Nyimbo 120
Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso
1. Kodi ndife anthu omvera Khristu
Pa zonse zimene ananena?
Kuzidziwa n’kosangalatsa ndithu.
Tidalitsidwa tikazimvera.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze
Mvera udalitsidwe.
2. Monga nyumba yomangidwa pathanthwe
Osati yomangidwa pamchenga,
Zochita zathu zingatiteteze
Kokha ngati Yesu timumvera.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze
Mvera udalitsidwe.
3. Monga mtengo wamumbali mwa madzi
Umabereka nthawi ’kafika,
Tikamvera tidzadalitsidwadi
Moyo wosatha tidzalandira.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze
Mvera udalitsidwe.
(Onaninso Deut. 28:2; Sal. 1:3; Miy. 10:22; Mat. 7:24-27.)