Miyambo 17:1-28

  • Usabwezere zoipa mʼmalo mwa zabwino (13)

  • Mkangano usanabuke, chokapo (14)

  • Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse (17)

  • “Mtima wosangalala uli ngati mankhwala amene amachiritsa” (22)

  • Munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha (27)

17  Ndi bwino kudya mkate wouma pali mtendere,*+Kusiyana ndi kuchita maphwando ochuluka* mʼnyumba imene muli mikangano.+  2  Wantchito wozindikira adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi.Adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.  3  Siliva amamuyengera mʼmbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera mungʼanjo,+Koma Yehova ndi amene amayesa mitima.+  4  Munthu woipa amakonda kumvetsera mawu opweteka.Ndipo munthu wachinyengo amamvetsera lilime loyambitsa mavuto.+  5  Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anamupanga.+Ndipo amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+  6  Zidzukulu zili ngati chisoti chaulemu kwa anthu okalamba,Ndipo ana amalemekezeka chifukwa cha bambo awo.*  7  Sitingayembekezere kuti munthu wopusa alankhule zinthu zanzeru.*+ Ndipo nʼzosayenera kuti wolamulira* azilankhula zabodza.+  8  Mphatso ili ngati mwala wamtengo wapatali kwa mwiniwake.*+Kulikonse kumene wapita, imachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino.+  9  Aliyense amene amakhululuka* zolakwa akufunafuna chikondi,+Koma amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.+ 10  Kudzudzula kumamufika pamtima munthu womvetsa zinthu,+Kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+ 11  Munthu woipa amangofuna kupanduka,Koma munthu wankhanza adzatumidwa kuti akamulange.+ 12  Ndi bwino kukumana ndi chimbalangondo chimene ana ake asowa,Kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru chimene chimachita zopusa.+ 13  Ngati munthu amabwezera zoipa pa zabwino,Zoipa sizidzachoka panyumba yake.+ 14  Kuyambitsa ndewu kuli ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.*Choncho mkangano usanabuke, chokapo.+ 15  Aliyense wonena kuti munthu woipa alibe mlandu ndiponso aliyense wonena kuti munthu wolungama ndi wolakwa,+Onsewa ndi onyansa kwa Yehova. 16  Kodi pali phindu lililonse ngati munthu wopusa ali ndi njira yopezera nzeru,Pamene alibe cholinga chopeza nzeruzo?*+ 17  Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse,+Ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.+ 18  Munthu wopanda nzeru amagwirana dzanja ndi munthu winaNdipo amalonjeza pamaso pa mnzake kuti iye akhala chikole.+ 19  Aliyense amene amakonda mikangano amakonda zolakwa.+ Aliyense woika khomo la nyumba yake pamwamba akudziitanira mavuto.+ 20  Munthu amene mtima wake ndi wopotoka zinthu sizidzamuyendera bwino,*+Ndipo amene amalankhula mwachinyengo adzagwera mʼmavuto. 21  Bambo amene wabereka mwana wopusa adzamva chisoni.Ndipo bambo wa mwana wopanda nzeru sasangalala.+ 22  Mtima wosangalala uli ngati mankhwala amene amachiritsa,+Koma munthu akakhumudwa mphamvu zake zimatha.*+ 23  Munthu woipa amalandira chiphuphu mobisa,Kuti akhotetse chilungamo.+ 24  Munthu wozindikira amakhala ndi cholinga choti apeze nzeru,Koma maso a munthu wopusa amangoyendayenda mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ 25  Mwana wopusa amamvetsa chisoni bambo ake,Komanso amapweteketsa mtima wa* mayi ake amene anamubereka.+ 26  Si bwino kulanga* munthu wolungama,Ndipo kukwapula anthu olemekezeka nʼkosayenera. 27  Munthu wodziwa zinthu amayamba waganiza asanalankhule,+Ndipo munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha.+ 28  Ngakhale munthu wopusa amene wakhala chete adzaonedwa ngati wanzeru,Ndipo amene watseka pakamwa pake adzaonedwa ngati wozindikira.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nsembe zochuluka.”
Kapena kuti, “popanda phokoso.”
Kapena kuti, “makolo awo.”
Kapena kuti, “wolemekezeka.”
Kapena kuti, “mawu abwino.”
Kapena kuti, “Mphatso ndi mwala umene umachititsa kuti mwiniwake akomeredwe mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amaphimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kutsegulira madzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Pamene ali wopanda nzeru?”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzapeza zabwino.”
Kapena kuti, “mafupa ake amauma.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amakwiyitsa.”
Kapena kuti, “kulipiritsa chindapusa.”