MOYO WATHU WACHIKHRISTU | MUKHALE NDI ZOLINGA MU CHAKA CHAUTUMIKI CHIKUBWERACHI
Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi—Upainiya
Timagwiritsa ntchito mphamvu zathu moyenera tikamakhala ndi zolinga zotumikira Yehova. (1Ak 9:26) Dzikoli latsala pang’ono kuwonongedwa, choncho kukhala ndi zolinga kungatithandize kuti tizigwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru. (Aef 5:15, 16) Pa kulambira kwa pabanja mungakambirane zolinga zimene mukufuna muzikwaniritse m’chaka chautumiki chikubwerachi. M’kabuku ka msonkhano kano, muli nkhani zimene zikufotokoza zolinga zosiyanasiyana zimene mungaganizire komanso kuzipempherera.—Yak 1:5.
Mwachitsanzo, kodi mungachite zinthu mogwirizana m’banja mwanu kuti kaya ndi munthu mmodzi ayambe upainiya wokhazikika? Ngati mukukayikira zoti mungakwanitse maola ofunikira, mungalankhule ndi apainiya ena amene zochitika pa moyo wawo n’zofanana ndi zanu. (Miy 15:22) Kapenanso mungacheze ndi mpainiya wina pa kulambira kwanu kwa pabanja. Kenako mungalembe ndandanda zingapo za mmene mungamachitire. Ngati munachitapo upainiya m’mbuyomu, onani ngati panopa mungakwanitsenso kuchita utumikiwu potengera mmene zinthu zilili pa moyo wanu.
Kodi ena m’banja mwanu angachite upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo? Ngati muli ndi thanzi lofooka, n’zotheka kuchita upainiya wothandiza ngati mutamakhala mu utumiki kwa kanthawi kochepa tsiku lililonse. Ngati simukhala ndi nthawi yokwanira yopita mu utumiki mkati mwa wiki chifukwa choti mumagwira ntchito kapena muli pa sukulu, mukhoza kusankha mwezi umene uli ndi holide kapena umene uli ndi masiku 5 a Loweruka ndi Lamlungu. Lembani pa kalendala miyezi imene mukufuna kuchita upainiya wothandiza ndipo konzani ndandanda yake.—Miy 21:5.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU MOLIMBA MTIMA—APAINIYA NDIPO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
-
Kodi zimene zinachitikira Mlongo Aamand zikutiphunzitsa chiyani za mmene Yehova amasamalirira mwachikondi anthu amene amadzipereka kuchita upainiya?