Kodi a Mboni za Yehova Amaphunzitsidwa Bwanji Mmene Angacitile Utumiki Wawo?
Nthawi zonse, a Mboni za Yehova amalandila maphunzilo amene amawathandiza pa mbali zonse za umoyo wawo wacikhristu, kuphatikizapo pa utumiki wawo. Utumiki umenewu ndi nchito imene Yesu analamula otsatila ake kuti azicita. Nchitoyi ndi yolalikila ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Timalandila maphunzilo amenewa pa misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu, komanso pa misonkhano yacigawo ndi yadela ya caka ndi caka. A Mboni amene ali ndi maudindo mumpingo kapena m’gulu, amalandila maphunzilo owonjezela ku masukulu apadela ophunzitsa Baibulo.
Zimene zili m’nkhani ino:
Kodi a Mboni za Yehova amalandila maphunzilo otani?
Misonkhano ya mpingo. Mlungu uliwonse, timakhala ndi misonkhano iwili ku malo athu olambilila, ochedwa Nyumba za Ufumu. Msonkhano wina umacitika mkati mwa mlungu ndipo wina umacitika kumapeto kwa mlungu. Aliyense ndi wolandilidwa ku misonkhanoyi ndipo sikukhala kuyendetsa mbale ya zopeleka.
Msonkhano wa mkati mwa mlungu. Timaphunzila mmene tingakulitsile luso lathu la kuwelenga, lokambilana ndi anthu, lokamba pa gulu, komanso kulalikila ndi kuphunzitsa. Timalandila maphunzilowa kudzela mu nkhani, makambilano, zitsanzo komanso kuonelela mavidiyo. Maphunzilowa amatithandiza kukhala aluso pamene tikulalikila uthenga wa m’Baibulo kwa anthu ena komanso pamene tikutsogoza maphunzilo a Baibulo ndi anthu acidwi. Onse amene amapezeka pamisonkhanoyi amapindula ndi maphunzilo amenewa. Koposa zonse misonkhano yathu imalimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu komanso cikondi cathu pa iye ndi okhulupilila anzathu.
Msonkhano wa kumapeto kwa mlungu. Gawo loyamba la msonkhano wa kumapeto kwa mlungu, limakhala nkhani ya m’Baibulo imene amaikonzela anthu omwe si Mboni. Gawo laciwili la msonkhanowu limakhala makambilano a mafunso ndi mayankho pa nkhani ya m’magazini yophunzila ya Nsanja ya Mlonda. a Nkhani zophunzila zimenezi, zimafotokoza nkhani ndi mfundo za m’Baibulo zimene zimatithandiza pa utumiki wathu ndi pa umoyo wathu.
Misonkhano yadela ndi yacigawo. Caka ciliconse timakhala ndi misonkhano itatu ikuluikulu. Pa misonkhanoyi pamakhala anthu ocokela m’mipingo yambili. Zocitika zosangalatsa zimenezi zimakhala ndi mitu yocokela m’Malemba ndipo pamakhala nkhani, zitsanzo, mbali zofunsa mafunso, komanso kuonelela mavidiyo. Mofanana ndi misonkhano ya mpingo, nayonso misonkhano yadela ndi yacigawo imatithandiza kukulitsa cidziwitso cathu ca Baibulo, komanso kukhala alaliki aluso a uthenga wabwino. Monga zilili ndi misonkhano ya mpingo, aliyense ndi wolandilidwa pa misonkhanoyi ndipo sipakhala kupititsamo mbale ya zopeleka.
Masukulu ophunzitsa Baibulo a Mboni za Yehova
Kuti alandile maphunzilo owonjezela, a Mboni za Yehova ena amaitanidwa ku masukulu osiyanasiyana ophunzitsa Baibulo. Kodi masukuluwa ndi otani? Nanga colinga ca masukuluwa n’ciyani? Amakhala utali wotani? Ndipo ndani ali woyenelela kulowa?
Sukulu ya Utumiki ya Apainiya
Colinga: Kuphunzitsa atumiki anthawi zonse amene amachedwa kuti apainiya, b kukulitsa luso lawo mu utumiki komanso pa nchito yophunzitsa. Pa sukuluyi pamakhala zokambilana, zitsanzo komanso zocita m’magulu.
Nthawi: Masiku 6.
Oyenela Kulowa: Amene acita upainiya kwa caka cimodzi kapena kuposelapo amaitanidwa kukalowa sukuluyi. Apainiya ena amene atumikila kwa nthawi yaitali, ndipo papita zaka zisanu kucokela pamene analowa sukuluyi angaitanidwe kuti alowenso.
Sukulu ya Alengezi a Ufumu
Colinga: Kupeleka maphunzilo apadela kwa atumiki anthawi zonse amene atumikila kwa nthawi yaitali. Ophunzila amaphunzitsidwanso mmene angakulitsile maluso awo polalikila ndi pophunzitsa, ndipo amaphunzila nkhani za m’Baibulo mozamilapo. Ambili amene amaliza maphunzilowa amatumizidwa kumalo kumene kukufunika alaliki ambili.
Nthawi: Miyezi iwili.
Oyenela Kulowa: Apainiya angafunsile kulowa sukuluyi ngati akwanilitsa ziyenelezo zina zake ndiponso ngati angakwanitse kutumikila kumene kukufunikila anchito ambili.
Sukulu ya Akulu
Colinga: Kuthandiza akulu c kuti azigwila bwino nchito yawo mumpingo, monga kuphunzitsa ndi kusamalila anthu mumpingo. Imawathandizanso kuti azikonda kwambili Mulungu ndi okhulupilila anzawo.—1 Petulo 5:2, 3.
Nthawi: Masiku asanu.
Oyenela Kulowa: Anthu amene angoikidwa kumene kukhala akulu ndiponso aja amene akhala akulu kwa zaka zambili koma sanalowepo sukuluyi m’zaka 5, amaitanidwa kuti alowe.
Sukulu ya Oyang’anila Madela ndi Akazi Awo
Colinga: Kuthandiza atumiki oyendela, ochedwa oyang’anila madela, d kuti azigwila bwino nchito zawo. (1 Timoteyo 5:17) Maphunzilowa amathandizanso akulu amenewa ndi akazi awo kuti akhale ndi cidziwitso cozama ca m’Malemba.
Nthawi: Mwezi umodzi.
Oyenela Kulowa: Oyang’anila madela atsopano ndi akazi awo amaitanidwa kusukuluyi pambuyo pocita utumiki wawo kwa caka cimodzi. Akalowa koyamba, amaitanidwanso pambuyo pa zaka 5 zilizonse.
Sukulu ya Utumiki wa Ufumu
Colinga: Kuthandiza akulu ndi atumiki othandiza e kusamalila maudindo awo mumpingo malinga ndi mmene zinthu zilili panthawiyo, mmene zinthu zikusinthila m’dzikoli, ndi zimene anthu mu mpingo akufunikila. (2 Timoteyo 3:1) Sukuluyi imacitika pakapita zaka zingapo.
Nthawi: Imacitika kwa nthawi ya utali wosiyanasiyana, nthawi zambili imakhala tsiku limodzi.
Oyenela Kulowa: Oyang’anila madela, akulu, komanso atumiki othandiza.
Sukulu ya Utumiki wa pa Beteli
Colinga: Kuthandiza atumiki a pa Beteli f kuti acite bwino nchito yawo ndiponso kuti akulitse cikondi cawo kwa Mulungu ndi kwa anzawo.
Nthawi: Masiku 5 ndi hafu.
Oyenela Kulowa: Anthu amene angoyamba kumene kutumikila pa Beteli ayenela kulowa sukuluyi. Atumiki a pa Beteli amene sanalowepo sukuluyi m’zaka 5 angaitanidwe kuti alowe sukuluyi.
Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo
Colinga: Kuthandiza ophunzila kukonda kwambili Baibulo komanso kulimvetsetsa mwakuya, ndi kuwathandiza kugwilitsa nchito zimene aphunzila. (1 Atesalonika 2:13) Amuna ndi akazi okhwima mwauzimu amene amalowa Sukulu ya Giliyadi amenewa, amakhala othandiza kwambili m’gulu la Yehova ndiponso pogwila nchito yophunzitsa Baibulo padziko lonse. Omaliza maphunzilowa angaikidwe kukhala amishonale kapena angatumidwe kukatumikila pa ofesi ya nthambi m’dziko lawo kapena m’dziko lina.
Nthawi: Miyezi 5.
Oyenela Kulowa: Maofesi a nthambi amapempha anthu ena amene ali mu utumiki wanthawi zonse kuti afunsile kulowa sukuluyi. Sukuluyi imacitikila ku America ku likulu la maphunzilo la Watchtower mu mzinda wa Patterson, ku New York.
Sukulu ya a m’Komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo
Colinga: Kuphunzitsa a m’Komiti ya Nthambi g kuti aziyang’anila nchito za pa ofesi ya nthambi komanso nchito za Mboni za Yehova m’dziko lawo kapena m’maiko amene ofesi yawo ya nthambi imayang’anila.
Nthawi: Miyezi iwili.
Oyenela Kulowa: A ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova amasankha ena a mu makomiti a nthambi ndi akazi awo kuti alowe sukulu imeneyi. Sukuluyi imacitikila ku likulu la maphunzilo la Watchtower mu mzinda wa Patterson, ku New York.
Kodi maphunzilo amene a Mboni amalandila amacokela kuti?
Maphunzilo onse amene a Mboni za Yehova amalandila amacokela m’Baibulo. Timakhulupilila kuti Baibulo linauzilidwa ndi Mulungu ndipo lili ndi malangizo abwino kwambili othandiza pambali zonse za umoyo wacikhristu.—2 Timoteyo 3:16, 17.
Kodi a Mboni za Yehova amafunika kulipila kuti alandile maphunzilo amenewa?
Ayi. Maphunzilo amenewa ndi aulele. Ndalama zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwawo ndi zimene zimathandiza poyendetsa nchito ya Mboni za Yehova.—2 Akorinto 9:7.
a Baibulo ndi mabuku athu othandiza pophunzila Baibulo, kuphatikizapo mavidiyo, zimapezeka pa webusaiti yathu ya jw.org.
b Mpainiya ndi wa Mboni wobatizidwa komanso wacitsanzo cabwino, angakhale mwamuna kapena mkazi, amene amadzipeleka kuti azilalikila uthenga wabwino kwa maola ena ake mwezi uliwonse.
c Akulu ndi amuna amene ndi Akhristu okhwima omwe amaphunzitsa kucokela m’Malemba ndi kuweta anthu a Yehova mwa kuwathandiza ndi kuwalimbikitsa. Iwo salandila malipilo alionse.
d Woyang’anila dela ndi mtumiki wanthawi zonse amene amayendela mipingo yosiyanasiyana m’dela lake mlungu uliwonse. Amalimbikitsa anthu a mumpingo mwa kukamba nkhani za m’Baibulo ndi kupita nawo kukalalikila.
e Atumiki othandiza amagwila nchito zolekanalekana potumikila anthu mumpingo. Izi zimapatsa akulu nthawi yokwanila yosamalila maudindo a kuphunzitsa komanso ubusa.
f Beteli ndi dzina lomwe linapelekedwa ku maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Atumiki a nthawi zonse amene amatumikila pa Beteli amagwila nchito imene imathandiza Mboni za Yehova m’gawo la nthambi yawo.
g Amuna atatu kapena oposelapo oyenelela ndi amene amatumikila m’Komiti ya Nthambi.