MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO
Zimene Zimacitika Popanga Sewelo Lakuti Mbili ya Moyo wa Yesu
OCTOBER 1, 2024
Caka cino, cinthu cimodzi cimene Mboni za Yehova zakhala zikuyembekezela mwacidwi ndi kutulutsidwa kwa Gawo 1 la sewelo lakuti Mbili ya Moyo wa Yesu. Anthu mamiliyoni alionelela kale sewelo limeneli. Ndipo limeneli ndi gawo loyamba pa magawo 18 a seweloli! Kodi n’ciyani cimacitika popanga mavidiyo amenewa? Nanga inu mukuthandiza bwanji pa nchitoyi?
Kusamalila Abale ndi Alongo Amene Akuthandiza Kupanga Vidiyoyi
Ku ofesi ya nthambi ya ku Australasia, kumene mbali yaikulu ya sewelo lakuti Mbili ya Moyo wa Yesu likujambulidwa, anthu pafupifupi 50 mpaka 80 amapezekapo pojambula mbali iliyonse. a Pali abale ndi alongo amene amakonza cakudya camasana, camadzulo, komanso zakudya zina za ojambulidwa komanso abale ndi alongo ojambula. Abalewa amadziwilatu cakudya cimene adzakonze kukali nthawi yokwanila. Esther, amene ali mu Dipatimenti Yoona pa Zakudya anati: “Kuti tizikhala ndi zakudya zabwino koma pamtengo wabwino, timagula zakudya kwa ogulitsa osiyanasiyana. Timasinthasitha mtundu wa zakudya zimene timaphika n’colinga cakuti zina zisamatayike.” Tsiku lililonse, timagwilitsa nchito madola 4 b pogula zakudya za munthu aliyense.
Abale ndi alongo amene akuthandiza popanga vidiyoyi, safunikila cakudya cokha koma amafunikilanso citetezo. Kutetezedwa ku ciyani? Nthawi zambili ku Australia kumakhala kotentha komanso kowala bwino, koma nthawi zina kutentha kumeneko kumakhala kopambanitsa. Pofuna kuti aliyense akhale wotetezeka ku dzuwa komanso kuti asafooke cifukwa ca kutentha, abale ndi alongo odzipeleka amakonza tumatenti komanso malo kumene anthu angapumulile. Amaonetsetsanso kuti mafuta odzitetezela ku dzuwa, ma ambulela, ndi madzi zilipo zokwanila. Kevin, amene amagwila nchito mu Dipatimenti Yoona za Mavidiyo ndi Zomvetsela, ananena kuti: “Ambili mwa abale ndi alongo amene amagwila nchito imeneyi ndi atumiki a pa Beteli ocita kuyendela. Amagwila nchito zimenezi ndi zina zambili modzicepetsa komanso mosangalala. Sitikanakwanitsa kupanga vidiyo imeneyi popanda thandizo lawo.”
Kujambulila Kutali Ndi Ofesi ya Nthambi
Mbali zina za seweloli sizingajambulidwile pa ofesi ya nthambi, cifukwa sizingaoneke ngati zenizeni. Pojambula mbali zotelo, ojambulawo amapita kumalo ena oyenelela kutali ndi ofesi ya nthambi. Pofuna kujambula nkhani zakale za m’Baibulo kumalo kumene kulibe nthambo za magetsi, misewu, komanso nyumba zamakono, opanga vidiyoyi amafunika kupita kumalo akutali kwambili. Zovala zawo zojambulila ndi zinthu zina, komanso makina ojambulila, zimalongedwa bwino n’kupelekedwa kumalo ojambulilawo. Kumeneko amazisunga kwa kanthawi pamalo otetezeka. Nchito yojambula isanayambe, abale amene amathandizila woyang’anila nchito yojambula seweloli amaonetsetsa kuti majeneleta, madzi akumwa aukhondo, komanso zimbudzi ndi mabafa ziliko. Abale opanga vidiyoyi, amakhala m’nyumba za abale a kumaloko, m’makontena a galimoto okonzedwa bwino, m’mahotela, kapena m’nyumba zamatabwa.
Kujambulila kumalo akutali kumafuna ndalama zambili, komanso nthawi yoculuka, ndipo kungakhale kolemetsa kwa onse olowetsedwamo. Conco, mu 2023, Bungwe Lolamulila linapeleka cilolezo cakuti pagulidwe masikilini ojambulila mavidiyo a ndalama zokwana madola 2.5-milliyoni. Masikilini amenewa amapangitsa kuti munthu akajambulidwa, azioneka ngati anajambulidwila kumalo ena ake. Pojambula mwa njila imeneyi, amagwilitsa nchito masikilini oonetsa zinthunzi zooneka bwino kwambili, komanso zounikila zapadela zimene zimapangitsa kuti vidiyoyo izioneka ngati anaijambulila panja kumalo ena ake. Izi zacititsa kuti nthawi zambili, tizipewa kuwononga ndalama zoculuka mwa kupita kumalo akutali. M’bale Darren, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Australasia, anati: “Kujambula pogwilitsa nchito masikilini ojambulila, kwathandiza kuti ojambulidwa asamakhale olema kwambili, komanso kuti ojambula azitha kujambula mbali zina mobwelezabweleza. Mwacitsanzo, zikanakhala kuti tinali kujambulila panja, tikanakhala ndi nthawi yocepa yojambula dzuwa likulowa cifukwa dzuwa siliima. Koma pogwilitsa nchito masikilini amenewa, tingathe kubweleza mbali ya kulowa kwa dzuwa mpaka titakhutila ndi zimene tajambula.”
“Cimwemwe Cimene Ndinapeza Cinaposa Zonse Zimene Ndinadzimana”
Pojambula mbali iliyonse ya sewelo lakuti Mbili ya Moyo wa Yesu, pamafunika anthu mahandiledi ojambulidwa komanso ojambula ambilimbili. Kodi iwo amamva bwanji poona zimene abale ndi alongo amacita powasamalila?
Amber, amene anayenda mtunda wopitilila makilomita 700 kucokela ku mzinda wakwawo wa Melbourne kuti akagwileko nchito imeneyi anati: “Kungocokela pamene n’nafika pamalo okwelela ndeke, abale a pa Beteli ananisamalila bwino kwambili. Atumiki ambili a pa Beteli anandiitanila ku cakudya. Ku malo ojambulila, onse anali kundipangitsa kudzimva wotetezeka komanso wokondedwa. N’nalandila madalitso oculuka pa ulendo umenewu. Cimwemwe cimene n’napeza cinaposa zinthu zonse zimene ndinadzimana!”
Derek, amene anagwilako nchito yopanga mavidiyowa anati: “Madipatimenti ambili akhala akutithandiza kucokela pamene nchitoyi inayamba. Ndimayamikila kwambili kugwila nchito ndi abale komanso alongo amene amagwilitsa nchito nthawi yawo, zinthu zawo, komanso mphamvu zawo panchito imeneyi. Iwo amatithandiza modzipeleka ndiponso mokoma mtima. N’zoonekelatu kuti Yehova waadalitsa ndipo nafenso watidalitsa. Ndine wotsimikiza kuti iye amayamikila osati cabe zotulukapo za nchito yathu koma mmenenso timaigwilila nchitoyi.”
Zikomo kwambili pa thandizo limene mwapeleka pa nchito yopanga mavidiyo amenewa mwa zopeleka zanu, kuphatikizapo zija zimene mumacita kupitila pa donate.jw.org.