Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

mustafahacalaki/DigitalVision Vectors via Getty Images

KHALANI MASO!

Makina Osewenza Ngati Munthu—Dalitso kapena Tsoka? Nanga Baibo Inenapo ciyani?

Makina Osewenza Ngati Munthu—Dalitso kapena Tsoka? Nanga Baibo Inenapo ciyani?

 Posacedwa, nkhume-nkhume za maiko, akatswili a sayansi, na akacenjede pa zopangapanga anathililapo ndemanga pa makina oseŵenza ngati munthu amenewa. Pofotokoza mapindu omwe abweletsa, iwo anaonetsanso nkhawa za momwe ikugwilitsidwa nchito.

  •   “Makina Oseŵenza Ngati Munthu ni cimodzi mwa zida zamakono comwe catukula umoyo wa anthu masiku ano . . . Pa nthawi imodzimodzi ikupeleka ciopsezo cacikulu kucitetezo, kuphela anthu maufulu komanso kupangitsa kukhala covuta anthu kuika cidalilo cawo pa ulamulilo wa demokalase.”—Anatelo mtsogoleli waciwili wa dziko la Amerika, Kamala Harris, pa May 4, 2023.

  •   “Ngakhale kuti Makina Oseŵenza ngati Munthu akhala othandiza pa zaumoyo mnjila zina, akupelekanso ciopsezo ku umoyo wa anthu,” kanatelo kagulu ka madokotala na akatswili a zaumoyo motsogoleledwa na Dr Frederik Federspiel, mu Nyuzi ya pa May 9, 2023, yochedwa BMJ Global Health. a

  •   “Anthu ayamba kale kusewenzetsa Makina Oseŵenza ngati munthu pofalitsa mabodza,ndipo palinso ciopsezo coti kutsogoloku anthu angasoŵe nchito. Kumbali inayi akatswili oona pa zida zamakono ali na nkhawa kuti kutsogoloku makinawa angabweletse mavuto pa anthu.”—Inatelo Nyuzi ya The New York Times, May 1, 2023.

 Pamene nthawi ikudutsa zidzawonekela bwino mmene anthu adzagwilitsile nchito makinawa, pa zabwino kapena pa zoipa. Kodi Baibo imakamba ciyani?

N’cifukwa ciyani zoyesayesa za anthu zikupatsa anthu mantha?

 Baibo imaonetsa cifukwa cake anthu sangakhale otsimikiza kuti zopangapanga za makono zingagwilitsidwe nchito pa zinthu zothandiza zokha.

  1.  1. Ngakhale pamene anthu ali na zolinga zabwino nthawi zina sangaoneletu zotulukapo zoipa za zocita zawo.

    •   “Pali njila yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.”—Miyambo 14:12.

  2.  2. Munthu sangalamulile ena mmene angagwilitsile nchito zimene iye wapanga.

    •   “Nchito yonse yovuta imene ndinali kugwila padziko lapansi pano, imene ndidzasiyile munthu amene akubwela pambuyo panga. Ndipo kodi ndani angadziwe kuti kaya adzakhala wanzelu kapena wopusa? Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinazipeza movutikila ndiponso zimene ndinazicita mwanzelu padziko lapansi pano.”—Mlaliki 2:18, 19.

 Izi zimatsimikizila mfundo yakuti timafunikila Mlengi wathu kutitsogolela.

Pamene tiyenela kuika cidalilo cathu

 Mlengi wathu analonjeza kuti sadzalola anthu kapena zinthu zimene anthuwo apanga kuti ziwononge dziko lapansi kapena mtundu wa anthu.

  •   “Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—Mlaliki 1:4.

  •   “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.—Masalimo 37:29.

 Kupitila m’Baibo Mlengi wathu amatitsogolela ku moyo wamtendele komanso wotetezeka. Kuti mudziwe zambili pa zimene Baibo imakamba ŵelengani nkhani yakuti “N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?” komanso yakuti “Tiziyembekezela Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”

a Yacokela mu nkhani yakuti “Threats by Artificial Intelligence to Human Health and Human Existence,” Yolembedwa na Frederik Federspiel, Ruth Mitchell, Asha Asokan, Carlos Umana, Komanso David McCoy.