KHALANI MASO!
Zivomezi Zamphamvu Zisakaza ku Turkey na ku Syria —Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Pa Lolemba, February 6, 2023, zivomezi zamphamvu zinawononga ku Turkey na Syria.
“Pa Lolemba, civomezi cacikulu cinapha anthu opitilila 3,700 kudela lalikulu ku dziko la Turkey, komanso kumpoto cakumadzulo kwa dziko la Syria. Pokhalanso kuti zacitika m’nyengo yozizila koopsa, zakhala zovuta kwambili kwa anthu amene anavulala, kapena amene nyumba zawo zinawonongeka. Cifukwa ca nyengo imeneyi, kwakhalanso kovuta kwambili kwa opulumutsa anthu kugwila nchito yawo.”—Reuters, February 6, 2023.
Mitima yathu imaŵaŵa kwambili tikamaŵelenga nkhani za matsoka ngati amenewa. Akagwa mavuto otelewa, tiyenela kudalila Yehova a, “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.” (2 Akorinto 1:3) Iye anatipatsa Malemba amene amatipatsa “ciyembekezo ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.
Baibo imatiphunzitsa nkhani izi:
Zimene zinanenedwelatu zokudza zivomezi.
Kumene tingapeze citonthozo na ciyembekezo.
Mmene Mulungu adzacotselepo mavuto onse.
Kuti mudziŵe zimene Baibo imakamba pa nkhani zimenezi, ŵelengani nkhani zotsatilazi:
a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.