Kodi Yehova Waonetsa Bwanji Kuti Amatikonda?
“Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza.”—1 YOHANE 3:1.
1. Kodi mtumwi Yohane anatilimbikitsa kuti tiziganizila za ciani? Nanga n’cifukwa ciani?
MTUMWI Yohane anatilimbikitsa kuti tiziganizila kwambili za cikondi cacikulu ca Yehova pa ife. Pa 1 Yohane 3:1 timaŵelenga kuti: “Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza.” Ngati tisinkhasinkha za cikondi cacikulu ca Yehova pa ife ndi mmene amacionetsela, timam’yandikila ndi kum’konda kwambili.
2. N’cifukwa ciani ena zimawavuta kukhulupilila kuti Yehova amaŵakonda?
2 N’zacisoni kuti anthu ena amaona kuti Mulungu sangawakonde. Iwo amakhulupilila kuti Mulungu amaona anthu kuti ndi acabecabe. Amaona kuti Iye amapanga cabe malamulo ndi kulanga amene samumvela. Cifukwa ca ziphunzitso zabodza, ena amaganiza kuti Mulungu ndi woipa mtima, ndipo n’zosatheka kum’konda. Ena amaona kuti Mulungu amakonda anthu onse mosasamala kanthu za zimene io amacita. Koma inu Yohane 3:16; 1 Yohane 4:8) Komabe, cifukwa ca mavuto amene mwakumana nao pa umoyo wanu, zingakuvuteni kukhulupilila kuti Yehova amakukondani kwambili.
cifukwa cophunzila Baibulo, mwadziŵa coonadi ponena za Yehova. Mwadziŵa kuti khalidwe lake lalikulu ndi cikondi, ndi kuti anakupatsani Mwana wake kuti akhale dipo lanu. (3. N’ciani cidzatithandiza kukhulupilila kuti Yehova amatikonda?
3 Kuti tikhulupilile kuti Yehova amatikonda, coyamba tiyenela kukhulupilila kuti iye ndiye anatipanga ndi kutipatsa moyo. (Ŵelengani Salimo 100:3-5.) Ndiye cifukwa cake Baibulo limakamba kuti munthu woyamba ndi “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Ndipo Yesu anatiphunzitsa kuti tiziitana Yehova kuti “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Conco, Yehova ndi Atate wathu ndipo amatikonda monga mmene tate wabwino amakondela ana ake.
4. (a) Kodi Yehova ndi Tate wotani? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino ndi yotsatila?
4 Anthu ena zimawavuta kukhulupilila kuti tate ndi munthu wacikondi. Akamaganizila za moyo wao akali ana, amawawidwa mtima cifukwa ca nkhanza imene atate ao anawacitila. Koma Yehova sangacitile ana ake zimenezo. Iye ndi Tate wabwino koposa. (Salimo 27:10) Iye amatikonda kwambili ndi kutisamalila m’njila zambili. Tikamaona mmene Yehova amatikondela, timayamba kum’konda kwambili. (Yakobo 4:8) M’nkhani ino, tikambilana njila zinai zimene Yehova amationetsela cikondi cake. Ndipo m’nkhani yotsatila, tidzakambilana njila zinai zimene tingaonetsele kuti timakonda Mulungu.
YEHOVA NDI WACIKONDI NDIPONSO WOOLOWA MANJA
5. N’ciani cimene Mulungu amapatsa anthu onse?
5 Pamene mtumwi Paulo anali ku Atene ku Girisi, anaona kuti kunali mafano ambili. Anthu anali kukhulupilila kuti mafanowo ndiye anawapatsa moyo. Conco, iye anawauza za “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu.” Anakamba kuti Mulungu “amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse,” ndipo “cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Machitidwe 17:24, 25, 28) Yehova amatipatsa zinthu zonse zimene timafunikila kuti tikhale moyo ndi kusangalala. Mungacite bwino kuganizila zina mwa zinthu zimene iye watipatsa cifukwa cotikonda.
6. Ndi malo okhalamo otani amene Yehova anatipatsa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
6 Mwacitsanzo, Yehova anatipangila malo okongola okhalamo. (Salimo 115:15, 16) Pa mapulaneti onse amene iye analenga, dziko lathuli ndiye lapadela. Asayansi atafufuza, anapeza mapulaneti ena ambili. Koma sanapeze pulaneti lina limene lili ndi zinthu zonse zimene anthu amafunikila kuti akhalebe ndi moyo. Yehova sanatipatse cabe zinthu zimene tifunikila kuti tikhale ndi moyo, koma anapanganso dzikoli kuti likhale lokongola, labwino kukhalamo, ndi lotetezeka kuti tisangalale ndi umoyo. (Yesaya 45:18) Tikaganizila za malo abwino okhalamo amene Atate wathu, Yehova, anatipatsa, timaona kuti iye amatikonda kwambili.—Ŵelengani Yobu 38:4, 7; Salimo 8:3-5.
7. Kodi mmene Yehova anatilengela zimaonetsa bwanji kuti amatikondadi?
7 Yehova anatilenga m’njila yakuti tizitha Genesis 1:27) Zimenezi zitanthauza kuti tikhoza kuona kuti iye amatikondadi, ndipo ifenso tikhoza kumuonetsa kuti timam’konda. Iye amadziŵa kuti zimenezi zimatipatsa cimwemwe ceniceni. Ngakhale ana amasangalala kwambili akadziŵa kuti makolo ao amawakonda. Ndipo musaiŵale kuti Yesu anatiphunzitsa kuti tikayandikila Atate wathu Yehova, tidzakhala osangalala kwambili. (Mateyu 5:3) Iye amatipatsa “zinthu zonse kuti tisangalale.” N’zoonekelatu kuti iye ndi woolowa manja, ndipo amatikonda kwambili.—1 Timoteyo 6:17; Salimo 145:16.
kutengela citsanzo cake. Imeneyi ndi njila ina imene waonetsela kuti amatikonda. (YEHOVA AMATIPHUNZITSA COONADI
8. N’cifukwa ciani tifuna kuti Yehova azitiphunzitsa?
8 Tate amakonda ana ake ndipo safuna kuti io azisoceletsedwa ndi kunamizidwa. Komabe, makolo ambili masiku ano savomeleza miyezo ya m’Baibulo ya Miyambo 14:12) Koma Yehova amatsogolela bwino kwambili ana ake cifukwa iye ndi “Mulungu wacoonadi.” (Salimo 31:5) Iye amakondwela kutiphunzitsa coonadi ponena za iye ndiponso mmene tingamulambilile. Ndipo amationetsa njila yabwino imene tingakhalile paumoyo wathu. (Ŵelengani Salimo 43:3.) Nanga ndi zinthu ziti zimene Yehova amatiphunzitsa zimene zimaonetsa mmene amatikondela?
cabwino ndi coipa. Pa cifukwa cimeneci, io amalephela kutsogolela bwino ana ao. Izi zimapangitsa banja kukhala losasangalala ndiponso losagwilizana. (9, 10. (a) N’cifukwa ciani Yehova amatiuza za iye? (b) Nanga amatiphunzitsa ciani za colinga cake kwa ife?
9 Coyamba, Yehova amatiuza za iye cifukwa amafuna kuti timudziŵe. (Yakobo 4:8) Conco watiuza dzina lake. Ndipo ngati pali dzina limene limachulidwa kwambili m’Baibulo, ndi dzina lake. Yehova watiuzanso za makhalidwe ake. Tikayang’ana zinthu zimene analenga, timaphunzila kuti ndi wamphamvu ndiponso wanzelu. (Aroma 1:20) Ndipo tikamaŵelenga Baibulo, timaphunzila kuti Iye ndi wacilungamo ndiponso wacikondi. Pamene tiphunzila za makhalidwe abwino a Yehova, timam’yandikila kwambili.
Pamene tiphunzila za makhalidwe abwino a Yehova timam’yandikila kwambili
10 Yehova amatiphunzitsanso za colinga cake. Amatiuza kuti ndife mbali ya banja lake. Iye amatifotokozela zimene tiyenela kucita kuti tizigwila nchito mogwilizana ndiponso mwamtendele ndi anthu onse a m’banja lake. Baibulo limaonetselatu kuti Mulungu sanatilenge m’njila yakuti tizidzisankhila cabwino ndi coipa. (Yeremiya 10:23) Yehova amadziŵa zinthu zotiyenelela. Ndipo ngati tigonjela kuulamulilo wake ndi kumumvela, tidzakhala ndi moyo wamtendele ndiponso wopindulitsa. Yehova watiphunzitsa coonadi cimeneci cifukwa amatikonda.
11. Ponena za tsogolo lathu, n’ciani cimene Atate wathu wacikondi watiuza?
11 Tate wacikondi amaganizila mwakuya za tsogolo la ana ake. Iye amafuna kuti io adzakhale ndi moyo wabwino. N’zacisoni kuti anthu ambili masiku ano amadela nkhawa kwambili za tsogolo lao. Ndipo ambili amagwilitsa nchito moyo wao kufunafuna zinthu zosakhalitsa. (Salimo 90:10) Ndife oyamikila kwambili kuti Atate wathu Yehova watiphunzitsa mmene tingakhalile ndi moyo wabwino tsopano, ndipo watilonjeza tsogolo labwino kwambili.
YEHOVA AMATSOGOLELA NDI KULANGIZA ANA AKE
12. Kodi Yehova anathandiza bwanji Kaini ndi Baruki?
12 Yehova ataona kuti Kaini watsala pang’ono kucita coipa, anayesa kum’thandiza mwa kum’funsa kuti: “N’cifukwa ciani wapsa mtima conco, ndipo nkhope yako yagwelanji? Ukasintha n’kucita cabwino, sindikuyanja kodi?” (Genesis 4:6, 7) Koma Kaini sanalandile thandizo la Yehova ndipo anavutika kwambili ndi zotsatilapo zake. (Genesis 4:11-13) Panthawi ina, Yehova anazindikila kuti Baruki wayamba kulefuka ndi kutopa cifukwa ca maganizo olakwika. Conco Yehova anamuuzilatu Baruki kuti maganizo ake anali olakwika ndipo anafunika kusintha. Baruki anamvela malangizo a Yehova ndipo anapulumutsa moyo wake.—Yeremiya 45:2-5.
13. N’ciani cimene atumiki okhulupilika a Yehova anaphunzila panthawi ya mavuto?
13 Yehova amatitsogolela ndi kutilangiza cifukwa amatikonda. Iye samangokhalila kutiongolela tikalakwitsa, koma amatiphunzitsa. (Aheberi 12:6) M’Baibulo, timaŵelenga za atumiki okhulupilika amene Yehova anaphunzitsa kuti akhale anthu abwino. Mwacitsanzo, Yosefe, Mose, ndi Davide anakumana ndi mavuto aakulu. Koma pamene anali kukumana ndi mavutowo, Yehova anali nao. Ndipo zinthu zimene anaphunzila panthawi ya mavuto zinawathandiza panthawi imene Yehova anawapatsa maudindo aakulu. Tikamaŵelenga m’Baibulo mmene Yehova anacilikizila ndi kuphunzitsila anthu ake, timaona kuti Iye amatikondadi.—Ŵelengani Miyambo 3:11, 12.
14. Kodi Yehova amationetsa bwanji kuti amatikonda tikalakwa?
14 Tikalakwa, Yehova amapitiliza kutionetsa cikondi. Tikamvela malangizo ake ndi kulapa, iye amatikhululukila “ndi mtima wonse.” (Yesaya 55:7) Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Mau amene Davide anakamba ponena za mmene iye amatikhululukila, amaonetsa kuti tilidi ndi Atate wacifundo. Davide anati: “Tamanda amene akukhululukila zolakwa zako zonse, iye amene akukucilitsa matenda ako onse. Tamanda amene akuombola moyo wako kudzenje, amene akukuveka kukoma mtima kosatha ndi cifundo ngati cisoti cacifumu. Monga mmene kum’mawa kwatalikilana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikila kutali zolakwa zathu.” (Salimo 103:3, 4, 12) Yehova amatitsogolela ndi kutilangiza m’njila zosiyanasiyana. Kodi mumasintha mwamsanga? Nthawi zonse muzikumbukila kuti Yehova amatilangiza cifukwa amatikonda.—Salimo 30:5.
YEHOVA AMATITETEZA
15. Ndi njila ina iti imene Yehova amaonetsela kuti amatikonda?
15 Tate wacikondi amateteza banja lake ku ngozi. N’zimenenso Atate wathu Yehova amacita. Pokamba za Yehova, wamasalimo anati: “Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupilika. Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.” (Salimo 97:10) Ganizilani izi: Mukaona cinthu cimene cingaononge maso anu, mumacitapo kanthu mwamsanga kuti muwateteze cifukwa ndi amtengo wapatali kwa inu. Nayenso Yehova amacitapo kanthu mwamsanga kuti ateteze anthu ake cifukwa ndi a mtengo wapatali kwa iye.—Ŵelengani Zekariya 2:8.
Yehova amacitapo kanthu mwamsanga kuti ateteze anthu ake cifukwa ndi a mtengo wapatali kwa iye
16, 17. Kodi Yehova anateteza bwanji anthu ake akale? Nanga masiku ano amawateteza bwanji anthu ake?
16 Njila ina imene Yehova anatetezela anthu ake kale ndiponso masiku ano, ndi kupitila mwa angelo. (Salimo 91:11) Mngelo mmodzi anapha asilikali 185,000 a Asuri usiku umodzi ndi kupulumutsa anthu a Mulungu. (2 Mafumu 19:35) M’nthawi ya atumwi angelo anapulumutsa Petulo, Paulo, ndi atumwi ena mwa kuwacotsa m’ndende. (Machitidwe 5:18-20; 12:6-11) Posacedwapa m’dziko lina la mu Africa munali nkhondo yoopsa. M’dzikolo munali msokonezo cifukwa anthu anali kumenyana, kuba, kugona anthu mwacikakamizo, ndiponso kuphana. Ngakhale kuti palibe Mboni ya Yehova imene inaphedwa, ambili anataikilidwa katundu wao wonse. Ngakhale n’conco, io anaona kuti Yehova amawakonda ndipo anali kuwasamalila. Mosasamala kanthu za mavuto ao, io anali osangalalabe. Pamene m’bale woimila likulu lathu anacezela abale ndi alongo ndi kuwafunsa mmene zinthu zilili, io anati: “Zonse zili bwino, Yehova anatithandiza.”
17 Atumiki ena a Yehova, monga wophunzila Sitefano ndi ena, anaphedwa cifukwa ca kukhulupilika kwao. Nthawi zina Yehova amalola zimenezi kucitika. Komabe, iye amateteza anthu ake monga gulu mwa kuwacenjeza za njila zosiyanasiyana zimene Satana amagwilitsila nchito kuti awasoceletse. (Aefeso 6:10-12) Macenjezo amenewa timawapeza m’Baibulo ndi m’mabuku amene gulu la Yehova limafalitsa. Mwacitsanzo, timaphunzila za zinthu zoipa zimene zimapezeka pa Intaneti, kuipa kokonda ndalama, za ciwelewele, mafilimu a ciwawa, mabuku ndi maseŵela oipa a pa kompyuta. Kukamba zoona, Yehova amatikonda ndipo afuna kutiteteza.
MWAI WAUKULU UMENE TILI NAO
18. Mumamva bwanji mukaganizila cikondi ca Yehova pa inu?
18 Pamene Mose anaganizila zinthu zimene Yehova anam’citila zaka zonse zimene anam’tumikila, anatsimikiza kuti Yehova amam’kondadi. Mose anati: “M’maŵa mutikhutilitse ndi kukoma mtima kwanu kosatha, kuti tifuule mokondwela ndi kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.” (Salimo 90:14) Ndife odalitsidwa cifukwa timakwanitsa kuona ndi kukhulupilila cikondi ca Yehova pa ife. Ndi mwai waukulu kukondedwa ndi Yehova. Ndipo tikumva mmene mtumwi Yohane anamvelela pamene anati: “Taganizilani za cikondi cacikulu cimene Atate watisonyeza.”—1 Yohane 3:1.