N’cifukwa Ciani Timalalikila?
Timadziŵika ndi nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba, pamalo amene pamapezeka anthu ambili ndi kulikonse kumene tapeza anthu. N’cifukwa ciani timagwila nchito imeneyi?
Mboni za Yehova zimalalikila n’colinga cotamanda Mulungu ndi kudziŵitsa anthu dzina lake. (Aheberi 13:15) Timafunanso kumvela lamulo la Kristu Yesu lakuti: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—Mateyu 28:19, 20.
Kuonjezela apo, timakonda anzathu. (Mateyu 22:39) Timadziŵa kuti anthu ambili ali ndi zipembedzo zao ndipo timadziwanso kuti si anthu onse amene angalandile uthenga wathu. Ngakhale n’telo, timaona kuti ziphunzitso za m’Baibulo zimapulumutsa miyoyo ya anthu. N’cifukwa cake timapitiliza “mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Kristu Yesu,” mmene anacitila Akristu oyambilila.—Machitidwe 5:41, 42.
Katswili wa cikhalidwe dzina lake Antonio Cova Maduro analemba za Mboni za Yehova kuti “pogwila nchito yolalikila zimakumana ndi mavuto ndipo zimalema kwambili. Koma zimapitiliza kugwila nchitoyi kuti uthenga wopatulika ufalikile padziko lonse lapansi.”—El Universal Nyuzipepala ya Venezuela
Anthu ambili amene amaŵelenga mabuku athu si a Mboni za Yehova. Ndipo anthu mamiliyoni amene amaphunzila nafe Baibulo ali ndi zipembedzo zao. Iwo amayamikila kuti Mboni za Yehova zimawafikila panyumba zao.
Mwina mungakhale ndi mafunso ena okhudza Mboni za Yehova. Kuti mupeze mayankho ake, tikupemphani kuti,
Mufunse mmodzi wa Mboni za Yehova.
Mupite pa webusaiti yathu ya www.jw.org.
Mukabwele ku misonkhano yathu, sitilipilitsa.