Ndili M’manja Mwanu
Citani daunilodi:
1. Yehova M’lungu mumaona
Za mumtima wanga wocimwa
Pamene n’kutumikilani.
Ningalankhule mawu oipa
Kapena kucita zoipa,
Nipempha, “Nithandizileni.”
(MWANA WA KOLASI)
Ndinu Atate wanga
Ndipo ine ndinetu dongo.
(KOLASI)
Munganiumbe kukhala
Munthu wabwino zedi,
Yemwe inu mungamukonde.
Umbeni mwacikondi
Nikhale bwenzi lanu.
Atate nipempha!
Umbeni ine.
Umbeni ine.
2. Nikamawelenga mawu anu
Ndi kucita zomwe mufuna,
Mumtima nimamvela bwino.
Nipatseni mtima womvela
Kuti nizicita zoyenela.
Zolakwa zisanilefule.
(MWANA WA KOLASI)
Ndinu Atate wanga
Ndipo ine ndinetu dongo
(KOLASI)
Munganiumbe kukhala
Munthu wabwino zedi,
Yemwe inu mungamukonde.
Umbeni mwacikondi
Nikhale bwenzi lanu.
Atate nipempha!
Umbeni ine.
Umbeni ine.
(KUMALIZA)
Conde n’thadizeni
Nikhale womvela.
Atate nipempha!
Umbeni ine,
Umbeni ine.