Cikumbutso ca Imfa ya Yesu

Mande, March 22, 2027

Caka ciliconse, a Mboni za Yehova amacita mwambo wokumbukila imfa ya Yesu kamodzi pa caka mogwilizana ndi zimene Yesu ananena kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—Luka 22:19.

Tikuitanilani inu ndi a m’banja lanu kuti mukapezekepo pa cocitika capadela cimeneci.

Mafunso Amene Anthu Ambili Amafunsa

Kodi ndani ayenela kupezekapo?

Aliyense ndi wolandilidwa, conco mungabwele ndi anzanu komanso a m’banja lanu.

Kodi pulogilamu imeneyi idzatenga utali wotani?

Pulogilamu imeneyi idzatenga pafupifupi ola limodzi.

Kodi pulogilamuyi idzacitikila kuti?

Funsani kwa a Mboni za Yehova a kwanuko.

Kodi nikapezekapo nidzafunika kulipila ndalama kapena kubvomela kupezeka pamisonkhano ina?

Ai.

Kodi padzakhala kuyendetsa mbale ya zopeleka?

Ai. Pa misonkhano ya Mboni za Yehova sipakhala kupititsamo mbale ya zopeleka.—Mateyo 10:8.

Kodi pali mtundu wa zovala zofunikila?

Ai. Ngakhale n’conco, a Mboni za Yehova amayesetsa kubvala mwaulemu komanso moonetsa kuti akulemekeza cocitikaco.

Kodi n’ciani cimene cidzacitika ku Cikumbutso?

Kudzakambidwa nkhani yolimbikitsa imene idzafotokoza kufunika kwa imfa ya Yesu komanso mapindu amene timapeza cifukwa ca zimene Mulungu ndi Yesu anaticitila. Msonkhanowu udzayamba komanso kutha ndi nyimbo.

Kodi Cikumbutso cotsatila cidzacitika liti?

2027: Mande, March 22

2028: Cisanu, April 9

2029: Cinai, March 29