Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa—Mavidiyo

PHUNZILO 1

Mawu Oyamba Ogwila Mtima

Kodi mungacite ciani kuti anthu amvetsele zimene mukambe?

PHUNZILO 2

Kukambilana Mwacibadwa

Mungawathandize bwanji omvetsela kuti amasuke pamene mukamba nawo?

PHUNZILO 3

Gwilitsilani Nchito Mafunso

Kodi mungagwilitsile nchito bwanji mafunso kuti mulingalile na omvetsela, kuwakopa cidwi, na kugogomeza mfundo zofunika?

PHUNZILO 4

Kachulidwe ka Malemba Koyenela

Kodi mungakonzekeletse bwanji omvetsela kuti apindule kwambili na malemba amene mudzaŵelenga?

PHUNZILO 5

Kuŵelenga Bwino

N’ciani cingatithandize kuti tizichula mawu ndendende mmene awalembela tikamaŵelenga?

PHUNZILO 6

Kumveketsa Bwino Cifukwa Coŵelengela Lemba

Mufunika kucita ciani pambuyo poŵelenga lemba kuti muthandize omvetsela kumvetsa cifukwa cimene mwaŵelengela lembalo?

Kukamba Zoona Zokha-Zokha Komanso Zokhutilitsa

Mungacite ciani kuti muzikamba zoona zokha-zokha?

PHUNZILO 8

Mafanizo Ophunzitsadi Kanthu

Potengela citsanzo ca Mphunzitsi Wamkulu, kodi mungaseŵenzetse bwanji mafanizo mogwila mtima?

PHUNZILO 9

Kuseŵenzetsa Bwino Zitsanzo Zooneka

Kodi zitsanzo kapena zinthu zina zooneka, mungaziseŵenzetse bwanji pothandiza omvela kumvetsa mfundo zofunika?

PHUNZILO 10

Kusinthasintha Mawu

N’cifukwa ciani kusintha-sinthako mawu n’kofunika kuti tingamveketse bwino malingalilo, na kukhudza mtima omvetsela?

PHUNZILO 11

Kukamba Mwaumoyo

Kodi mungakambe bwanji mwaumoyo kuti mulimbikitse omvetsela kucitapo kanthu?

PHUNZILO 12

Mzimu Waubwenzi na Cifundo

Mungaonetse bwanji mzimu waubwenzi na cifundo kwa omvetsela?

PHUNZILO 13

Kumveketsa Phindu ya Nkhani

Kodi mungamveketse bwanji phindu ya nkhani yanu, komanso kulimbikitsa omvetsela kucitapo kanthu?

PHUNZILO 14

Kumveketsa Bwino Mfundo Zazikulu

Thandizani omvela kukutsatilani m’nkhani yanu, kumvetsetsa, komanso kukumbukila zimene muphunzitsa mwa kumveketsa mfundo zazikulu.

PHUNZILO 15

Kukamba Motsimikiza

Kodi mungakambe bwanji motsimikiza pamene mukamba nkhani kapena kulalikila?

PHUNZILO 16

Khalani Wolimbikitsa Komanso Wotsitsimula

Ni zinthu zitatu ziti zimene tifunika kucita kuti tizikamba zinthu zothandiza komanso zolimbikitsa?

PHUNZILO 17

Muzikamba Zosavuta Kumvetsa

Kodi mufunika kupewa ciani pamene muthandiza omvela anu kumvetsa tanthauzo la zimene mukukamba?

PHUNZILO 18

Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvela

Kodi mungaphunzitse bwanji m’njila yopangitsa omvela anu kuona kuti aphunzilapodi kanthu?

Mungakondenso Izi

MABUKU NA MABULOSHA

Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa

Kabuku kano kanakonzedwa kuti kakuthandizeni kunola maluso anu a kuŵelenga, kulankhula, komanso kuphunzitsa.