Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Aakulu Kapena Chilema?

Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Aakulu Kapena Chilema?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Aakulu Kapena Chilema?

“ULEMERERO wa anyamata ndiwo mphamvu yawo,” limatero lemba la Miyambo 20:29. Ngati mukuvutika m’thupi kapena ngati muli wolumala, mungaganize kuti lemba limeneli siligwira ntchito kwa inuyo. Koma zimenezi si zoona. Pali achinyamata ambiri olumala ndiponso odwala matenda aakulu, amene alimbana bwinobwino ndi mikwingwirima imene akukumana nayo. Olemba Galamukani! analankhula ndi anyamata anayi oterewa.

Hiroki, wa ku Japan, anabadwa ndi matenda a muubongo omwe amaumitsa ziwalo. Iye anati: “Ndimavutika kuimika mutu wanga, komanso sinditha kuyendetsa manja anga bwinobwino. Moti chilichonse amachita kundichitira.”

Natalie ndi mchimwene wake James ku South Africa, anabadwa ndi matenda enaake omwe si ofala kwambiri, amene amawalepheretsa kukula. Komanso Natalie ali ndi matenda opindika msana. Iye anati: “Kanayi konse andichitapo opaleshoni yowongola msana ndipo mapapo anga ndi ofooka chifukwa cha vutoli.”

Timothy, wa ku Britain, anam’peza ndi matenda ofooketsa thupi ali ndi zaka 17. Iye anati: “Pasanathe n’komwe miyezi iwiri, matendawa anandifooleratu moti sindinkatha ngakhale kuimirira.”

Danielle, wa ku Australia, anam’peza ndi matenda a shuga ali ndi zaka 19. Iye anati: “Anthu ena sazindikira kuti matenda angawa ndi woopsa chifukwa choti si matenda oonekera kwa anthu ayi. Komatu matendawa ndi oopsa kwambiri moti ndingathe kufa nawo.”

Ngati mukudwala matenda enaake aakulu kapena ngati muli wolumala, mawu amene ananena Hiroki, Natalie, Timothy, ndi Danielle akulimbikitsani kwambiri. Ngati muli ndi thanzi labwinobwino, mawu awowa akuthandizani kumvetsa anzanu amene akudwala matenda aakulu kapena amene ali olumala.

Olemba Galamukani!: Kodi chosautsa kwambiri n’chiyani pa vuto limene uli nalo?

Natalie: Kwa ineyo ndingati ndi mmene anthu amandiyang’anira. Nthawi zonse ndimakhala omangika kwambiri. Ndimangoona ngati kuti anthu onse maso awo amakhala pa ine nthawi zonse.

Danielle: Vuto la matenda a shuga n’lakuti umafunika kusankha zakudya mosamala, kusadya pang’ono kapena kwambiri, komanso kudziwa zakudya zoyenera kuchepetsa. Zakudya zinazake zikachepa kapena kuchuluka ndingathe kukomoka chifukwa chochuluka shuga m’thupi.

Hiroki: Ndili ndi njinga inayake ya anthu olumala, yomwe anaipanga mogwirizana ndi kulumala kwanga, ndipo pa tsiku ndimakhala maola 15 osatembenuka m’njira ina iliyonse. Chinanso n’chakuti tulo tanga n’tovuta kwambiri moti ndimatha kudzidzimuka ngakhale ndi kaphokoso kochepa chabe.

Timothy: Poyamba, vuto langa lalikulu linali kuvomereza kuti ndikudwaladi. Vuto langali ndinkachita nalo manyazi kwambiri.

Olemba Galamukani!: Kodi pali mavuto enanso amene umakumana nawo?

Danielle: Matenda a shuga amandifooketsa kwambiri. Ndimafunika kugona kwambiri kuposa anthu a msinkhu wanga. Komanso matenda ashugawa alibe mankhwala.

Natalie: Vuto lalikulu ndi kufupika kwanga komweku. Ndimavutika kwambiri kuchita zinthu za tsiku ndi tsiku monga kutsitsa zinthu zimene ndikufuna kugula. Moti ndikapita ndekha kumsika ndimavutika kwambiri.

Timothy: Ndimamva ululu wosaneneka komanso ndimavutika maganizo kwabasi. Ndisanayambe kudwala, ndinali munthu wazintchito kwambiri. Ndinali pantchito komanso ndinkayendetsa galimoto. Ndinkachita masewera osiyanasiyana, monga mpira wa miyendo komanso masewera ena. Koma pano tsiku lonse limathera pa chinjinga.

Hiroki: Ndili ndi vuto lolephera kulankhula bwinobwino. Motero ndimamangika kwambiri kuyambitsa nkhani. Nthawi zina manja anga amatha kutambasuka mwadzidzidzi moti ndimangozindikira kuti ndamenya munthu mwangozi. Ndiye ndimakanikanso kupepesa chifukwa cha vuto langa lolephera kulankhula bwinobwino.

Olemba Galamukani!: Ndiyeno n’chiyani chakuthandiza kupirira vuto lako?

Danielle: Ndimayesetsa kuganizira kwambiri zinthu zimene zikundiyendera bwino pamoyo wanga. Anthu a m’banja lathu amandikonda kwambiri, ndili ndi anzanga amene amandikonda mumpingo, ndipo chachikulu n’chakuti, Yehova Mulungu amandithandiza. Ndimayesetsanso kuti nthawi zonse ndizidziwa zinthu zimene atulukira zokhudza matenda a shuga. Ndimaona kuti ineyo ndi amene ndili ndi udindo woyang’anira thanzi langa ndipo ndimayesetsa kudziyang’anira bwino kwambiri.

Natalie: Kupemphera kumandithandiza kwambiri. Ndimayesetsa kuthana ndi vuto lililonse palokha. Kuti ndisamangodzimvera chisoni ndimakhala wotanganidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. Komanso ndili ndi makolo othandiza kwambiri, amene ndimamasuka kuwauza zakukhosi kwanga.

Timothy: Tsiku lililonse ndimaonetsetsa kuti ndachita chinachake chauzimu, ngakhale kwa kanthawi kochepa chabe. Mwachitsanzo, tsiku lililonse ndikangodzuka ndimawerenga lemba la tsiku. Chinanso ndimawerenga Baibulo pandekha ndiponso kupemphera, makamaka ngati zinthu sizikundiyendera bwino tsiku limenelo.

Hiroki: Sindilimbana ndi zinthu zimene sindingathe kuzisintha chifukwa kumeneku n’kungotaya nthawi pachabe. M’malo mwake ndimayesetsa kuchita zonse zimene ndingathe kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Mulungu, ndipo matenda angawa sindiwatenga ngati chinthu chodzikhululukira kuti ndisamawerenge Baibulo mokhazikika. Ndikamalephera kugona, ndimapezerapo mwayi wopitiriza kupemphera.—Onani Aroma 12:12.

Olemba Galamukani!: Kodi anthu ena akuthandiza bwanji?

Hiroki: Akulu nthawi zonse amandiyamikira chifukwa cha zinthu zimene ndimachita, ngakhale zitakhala zochepa chabe. Komanso abale ndi alongo amanditenga akamapita ku maulendo awo obwereza ndi kumaphunziro awo a Baibulo.—Onani Aroma 12:10.

Danielle: Mwina chimodzi mwa zinthu zimene zimandilimbikitsa kwambiri ndicho mawu oyamikira amene abale ndi alongo mumpingo amandiuza. Zimenezi zimandithandiza kuona kuti ndine munthu wofunika, ndipo zimandilimbikitsa kuti ndipitirize kuchita bwino.

Timothy: Kumpingo kwathu kuli mlongo wina wachikulire amene nthawi zonse amayesetsa kundilankhulitsa. Akulu ndiponso akazi awo amandilimbikitsanso kwambiri ndi kundipatsa malangizo osiyanasiyana ondithandiza pavuto langa. Mkulu wina, yemwe ali ndi zaka 84, anandithandiza kukhala ndi zolinga zimene ndingathe kuzikwaniritsa. Mtumiki wothandiza wina anandipempha kuti ndilowe naye m’munda, ndipo anakonza zoti tikalalikire m’gawo linalake lopanda zitunda, moti zinali zosavuta kuyenda m’gawolo ndi njinga yanga.—Onani Salmo 55:22.

Natalie: Ndikangolowa m’Nyumba ya Ufumu, abale ndi alongo amandilandira mwansangala. Nthawi zonse achikulire amandiuza mawu enaake olimbikitsa, ngakhale kuti nawonso pawokha akukumana ndi zokhoma.—Onani 2 Akorinto 4:16, 17.

Olemba Galamukani!: Kodi n’chiyani chimakuthandiza kuti usamangokhalira kudandaula?

Hiroki: Poti ndine wa Mboni za Yehova, ndili m’gulu la anthu amene ali ndi chiyembekezo. Ndikaganizira zimenezi ndimalimba mtima n’kusiya kudandaula.—Onani 2 Mbiri 15:7.

Danielle: Ndimaganizira za mwayi umene ndili nawo womvetsa cholinga cha Mulungu. Pali anthu ambirimbiri a thanzi labwinobwino, koma moyo wawo si wosangalatsa ngati wangawu.—Onani Miyambo 15:15.

Natalie: Ndimaona kuti ndimalimbikitsidwa ndikamacheza ndi anthu olimbikitsa. Chinanso ndicho kuwerenga nkhani za anthu ena amene akutumikira Yehova ngakhale kuti akukumana ndi mayesero. Komanso ndikamapita ku Nyumba ya Ufumu, ndimadziwa kuti ndikalimbikitsidwa ndi kukumbutsidwa za mwayi umene ndili nawo wokhala Mboni ya Yehova.—Onani Aheberi 10:24, 25.

Timothy: Lemba la 1 Akorinto 10:13, limasonyeza kuti Yehova sangalole kuti tikumane ndi zinthu zimene sitingakwanitse kuzipirira. Ndikaganizira mfundo imeneyi ndimadzifunsa kuti, ngati Yehova akuona kuti ndingathe kupirira mayesero amenewa, ineyo ndine ndani kuti nditsutsane naye?

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Hiroki ndi Timothy amayenda pa njinga ya anthu olumala. Ngati inunso muli ndi vuto ngati limeneli, kodi mawu a anyamata awiriwa akulimbikitsani motani?

▪ Danielle ananena kuti “anthu ena sazindikira kuti matenda angawa n’ngoopsa chifukwa choti si matenda oonekera kwa anthu ayi.” Kodi inunso muli ndi matenda enaake ‘osaoneka kwa anthu’? Nanga mungaphunzire chiyani pa mawu amene Danielle ananenawa?

▪ Natalie anati vuto limodzi limene limamusautsa zedi ndi lakuti anthu amamuyang’ana kwambiri. Kodi mungatani kuti munthu ngati Natalie asakhale womangika mukakumana naye? Ngati muli ndi matenda kapena chilema changati cha Natalie, kodi mungatani kuti mutsanzire maganizo ake?

▪ Pamunsipa lembanipo mayina a anthu aliwonse amene mukuwadziwa, omwe akudwala matenda aakulu, kapena omwe ali ndi chilema chinachake.

․․․․․

▪ N’chiyani chimene mungachite kuti muthandize aliyense wa anthuwa?

․․․․․

․․․․․

[Bokosi patsamba 27]

Baibulo Ndi Lolimbikitsa

Yesu amachitira chifundo kwambiri anthu amene ali ndi mavuto enaake m’thupi.—Maliko 1:41.

Mwa “kuchiritsa anthu matenda amtundu uliwonse,” Yesu ankasonyeza zimene zidzachitike mu Ufumu wa Mulungu.—Mateyo 4:23.

M’dziko latsopano, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala,’” ndipo sikudzakhalanso zopweteka.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:1-4.

Ngakhale imfa “idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:25, 26.

[Chithunzi patsamba 26]

Hiroki, wa zaka 23, ku Japan

[Chithunzi patsamba 26]

Natalie, wa zaka 20, ku South Africa

[Chithunzi patsamba 26]

Timothy, wa zaka 20, ku Britain

[Chithunzi patsamba 26]

Danielle, wa zaka 24, ku Australia