Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FPG/The Image Bank via Getty Images

KHALANI MASO!

Andale Akucenjeza za Aramagedo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Andale Akucenjeza za Aramagedo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Pa Mande m’maŵa, pa 10 October, 2022, asilikali a Russia anaponya mabomba awo n’kuwaphulitsila m’mizinda yosiyana-siyana ya dziko la Ukraine. Iwo anacita izi pobwezela kuwonongedwa kwa ulalo wawo umene unaphulitsidwa masiku aŵili kumbuyoko. Inde ulalo wofunika kwambili wolumikiza Crimea na Russia. Izi zinacitika pambuyo pa macenjezo a nkhumenkhume zina zandale akuti tili pa ciopsezo ca kubuka kwa nkhondo ya Aramagedo.

  •   “Kucokela pa nthawi ya ulamulilo wa [Pulezidenti wa America John F.] Kennedy, pamene mabomba anaphulitsidwa pa cisumbu ca Cuba, sitinakhalepo pa ciopsezo ca nkhondo ya Aramagedo ngati mmene zilili palipano. . . . Siniona kuti pali njila iliyonse [yogwilitsa] nchito zida zanyukiliya mocenjela, moti n’kupewa nkhondo ya Aramagedo.”—Anatelo Joe Biden Pulezidenti wa America pa 6 October, 2022.

  •   “Inenso niona kuti imeneyi ni Aramagedo basi, ndipo dziko lonse lili pa ciopsezo.”—Anatelo Volodymyr Zelensky, Pulezidenti wa ku Ukraine, atafunsidwa za kuthekela kogwilitsa nchito mabomba anyukiliya, pa Nyuzi ya BBC pa 8 October, 2022.

 Kodi kuthekela kogwilitsa nchito zida za nyukiliya n’kumene kudzayambitsa nkhondo ya Aramagedo? Nanga Baibo ikutipo ciyani?

Kodi zida zanyukiliya n’zimene zidzabutsa Aramagedo?

 Ayi. Mawu akuti “Haramagedo” kapenanso kuti Aramagedo amapezeka kamodzi kokha m’Baibo pa Chivumbulutso 16:16. Mawuwa satanthauza nkhondo ya pakati pa maiko ayi, koma pakati pa Mulungu na “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 16:14) Mulungu adzagwilitsa nchito nkhondo ya Aramagedo pothetsa ulamulilo wonse wa anthu.—Danieli 2:44.

 Kuti mudziŵe zimene zidzacitike padziko lapansi nkhondo ya Aramagedo ikadzamenyedwa, ŵelengani nkhani yakuti Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?

Kodi nkhondo yanyukiliya ingadzawononge dziko lapansi pamodzi na anthu?

 Ayi. Ngakhale kuti anthu olamulila angadzaseŵenzetse zida zanyukiliya kutsogoloku, Mulungu sadzalola kuti dziko lidzawonongedwe. Baibo imati:

  •   “Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—Mlaliki 1:4.

  •   “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

 Ngakhale n’telo, maulosi a m’Baibo na zimene zikucitika palipano zionetsa kuti posacedwa tidzafika paciinde-inde cosinthilatu zinthu kumene sikunacitikepo cikhalile. (Mateyu 24:3-7; 2 Timoteyo 3:1-5) Kuti mudziŵe zimene Baibo ikamba za kutsogoloku, pemphani kuti mmodzi wa ife aziphunzila nanu Baibo kwaulele.