Nyimbo 81
“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
1. Yehova nthawi zonse timachimwa
Chifukwa cha kupanda ungwiro.
Pali tchimo lomwe limatikola,
Kusowa kwa chikhulupiriro.
(KOLASI)
M’tiwonjezere chikhulupiriro.
Muzofo’ka zathu m’tithandize.
M’tiwonjezere mwachifundo chanu,
Tikulemekezeni mu zonse.
2. N’zosatheka kukukondweretsani
Ngati sitimakhulupirira.
Chikhulupiriro n’chotiteteza
Ndipo chimatilimbitsa mtima.
(KOLASI)
M’tiwonjezere chikhulupiriro.
Muzofo’ka zathu m’tithandize.
M’tiwonjezere mwachifundo chanu,
Tikulemekezeni mu zonse.
(Onaninso Gen. 8:21; Aheb. 11:6; 12:1.)