Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Kodi Mulungu ndiye acititsa mavuto?
Kodi mungayankhe kuti:
Inde
Iyai
Kapena
Zimene Baibo imakamba
“Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.” (Yobu 34:10) Mulungu si amene acititsa zoipa kapena mavuto amene tiona padziko.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Satana Mdyelekezi, amene ni “wolamulila wa dziko,” ndiye amacititsa mavuto ambili. —Yohane 14:30.
Mavuto na zinthu zina zoipa zimacitika cifukwa anthu ena amasankha kucita zoipa —Yakobo 1:14, 15.
Kodi mavuto adzasila?
Ena amakhulupilila kuti anthu angakwanitse kuthetsa mavuto ngati acita zinthu mogwilizana. Pamene ena amaona kuti mavuto sangasile padziko. Inu muganiza bwanji?
Zimene Baibo imakamba
Mulungu adzathetsa mavuto. “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Mfundo zina zimene tingaphunzile m’Baibo
Mulungu adzaseŵenzetsa Yesu kuti acotse mavuto onse amene Mdyelekezi amacititsa. —1 Yohane 3:8.
Anthu abwino adzakhala na mtendele woculuka padziko lapansi kwamuyaya. —Salimo 37:9-11, 29.