Nkhani Ya Pacikuto
Why Understand the Bible?
“Baibulo ndi buku la cipembedzo lodziŵika kwambili. Koma kwa anthu a Cichainizi ndi buku lacilendo ndipo n’losathandiza.”—LIN, CHINA.
“Sindimvetsetsa mabuku oyela acipembedzo canga ca Cihindu. Ndiye ndingakwanitse bwanji kumvetsetsa Baibulo Lopatulika?”—AMIT, INDIA.
“Ndimalemekeza Baibulo cifukwa ndi buku lakale, ndipo ndamva kuti anthu amaligula kwambili. Koma sindinalionepo.”—YUMIKO, JAPAN.
Anthu ambili padziko lonse amalemekeza kwambili Baibulo. Ngakhale n’conco, io amadziŵa nkhani zocepa za m’Baibulo mwinanso sazidziŵa n’komwe. Mfundo imeneyi ndi yoona. Mwacitsanzo, anthu mamiliyoni a ku Asia sadziŵa zimene Baibulo limakamba. N’cimodzimodzinso ndi anthu ambili a m’maiko amene Baibulo ndi lofala kwambili.
Mwina mungadzifunse kuti: N’cifukwa ciani ndifunika kumvetsetsa Baibulo? Kumvetsetsa buku lopatulika limeneli, kudzakuthandizani kucita zotsatilazi:
-
Kukhala wokhutila ndi wacimwemwe
-
Kulimbana ndi mavuto a m’banja
-
Kulimbana ndi nkhawa za paumoyo
-
Kukhala bwino ndi anthu ena
-
Kuseŵenzetsa ndalama mwanzelu
Mwacitsanzo, mvelani zimene Yoshiko wa ku Japan anakamba. Iye sanali kudziŵa zimene Baibulo limakamba. Conco, anaganiza zoyamba kuliŵelenga. Nanga panali zotsatilapo zotani? Iye anakamba kuti: “Baibulo landithandiza kukhala ndi umoyo waphindu ndi kukhala ndi ciyembekezo cabwino ca mtsogolo. Tsopano ndili ndi umoyo wokhutilitsa.” Amit amene tamuchula kuciyambi kwa nkhani ino, nayenso anayamba kuphunzila Baibulo payekha. Iye anati: “Ndinadabwa kwambili ndi uthenga wa m’Baibulo. M’bukuli, muli mfundo zothandiza kwa munthu aliyense.”
Baibulo lathandiza anthu ambili kusintha umoyo wao. Bwanji osaliŵelenga ndi kuona mmene lingakuthandizileni inuyo panokha?