Nyimbo 96
Fufuzani Anthu Oyenerera
1. Ambuye wathu anatisonyeza
Njira yolalikirira:
‘Kulikonse kumene mungapite
Fufuzani oyenerera.
Muziwapatsa moni eni nyumba
Ndikuwafunira mtendere.
Ngati akana sansani fumbi
Kumapazi anu muwasiye.’
2. Onse amene akulandirani
Alandiranso Ambuye.
Mulungu adzawathandizadi
Kuti nawonso atumikire.
Musade nkhawa kuti munenanji,
Yehova adzakuuzani.
Ngati mutayankha mokoma mtima
Ofatsa adzakumverani.
(Onaninso Mac. 13:48; 16:14; Akol. 4:6.)