Pemphelo —Kodi Lingakuthandizeni Bwanji?
Tisanacite ciliconse, mwacibadwa timadzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzapeza phindu lotani?’ Kodi n’kulakwa kufunsa funso limeneli pa nkhani ya pemphelo? Osati kwenikweni. Mwacibadwa, timafuna kudziŵa ngati cimene tifuna kucita cili ndi phindu lililonse. Ngakhale munthu wabwino Yobu anafunsa kuti: “Nditamuitana, kodi angandiyankhe?”—Yobu 9:16.
M’nkhani zoyambilila, taona umboni wakuti pemphelo n’lofunika kwambili osati polambila cabe kapena tikapanikizika maganizo. Mulungu woona amamva mapemphelo. Ngati tipemphela m’njila yovomelezeka ndipo timapempha zinthu zoyenela, Mulungu adzatimvetsela. Ndipo iye amatipempha kuti timuyandikile. (Yakobo 4:8) Conco, kodi tidzapindula bwanji ngati timapemphela tsiku ndi tsiku? Tiyeni tikambilane ena mwa mapindu a pemphelo.
Timakhala ndi mtendele wa m’maganizo.
Mukakumana ndi mavuto paumoyo wanu, kodi mumada nkhawa kwambili? Panthawi ngati imeneyi, Baibulo limatilimbikitsa ‘kupemphela mosalekeza,’ komanso kuti ‘zopempha zathu zidziŵike kwa Mulungu.’ (1 Atesalonika 5:17; Afilipi 4:6) Baibulo limatitsimikizila kuti ngati tipemphela kwa Mulungu, “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu].” (Afilipi 4:7) Ngati tiuza Atate wathu wakumwamba nkhawa zathu, tidzakhala ndi mtendele wa m’mganizo. Ndipotu iye amatilimbikitsa kucita zimenezi. Lemba la Salimo 55:22 limati: “Umutulile Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakucilikiza.”
“Umutulile Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakucilikiza.”—Salimo 55:22
Anthu ambili padziko lonse lapansi akhalapo ndi mtendele umenewo. Mkazi wina dzina lake Hee Ran
wa ku South Korea anakamba kuti: “Ndikakhala ndi mavuto aakulu, ndimapemphela ndipo ndikatelo, ndimamva bwino ndipo ndimamva kuti ndili ndi mphamva zopilila mavutowo.” Nayenso Cecilia wa ku Philippines anakamba kuti: Monga kholo, ndimada nkhawa kwambili ndi ana anga komanso amai anga amene tsopano sakwanitsa kundidziŵa cifukwa ca ukalamba ndi matenda. Koma ndimakwanitsa kucita zofunika za tsiku ndi tsiku ndili ndi nkhawa zocepa cifukwa ca pemphelo. Ndikudziŵa kuti Yehova adzandithandiza kuwasamalila.”Timatonthozedwa ndi kulimbikitsidwa tikakumana ndi mayeselo.
Kodi ndinu wopanikizika maganizo cifukwa cakuti moyo wanu uli pangozi kapena mukukumana ndi mavuto aakulu? Kupemphela kwa “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse” kungatipatse mpumulo waukulu. Baibulo limatiuza kuti iye “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Mwacitsanzo, panthawi ina pamene Yesu anapanikizika maganizo, “anagwada ndi kuyamba kupemphela.” Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? “Mngelo wocokela kumwamba anaonekela kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:41, 43) Mwamuna wina wokhulupilika Nehemiya, anaopsezedwa ndi anthu oipa amene anayesetsa kumuletsa kugwila nchito ya Mulungu. Iye anapemphela kuti: “Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.” Zocitika zimene zinatsatilapo, zikuonetsa kuti Mulungu anamuthandiza kugwila bwino nchito yake. (Nehemiya 6:9-16) Ponena za pemphelo, Reginald wa ku Ghana anafotokoza kuti: “Ndikapemphela, makamaka pamene ndili pamavuto, ndimamva kuti ndafotokozela munthu amene ali ndi njila yondithandizila ndipo amanditsimikizila kuti ndisade nkhawa.” Zoonadi, Mulungu amatitonthoza tikapemphela kwa iye.
Timalandila nzelu zocokela kwa Mulungu.
Zinthu zina zimene timasankha zimatikhudza ndipo zingakhudzenso anthu ena amene timakonda. Nanga tingasankhe bwanji zinthu mwanzelu? Baibulo limati: “Ngati wina akusoŵa nzelu [makamaka panthawi ya mayeselo], azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka moolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.” (Yakobo 1:5) Tikapempha nzelu kwa Mulungu, iye amatipatsa mzimu woyela kuti utithandize kusankha zinthu mwanzelu. Ndipo tiyenela kupempha mzimu woyela cifukwa Yesu anatitsimikizila kuti, “Atate wakumwamba adzapeleka moolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.
Ngakhale Yesu anaona kuti kupempha Atate wake kuti am’thandize kusankha zinthu mwanzelu n’kofunika. Baibulo limatiuza kuti pamene Yesu anafuna kusankha amuna 12 kuti akhale otsatila ake, “anacezela kupemphela kwa Mulungu usiku wonse.”—Luka 6:12.
Mofanana ndi Yesu, anthu ambili masiku ano amalimbikitsidwa akaona mmene Mulungu wawathandizila kusankha zinthu mwanzelu. Regina wa ku Philippines anafotokoza mavuto osiyanasiyana amene anakumana nao. Mavuto monga kupezela banja lake zinthu zofunika pambuyo pa imfa ya mwamuna wake, kucotsedwa nchito, ndi kulela ana. N’ciani camuthandiza kusankha zinthu mwanzelu? Iye anakamba kuti: “Mwapemphelo ndimadalila thandizo la Yehova.” Kwabena wa ku Ghana, anakamba cifukwa cake anapempha Mulungu kuti amuthandize. Iye anati: “Ndinacotsedwa pa nchito ya zomangamanga imene inali ya malipilo abwino.” Poganizila zocita, iye anati: “Ndinapemphela kwa Yehova mosalekeza kuti andithandize kusankha zinthu mwanzelu.” Iye anapitiliza kuti: “Ndimakondwela kuti Yehova anandithandiza kusankha nchito imene imandithandiza kupeza zofunika za paumoyo ndi kucita zinthu za kuuzimu.” Inunso, Mulungu adzakutsogolelani ngati mupempha thandizo pa zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wanu ndi iye.
Takambilana zinthu zocepa cabe za mmene pemphelo lingakuthandizileni. (Kuti mudziŵe zambili onani bokosi lakuti “Ubwino wa Pemphelo.”) Koma kuti inu mulandile madalitso amenewa, coyamba muyenela kudziŵa Mulungu ndi cifunilo cake. Ngati mufuna kudziŵa za Mulungu, tikukulimbikitsani kupempha wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kuphunzila Baibulo. * Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuyandikila “Wakumva pemphelo.”—Salimo 65:2.
^ par. 13 Kuti mudziŵe zambili, pemphani a Mboni za Yehova a m’dela lanu kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.jw.org.