Onani zimene zilipo

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Miyambo 17:17—“Bwenzi Lenileni Limakukonda Nthawi Zonse”

Miyambo 17:17—“Bwenzi Lenileni Limakukonda Nthawi Zonse”

“Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Bwenzi limakonda nthawi zonse; Ndipo mbale anabadwila kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Miyambo 17:17

 Anzathu enieni amakhala odalilika. Mofanana ndi anthu a m’banja limodzi, iwo amakhala okhulupilika ndi acikondi, makamaka pa nthawi zovuta.

 “Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse.” Mawu amenewa angamasulilidwenso kuti “mabwenzi amaonetsa cikondi nthawi zonse.” Mawu a Ciheberi amene palembali anawamasulila kuti “cikondi” amaphatikizapo zambili kuposa cabe mmene munthu akumvela mumtima. Ndi cikondi copanda dyela cimene munthu amaonetsa m’zocita zake. (1 Akorinto 13:4-7) Mabwenzi amene amakondana mwanjila imeneyi amakhalabe ogwilizana ngakhale asemphane maganizo kapena kukumana ndi mavuto ena. Amakhululukilananso ndi mtima wonse. (Miyambo 10:12) Ndipo sacitilana nsanje wina zikamuyendela bwino. M’malomwake, amasangalala naye mnzakeyo.—Aroma 12:15.

 “Mnzako weniweni . . . ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.” Mwambi umenewu unacokela pa mfundo yakuti anthu a m’banja limodzi amagwilizana kwambili. Conco tikamacita zonse zimene tingathe kuti tithandize mnzathu amene akukumana ndi mavuto, timacita zinthu ngati mmene m’bale ndi mlongo wake weniweni akanacitila. Komanso cikondi cimene cimagwilizanitsa mabwenzi otelo sicicepa ngakhale akumane ndi mavuto otani. M’malomwake cimakula cifukwa akakumana ndi mavuto, amakondana komanso kulemekezana.

Nkhani yonse ya pa Miyambo 17:17

 M’buku la Miyambo muli nzelu zothandiza zimene zinalembedwa ngati mawu afupiafupi amene amapangitsa wowelenga kuganiza. Mfumu Solomo ndi amene analemba mbali yaikulu ya buku la m’Baibulo limeneli. Iye analemba bukuli motsatila kalembedwe ka ndakatulo za Ciheberi, m’malo molemba mawu omveka ofanana, iye analemba ziganizo zofanana kapena zotsutsana pofuna kumveketsa bwino mfundo ya ciganizo ca pambuyo. Miyambo 17:17 ndi citsanzo ca ndakatulo ya ziganizo zofanana. Mbali yaciwili ya vesili imveketsa bwino mfundo ya mbali yoyamba. Miyambo 18:24 ndi citsanzo ca ndakatulo ya ziganizo zotsutsana. Lembali limati: “Pali anthu ogwilizana amene ndi okonzeka kucitilana zoipa, koma pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”

 Polemba Miyambo 17:17, Solomo ayenela kuti anali kuganizila ubwenzi wolimba umene unali pakati pa atate wake, Davide, ndi Yonatani mwana wa Mfumu Sauli. (1 Samueli 13:16; 18:1; 19:1-3; 20:30-34, 41, 42; 23:16-18) Ngakhale kuti Davide ndi Yonatani sanali a m’banja limodzi, iwo anali kugwilizana kwambili kuposa anthu a m’banja limodzi. Yonatani anali wokonzeka ngakhale kufa kuti ateteze mnzake wacinyamatayu. a

Mmene Mabaibulo Ena Anamasulilila Miyambo 17:17

 “Mnzako amakukonda nthawi zonse, ndipo amakhala m’bale pa nthawi ya mavuto.”—The Bible in Basic English.

 “Mnzako amakhalabe mnzako nthawi zonse, iye ndi m’bale amene anabadwa kuti akuthandize pa mavuto.”—The Moffatt Translation of the Bible.

 “Mnzako amaonetsa kuti ndi mnzako nthawi zonse—m’bale [woteleyu] anabadwila kuti akuthandize pa mavuto.”—The Complete Jewish Study Bible.

 Onelelani vidiyo yaifupi iyi imene ifotokoza mfundo za m’buku la Miyambo.

a Onani nkhani yakuti “Anagwirizana Kwambiri.”