“Mukufunika Kupilila”
MAI wina dzina lake Anita, * atabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova, mwamuna wake anayamba kumutsutsa koopsa. Iye anakamba kuti: “Mwamuna wanga anandiletsa kupita kumisonkhano ndipo anandiletsanso ngakhale kuchula dzina la Mulungu. Ndinali kuti ndikachula dzina lakuti Yehova mwamuna wanga anali kukwiya kosaneneka.”
Vuto lina lalikulu limene Anita anakumana nalo linali kuphunzitsa ana ake zokhudza Yehova. Anita anakamba kuti: “Ndinaletsedwa kulambila Yehova m’nyumba muli mwanga. Zinali zosatheka kuphunzitsa ana anga poonekela, kapenanso kupita nao kumisonkhano.”
Zimene zinacitikila Anita zikuonetsa kuti kutsutsidwa ndi anthu a m’banja kumayesa cikhulupililo ca Mkristu. Cikhulupililo ca Mkristu cingayesedwenso ndi matenda osatha, imfa ya mwana wake, kapena mnzake wam’cikwati, kapenanso wacibale wake akasiya kutumikila Yehova. Nanga n’ciani cingathandize Mkristu kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova?
Ngati zotelozo zakucitikilani, kodi mungacite ciani? Mtumwi Paulo anati: “Mukufunika kupilila.” (Aheb. 10:36) Koma n’ciani cingakuthandizeni kupilila?
KUDALILA YEHOVA NDIPONSO KUPEMPHELA
Cinthu cimodzi cofunika kwambili cimene cingatithandize kupilila mayeselo ndi kupemphela kwa Yehova kuti atithandize. Tiyeni tione citsanzo ca mlongo wina dzina lake Ana. Tsiku lina masana pa Mande, banja la Ana linakumana ndi vuto lalikulu. Mwamuna wake amene anakhala naye m’cikwati kwa zaka 30 anamwalila mwadzidzi ali kunchito. Iye anadandaula kuti: “Mwamuna wanga atapita kunchito sanabwelelenso kunyumba, ndipo iye anali ndi zaka 52 cabe.”
Kodi cinathandiza Ana kupilila n’ciani? Ana anapitiliza kugwila nchito imene inamuthandiza kupilila cifukwa nchitoyo inali kumutangwanitsa kwambili. Komabe nchitoyo sinathetse cisoni cimene anali naco. Ana anakamba kuti: “Ndinakhuthulila Yehova nkhawa zanga zonse ndi kumucondelela kuti andithandize kupilila cisoni cacikulu cimene ndinali naco.” Kodi Yehova anayankha pemphelo lake? Inde! Anayankha. Ana anati: “Mtendele wa mumtima wocokela kwa Mulungu unakhazika maganizo anga pansi. Ndipo sindikukaikila ngakhale pang’ono kuti Yehova adzaukitsa mwamuna wanga.”—Afil. 4:6, 7.
“Wakumva pemphelo” walonjeza atumiki ake kuti adzawapatsa ciliconse cimene akufuna kuti akhalebe okhulupilika kwa iye. (Sal. 65:2) Kodi inuyo simukuvomeleza kuti lonjezoli ndi lolimbitsa cikhulupililo? Zoonadi, lonjezo limeneli likutsimikizila kuti nanunso mungapilile.
MISONKHANO YACIKRISTU IMATITHANDIZA KWAMBILI
Yehova wakhala akuthandiza anthu ake kupilila kupyolela mu mpingo wacikristu. Mwacitsanzo, panthawi imene Akristu a ku Tesalonika anali kuzunzidwa, Paulo anawalimbikitsa kuti: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukucitila.” (1 Ates. 2:14; 5:11) Akristu a ku Tesalonika amenewa anapilila cizunzo cifukwa anali kugwilizana kwambili, kukondana, ndi kuthandizana. Akristu amenewa ndi citsanzo cabwino kwambili kwa ife cifukwa anasonyeza zimene zingatithandize kupilila.
Kukhala paubwenzi wabwino kwambili ndi anthu a mumpingo kungatithandize kugaŵana zinthu ‘zolimbikitsa.’ (Aroma 14:19) Izi n’zofunika kwambili makamaka panthawi ya mavuto. Paulo anakumana ndi mavuto ambili, koma Yehova anamupatsa mphamvu kuti apilile. Nthawi zambili, Mulungu anali kumulimbikitsa kudzela mwa Akristu anzake. Mwacitsanzo, pamene Paulo anatumiza moni kwa Akristu a ku Kolose, iye anakamba kuti “amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa” kwambili. (Akol. 4:10, 11) Cikondi cimene Akristuwo anali naco kwa Paulo cinali kuwasonkhezela kumutonthoza ndi kumulimbikitsa pakafunika kutelo. Mofanana ndi Paulo, mwina inunso mwalimbikitsidwapo ndi abale ndi alongo a mumpingo wanu.
THANDIZO LOCOKELA KWA AKULU
Yehova wapeleka akulu mumpingo wacikristu amene angatithandize kupilila. Amuna okhwima mwa kuuzimu amenewa angakhale “malo obisalilapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” (Yes. 32:2) Zimenezi ndi zolimbikitsa kwambili. Kodi inuyo mumawafikila akulu mukakhala ndi vuto? Cilimbikitso cimene akulu amapeleka cingakuthandizeni kupilila.
Akulu sacita zinthu mozizwitsa. Iwo ndi opanda ungwilo ‘okhala ndi zofooka ngati ifeyo.’ (Mac. 14:15) Ngakhale n’telo, mapembedzelo ao angacite zazikulu. (Yak. 5:14, 15) Mwacitsanzo, m’bale wina wa ku Italy amene wapilila matenda osacilitsika amene amamufooketsa ndi kumuwondetsa anati: “Cikondi cimene akulu amandionetsa pondicezela kaŵilikaŵili cimandilimbikitsa kupilila.” Kodi inuyo mumayamikila mphatso imene Yehova wakupatsani omwe ndi akulu?
MUZICITA ZINTHU ZAKUUZIMU NTHAWI ZONSE
Palinso zinthu zina zimene tingacite kuti tipilile. Cimodzi mwa zinthu zimenezi ndi kucita zinthu zakuuzimu nthawi zonse. Ganizilani citsanzo ca John wa zaka 39, amene anapezeka ndi khansa yoopsa kwambili. Iye anati: ‘Ndinaona ngati a dokotala andinamiza cifukwa ndinali wacinyamata.’ Panthawiyo mwana wa John anali ndi zaka zitatu cabe. John anapitiliza kuti, “Izi zinapangitsa kuti mkazi wanga azisamalila mwana wathu komanso ineyo ndiponso kundipelekeza kukaonana ndi dokotala.” Mankhwala amene John anali kumwa a khansa anali kumucititsa kuti azikhala otopa ndi kumva mseru. Kuonjezela apo, abambo ake a John anadwala matenda aakulu ndipo anafunika cisamalilo ca banja.
Kodi n’ciani cinathandiza John ndi banja lake kupilila panthawi yovuta imeneyi? John anati: “Mosasamala kanthu za vuto langa, ndinali kuonetsetsa kuti ineyo ndi banja langa tikucita zinthu za kuuzimu nthawi zonse. Tinali kupezeka pamisonkhano yonse, kulalikila mlungu uliwonse, ndi kucita Kulambila kwa Pabanja ngakhale kuti kucita zimenezi kunali kovuta.” John anaona kuti cimene cingathandize munthu kupilila mavuto ndi kukhala wolimba mwa kuuzimu. Kodi John anapeleka cilimbikitso cotani kwa anthu amene akulimbana ndi mavuto? Iye anati: “Pamene maganizo akhala pansi, nkhawa zonse zimaloŵedwa m’malo ndi mphamvu ndiponso cikondi ca Yehova. Conco, nanunso Yehova angakulimbikitseni mmene walimbikitsila ine.”
Sitikukaikila ngankhale pang’ono kuti mwa thandizo la Mulungu tingapilile ziyeso kapena mavuto amene tingakumane nao tsopano kapena mtsogolo. Tiyeni tizidalila Yehova ndi kupemphela kwa iye ndiponso kukhala paubwenzi wolimba ndi abale ndi alongo athu a mumpingo. Pezani cilimbikitso kwa akulu acikristu ndipo yesetsani kucita zinthu zakuuzimu nthawi zonse. Tikacita zonsezi tidzaonetsa kuti tikutsatila mau a mtumwi Paulo akuti, “Mukufunika kupilila.”
^ par. 2 Maina ena asinthidwa.