Nyimbo 119
Bwerani Mudzatsitsimulidwe!
(Aheberi 10:24, 25)
1. Tikukhaladi m’dziko losochera,
Anthu sakudziwa M’lungu.
Tikufunikiradi malangizo
Osonyeza njira yathu.
Misonkhano yathu imathandiza
Kukhala n’chiyembekezo,
Imatilimbikitsa n’kutipatsa
Mphamvu yochita zabwino.
Zimene Yehova watilamula
Ife sitidzazisiya.
Pamisonkhano yathu timapeza
Malangizo oyenera.
2. Yehova akudziwa bwino zinthu
Zomwe timafunikira.
Tikamasonkhana timasonyeza
Kuti timamudalira.
Tikamamvera nkhani za abale
Timalimbikitsidwadi.
Timadziwa kuti sitili tokha,
Iwo atithandizadi.
Poyembekezera Paradaiso
Sitisiya kusonkhana.
Tiziphunzira kugwiritsa ntchito
Nzeru yochoka kumwamba.
(Onaninso Sal. 37:18; 140:1; Miy. 18:1; Aef. 5:16; Yak. 3:17.)