Onani zimene zilipo

Kodi Baibo Linganithandize Ngati Nili na Maganizo Ofuna Kudzipha?

Kodi Baibo Linganithandize Ngati Nili na Maganizo Ofuna Kudzipha?

Yankho la m’Baibo

 Inde. Baibo inacokela kwa “Mulungu, amene amalimbikitsa osautsika mtima.” (2 Akorinto 7:6) Olo kuti si buku lothandiza anthu ovutika maganizo, Baibo lathandiza anthu ambili amene anali na maganizo ofuna kudzipha. Malangizo ake inunso angakuthandizeni.

 Kodi Baibo imapeleka malangizo otani pa nkhaniyi?

  • Uzankoni ena mmene mumvelela.

     Zimene Baibo imakamba: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

     Mfundo yake: Tonsefe timafuna kuti anthu ena atithandize tikapsinjika maganizo.

     Kusauzako anzanu mmene mumvela, kuli monga mwanyamula cimwala colema cimene simukufuna kucitula pansi. Koma mukawafotokozela, zimakhala ngati mwacitula, ndipo zinthu zimayamba kukuyendelani bwino.

     Yesani kucita izi: Fotokozani mmene mumvela kwa munthu wina lelo, mwina wa m’banja lanu kapena mnzanu amene mumadalila. * Kapenanso mungalembe papepala mmene mumvelela.

  • Kaonaneni na dokotala.

     Zimene Baibo imakamba: “Anthu abwino-bwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.

     Mfundo yake: Tikadwala, tiziyesetsa kupeza thandizo la kucipatala.

     Ngati munthu afuna kudzipha, cingakhale cizindikilo ca matenda ovutika maganizo. Conco, musacite manyazi kuonana na dokotala monga mmene mumacitila mukadwala matenda ena alionse. Ndipo n’zotheka kucila matenda ovutika maganizo.

     Yesani kucita izi: Mwamsanga kaonaneni na dokotala wodziŵa nchito kuti akuthandizeni.

  • Muzikumbukila kuti Mulungu amasamala za inu.

     Zimene Baibo imakamba: “Mpheta zisanu amazigulitsa makobidi aŵili ocepa mphamvu, si conco kodi? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imene imaiŵalika kwa Mulungu. . . . Musacite mantha. Ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili.”—Luka 12:6, 7.

     Mfundo yake: Ndinu amtengo wapatali kwa Mulungu.

     Mungaone monga palibe amene amakuganizilani, koma Mulungu adziŵa mavuto onse amene mukumana nawo. Iye amakukondani ngakhale pamene mwayamba kuganiza kuti simukufunanso kukhala na moyo. Salimo 51:17 imati: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.” Inde, Mulungu amafuna kuti mukhalebe na moyo cifukwa amakukondani.

     Yesani kucita izi: Fufuzani m’Baibo kuti muone umboni wakuti Mulungu amakukondani. Mwacitsanzo, ŵelengani mutu 24 m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova.

  • Muzipemphela kwa Mulungu.

     Zimene Baibo imakamba: ‘Mutulileni [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

     Mfundo yake: Mulungu akukupemphani kuti muzimasuka kumuuza ciliconse cimene cikukudetsani nkhawa.

     Mulungu adzakupatsani mtendele wa mumtima komanso mphamvu kuti muthe kupilila mavuto amene mukumana nawo. (Afilipi 4:6, 7, 13) Mwa njila imeneyi, Mulungu amathandiza anthu amene amapempha thandizo lake.—Salimo 55:22.

     Yesani kucita izi: Pemphelani kwa Mulungu lelo. Museŵenzetse dzina lake lakuti Yehova, ndipo muuzeni mmene mumvelela. (Salimo 83:18) M’pempheni kuti akuthandizeni kupilila.

  • Muziganizila zinthu zabwino zimene Baibo inatilonjeza.

     Zimene Baibo imakamba: “Ciyembekezo cimene tili nacoci cili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.”—Aheberi 6:19.

     Mfundo yake: Maganizo athu akhoza kusokonezeka monga mmene imacitila sitima imene yakumana na cimphepo pamadzi. Koma zabwino zimene Baibo inatilonjeza zingathandize kuti maganizowo akhale m’malo.

     Zimene tikuyembekezela si maloto ayi, koma n’zimene Mulungu analonjeza kuti adzacotsapo zopweteka.—Chivumbulutso 21:4.

     Yesani kucita izi: Dziŵani zambili zokhudza malonjezo a m’Baibo mwa kuŵelenga phunzilo 5 m’bulosha yakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu.

  • Muzicita zinthu zimene zimakusangalatsani.

     Zimene Baibo imakamba: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa.”—Miyambo 17:22.

     Mfundo yake: Tikamacita zinthu zimene timakonda, timacepetsako kukhala ovutika maganizo kapena ankhawa..

     Yesani kucita izi: Citani zinthu zimene zimakuthandizani kumva bwino. Mwacitsanzo, mvetselani nyimbo zabwino, ŵelengani nkhani inayake yolimbikitsa, kapena citani maseŵelo ena ake amene amakusangalatsani. Mungakhalenso osangalala mukamathandiza ena, olo pa zinthu zing’ono-zing’ono.—Machitidwe 20:35.

  • Muzisamalila thanzi lanu.

     Zimene Baibo imakamba: “Kucita maseŵela olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”—1 Timoteyo 4:8.

     Mfundo yake: Timapindula tikamacita maseŵela olimbitsa thupi, kugona mokwanila, komanso kudya cakudya copatsa thanzi.

     Yesani kucita izi: Pangani kaulendo kakuti muwongoleko miyendo, mwina kwa 15 mphindi cabe.

  • Kumbukilani kuti zinthu zimatha kusintha mu umoyo.

     Zimene Baibo imakamba: “Simukudziŵa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—Yakobo 4:14.

     Mfundo yake: Vuto lothetsa nzelu, ngakhale lioneke monga simungathe kulithetsa, likhoza kukhala la kanthawi cabe.

     Ngakhale zinthu zifike pothina motani, dziŵani kuti nthawi ina zidzakhala bwino. Conco, pezani njila imene ingakuthandizeni kupilila. (2 Akorinto 4:8) M’kupita kwa nthawi, zinthu zimatha kukhalanso m’malo mwake. Koma mukadzipha, basi inuyo mwafa.

     Yesani kucita izi: Ŵelengani nkhani za m’Baibo za anthu amene analefuka mpaka kuyamba kuganiza zakuti afe cabe. Ndipo onani mmene zinthu zinasinthila pa moyo wawo n’kuyamba kuyenda bwino, ngakhale kuti sanali kuyembekezela kuti zinthu zingasinthe. Ganizilani zitsanzo izi:.

 Kodi Baibo imachula anthu amene anali kulakalaka kufa?

 Inde. Baibo imafotokoza za anthu ena amene anali na maganizo ofuna kufa. Mulungu sanawadzudzule, koma anawathandiza. Ndipo angacitenso cimodzimodzi kwa imwe.

Eliya

  •  Kodi iye anali ndani? Eliya anali mneneli wolimba mtima. Koma nthawi ina nayenso analefuka. Yakobo 5:17 imakamba kuti: “Eliya anali munthu monga ife tomwe.”

  •  N’cifukwa ciyani anali kufuna kuti afe? Pa nthawi ina, Eliya anaona kuti watsala yekha-yekha, anali na nkhawa, ndiponso anadziona kuti ni wosafunika. Ndiye cifukwa cake anapemphela kuti: “Cotsani moyo wanga Yehova.”—1 Mafumu 19:4.

  •  N’ciyani cinam’thandiza? Eliya anafotokozela Mulungu mmene anali kumvela. Nanga Mulungu anamulimbikitsa bwanji? Mulungu anamuonetsa kuti amasamala za iye, ndipo anaonetsa Eliya zinthu zoonetsa kuti Iye ndi wamphamvu. Cina, anamutsimikizila kuti akali munthu wofunika ngako, ndipo anamupatsa munthu wabwino komanso wacikondi kuti azimuthandiza.

  •  Ŵelengani nkhani ya Eliya: 1 Mafumu 19:2-18.

Yobu

  •  Kodi iye anali ndani? Anali munthu wolemela, ndipo anali na banja lalikulu. Iye anali kutumikila Mulungu woona mokhulupilika.

  •  N’cifukwa ciyani anali kufuna kuti afe? Mwadzidzidzi, Yobu anakumana na mavuto ambili motsatizana. Anataikilidwa kKatundu wake wonse. Ana ake onse anafa nyumba itawagwela. Iyeyo anadwala matenda opweteka kwambili. Ndipo pamapeto pake, anzake anamuimba mlandu wabodza wakuti mavuto amene akukumana nawo anacita kudzibweletsela yekhawo anacita kuwaputa dala. Yobu anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kale-kale.”—Yobu 7:16.

  •  N’ciyani cinamuthandiza kuwongolela maganizo ake? Yobu anapemphela kwa Mulungu. Komanso, anauzako anthu ena mavuto akewo. (Yobu 10:1-3) Analimbikitsidwa na mnzake wina wacikondi dzina lake Elihu. Iye anam’thandiza kuona mavuto ake moyenela. Koma coposa zonse, Yobu anamvela malangizo a Mulungu, na kulandila thandizo lake.

  •  Ŵelengani nkhani ya Yobu: Yobu 1:1-3, 13-22; 2:7; 3:1-13; 36:1-7; 38:1-3; 42:1, 2, 10-13.

Mose

  •  Kodi iye anali ndani? Mose anali mtsogoleli wa Aisiraeli, ndiponso mneneli wokhulupilika.

  •  N’cifukwa ciyani anali kufuna kuti afe? Mose anali kupanikizika cifukwa ca udindo waukulu. Cina, anthu anali kungomunyoza, mpaka anafika polema nazo. Ndiye cifukwa cake, anadandaulila Mulungu kuti: “Ingondiphani.”—Numeri 11:11, 15.

  •  N’ciyani cinam’thandiza? Mose anauza Mulungu mmene anali kumvelela. Ndipo Mulungu anamuthandiza pomucepetsela nchito yake kuti asamapanikizike.

  •  Ŵelengani nkhani ya Mose: Numeri 11:4-6, 10-17.

^ ndime 5 Mukaona kuti maganizo ofuna kudzipha akukulabe ndipo palibe aliyense amene angakuthandizeni, tumilani foni anthu amene anaphunzitsidwa nchito yothandiza anthu ovutika maganizo ngati alipo m’dela lanu.