Nyimbo 52
Tetezani Mtima Wanu
(Miyambo 4:23)
1. Tetezani mtima wanu
Mukhale ndi moyo.
Mulungu adziwa bwino
Mmene tililidi.
Mtima ndi wonyenga
ungakusocheretseni.
Choncho ganizani bwino,
Mverani Yehova.
2. Konzanitu mtima wanu
Ufune Yehova
Pempherani muuzeni
Za kukhosi kwanu.
Zomwe M’lungu aphunzitsa
Tiyeni timvere,
Choncho tidzamutamanda
Tsiku lililonse.
3. Tetezani mtima wanu
Mupewe zoipa.
Akufikeni pa mtima.
Mawu a Mulungu
Yehova akonda onse
Okhulupirika.
Choncho mulambirenitu
Monga bwenzi lake.
(Onaninso Sal. 34:1; Afil. 4:8; 1 Pet. 3:4.)