Kodi Mulungu Amapezeka Pena Paliponse?
Yankho la m’Baibo
Mulungu amatha kuona zilizonse, komanso amacita zimene afuna kulikonse kumene angasankhe. (Miyambo 15:3; Aheberi 4:13) Komabe, Baibo siphunzitsa kuti Mulungu amapezeka paliponse, kutanthauza kulikonse, m’zinthu zonse. M’malo mwake, imaonetsa kuti iye ni munthu ndipo ali na malo amene amakhala.
Thupi la Mulungu: Mulungu ni munthu wamzimu. (Yohane 4:24) Anthu sangathe kumuona. (Yohane 1:18) Masomphenya a olembedwa m’Baibo amaonetsa kuti Mulungu ali na malo amene amakhala. Siyamaonetsepo zakuti iye amapezeka pena paliponse.—Yesaya 6:1, 2; Chivumbulutso 4:2, 3, 8.
Malo kumene Mulungu amakhala: Mulungu amakhala ku malo a mizimu, malo osiyana kwambili na cilengedwe conse. Kumalo kumeneko Mulungu alinso na ‘malo ake okhala kumwamba.’ (1 Mafumu 8:30) Baibo imakamba za nthawi pamene zolengedwa zauzimu zinapita “kukaonekela pamaso pa Yehova.” * Izi zionetsa kuti Mulungu ali na malo ake-ake kumene iye amakhala.—Yobu 1:6.
Ngati Mulungu sapezeka pena paliponse, kodi iye amasamala za ine panekha?
Inde. Mulungu amasamala kwambili za munthu aliyense. Ngakhale kuti amakhala ku malo a zolengedwa zamzimu, Iye amasamala za anthu amene ali padziko lapansi amene amafunitsitsa kum’kondweletsa, ndipo amawathandiza. (1 Mafumu 8:39; 2 Mbiri 16:9) Onani mmene Yehova amaonetsela kuti amasamala za alambili ake oona mtima:
Mukamapemphela: Yehova amamvela pemphelo lanu nthawi yomweyo.—2 Mbiri 18:31.
Mukakhala na nkhawa: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.
Mukafuna citsogozo: Yehova ‘adzakupatsani nzelu ndi kukulangizani’ kupitila m’Mawu ake Baibo.—Salimo 32:8.
Maganizo olakwika pankhani yakuti Mulungu ali pena paliponse
Maganizo olakwika: Mulungu ali paliponse m’cilengedwe conse.
Mfundo yazoona: Mulungu sakhala padziko lapansi, kapena m’cilengedwe cimene timaona. (1 Mafumu 8:27) N’zoona kuti nyenyezi komanso zinthu zokongola zimene anapanga ‘zimalengeza ulemelelo wa Mulungu.’ (Salimo 19:1) Munthu amene wajambula cithunzi cina cake, sakhala m’cithunzi cimene wajambulaco. Komabe, cithunzico cimatiuza zina zake zokhudza wojambulayo. Mofananamo, Mulungu nayenso sakhala m’zinthu zimene analenga. Ngakhale n’telo, cilengedwe cimatiuza ‘makhalidwe osaoneka’ a Mlengi wathu monga mphamvu zake, nzelu komanso cikondi.—Aroma 1:20.
Maganizo olakwika: Kuti Mulungu azidziŵa zinthu zonse komanso kuti akhale wamphamvu zonse, iye afunika kukhala paliponse.
Mfundo yazoona: Mzimu woyela wa Mulungu, ni mphamvu imene Mulungu amaitumiza kuti ikagwile nchito. Mwa kuseŵenzetsa mzimu wake woyela, Mulungu angacite ciliconse, kulikonse, nthawi iliyonse, popanda iye mwini kupitako kumeneko.—Salimo 139:7.
Maganizo olakwika: Salimo 139:8 imaonetsa kuti Mulungu amakhala paliponse. Imati: “Ngati ndingakwele kumwamba, inu mudzakhala komweko. Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.”
Mfundo yazoona: Lemba limeneli silikamba za ku malo kumene Mulungu amakhala. Koma ikutiphunzitsa mwandakatulo kuti kulibe malo amene ali kutali kwa Mulungu cakuti n’kulephela kutithandiza.
^ ndime 3 Baibo imakamba kuti dzina la Mulungu ni Yehova.