINTHU ZOGWETSA MPHWAYI
BAIBULO LIMATI: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.”—Miyambo 24:10.
ZIMENE ZIMACHITIKA: Munthu akamangoganizira zinthu zogwetsa mphwayi amafooka ndipo amalephera kupeza njira zothetsera mavuto ake.
CHITSANZO: Juliza sankasangalala pa nthawi imene anali mwana. Bambo ake anali chidakwa ndipo banja lawo linali losauka. Nthawi zonse ankangokhalira kusamuka. Poyamba Juliza ankangoganizira mavuto akewo koma kenako anadzasintha. Kodi chinamuthandiza n’chiyani? Juliza anati: “Baibulo linandithandiza kwambiri kuti ndisinthe mmene ndinkaonera zinthu ngakhale pamene zinthu sizinkayenda bwino m’banja lathu. Mpaka pano Baibulo limandithandiza kwambiri kuti ndisamangoganizira zinthu zogwetsa ulesi. Panopa ndikaona anthu amene akuchita zinazake zosandisangalatsa ndimawamvetsa, chifukwa ndimadziwa kuti pali chinachake chimene chikuwachititsa.”
Baibulo lili ndi mfundo zomwe zingathandize aliyense kukhala ndi maganizo oyenera ngakhale akukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, lemba la Aefeso 4:23 limalimbikitsa aliyense kuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.”
Lembali likusonyeza kuti aliyense angasinthe mmene amaganizira. N’chifukwa chake lanena kuti, “mukhale atsopano” pa nkhani ya mmene mumaganizira. Ndipotu zimenezi n’zofunika kumazichita nthawi zonse.
2 MUZIGANIZIRA ZINTHU ZABWINO
BAIBULO LIMATI: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”—Miyambo 15:15.
ZIMENE ZIMACHITIKA: Munthu akamangoganizira za mavuto ake amakhala “wosautsika” ndipo tsiku lililonse limakhala ‘loipa.’ Koma amene amaganizira zinthu zabwino, “amakhala wamtima wosangalala.” Ndiye kodi inuyo mungakonde kumaganizira zotani?
CHITSANZO: Bambo wina, dzina lake Yanko, anachitidwa opaleshoni ya mu ubongo maulendo angapo. Zimenezi zinachititsa kuti azivutika kuyenda komanso kuyankhula. A Yanko ankangokhala odandaula kwa zaka zambiri chifukwa ankaopa kuti vuto lawoli liwalepheretsa kuchita zimene ankafuna. Koma kenako anasintha maganizo. Kodi n’chiyani chinawathandiza? A Yanko anati: “M’malo momangoganizira zimene ndikulephera kuchita, ndimayesetsa kumaganizira zinthu zomwe zingandilimbikitse.”
Kuwerenga Baibulo n’kumene kwathandiza a Yanko kuti aziganizira zinthu zabwino. Iwo ananenanso kuti: “Kuwerenga Baibulo kumandithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera. Ndimaona kuti ndikhozabe kukwaniritsa zinthu zimene ndinkafuna poyamba. Koma chifukwa cha mmene zinthu zilili panopa, ndimayesetsa kuchita zochepa zimene ndingakwanitse. Ndiye ndikayamba kuganizira zinthu zofooketsa, ndimayesetsa kumaganizira zinthu zabwino ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndizisangalala.”
Zomwe a Yanko amachita, zikusonyeza kuti n’zotheka kusiya kuganizira zinthu zofooketsa n’kuyamba kumaganizira zinthu zabwino. Ngati nanunso mukukumana ndi vuto linalake, mungachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ndingalepheredi kuchita chilichonse chifukwa cha vutoli? Kodi ndafika posoweratu mtengo wogwira kapena pali zimene ndingachite kuti ndizikhalabe wosangalala?’ Zoterezi zikakuchitikirani muziganizira zinthu zabwino m’malo momangoganizira zinthu zofooketsa.
3 MUZITHANDIZA ANTHU ENA
BAIBULO LIMATI: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
ZIMENE ZIMACHITIKA: Munthu amene amathandiza ena amasangalala kwambiri. Tikutero chifukwa anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kuthandiza ena osati wongofuna kudzisangalatsa. (Afilipi 2:3, 4; 1 Yohane 4:11) Kuchitira ena zabwino kungatithandize kuti tizisangalalabe ngakhale tikukumana ndi mavuto.
CHITSANZO: Josué ali ndi chotupa cha pamsana chomwe chinayamba chifukwa choti mafupa a msana sanalumikizane bwinobwino. Zimenezi zimachititsa kuti azimva ululu woopsa. Komabe sikuti matenda akewa amamulepheretsa kuthandiza ena. Josué anati: “M’malo moganiza kuti, ‘Sindingakwanitse kuthandiza ena,’ ndimayesetsa kuganizira zimene ndingachite kuti ndiwathandize. Ndikamathandiza ena ndimaiwalako mavuto anga ndipo ndimakhala wosangalala.”
ZIMENE MUNGACHITE
Muziyesetsa kuganizira zomwe mungachite kuti muthandize ena. Mwachitsanzo, mukhoza kuphikira chakudya munthu wina amene akudwala. Mwinanso mungathandize munthu wina wokalamba pomugwirira ntchito zapakhomo.
Munthu akabzala mbewu amayesetsa kuzisamalira kuti zikule bwino. Mwachitsanzo, amazula udzu womwe ungapangitse kuti mbewuzo zisakule bwino komanso zisabereke zipatso. Mofanana ndi zimenezi inunso muzisiya msanga kuganizira zinthu zomwe zingakuchititseni kuti musamasangalale. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muziganizira kwambiri zinthu zabwino zomwe zingakuthandizeni kuti muzisangalala. Mukamachita zimenezi mudzaona kuti n’zotheka munthu kumasangalalabe ngakhale ali ndi mavuto.
Anthu ena amapewa kudya zakudya zinazake chifukwa choti zimawadwalitsa. Nanunso mungachite bwino kumapeweratu kuganizira zinthu zofooketsa chifukwa zingakuchititseni kuti musamasangalale