NYIMBO 104
Mphatso ya Mzimu Woyela
-
1. Mfumu, Yehova, Atate wathu,
Ndinu Mulungu wacifundo.
Tithandizeni, titonthozeni,
Kuti tilimbane na mavuto.
-
2. Inu mudziŵa ndise ocimwa;
Nthawi zina timasocela.
Conde mvelani pemphelo lathu.
Titetezeni na mzimu wanu.
-
3. Tikavutika, tikakhumudwa
Mzimu wanu uticengete.
M’lungu tipempha, tilimbitseni,
Tipitilize kucilimika.
(Onaninso Sal. 51:11; Yoh. 14:26; Mac. 9:31)