Nyimbo 66
Tizitumikira Yehova ndi Moyo Wathu Wonse
1. Yehova Wamphamvuyonse
Inetu ndimakukondani.
Mtima wanga wonse umafuna
Kukutumikirani.
Malamulo anu ndimvera
Zofuna zanu ndichita.
(KOLASI)
Inu Yehova ndinu woyenera
Kutumikiridwa.
2. Atate, zomwe munalenga
Zimakulemekezani.
Ndadzipereka ndi mphamvu
Zonse kukutumikirani.
Zonse ndinakulonjezani
Ndidzayesetsa kuchita.
(KOLASI)
Inu Yehova ndinu woyenera
Kutumikiridwa.
(Onaninso Deut. 6:15; Sal. 40:8; 113:1-3; Mlal. 5:4; Yoh. 4:34.)