Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
Kodi mau a Davide pa Salimo 37:25 ndi mau a Yesu pa Mateyu 6:33, atanthauza kuti Yehova sadzalola Mkristu kusoŵa cakudya?
Davide analemba kuti ‘sinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha cakudya.’ Iye anakamba mau amenewa malinga ndi zimene zinam’citikila. Anadziŵa kuti Mulungu amasamalila nthawi zonse. (Sal. 37:25) Komabe, mau a Davide satanthauza kuti wolambila Mulungu sasoŵa zofunikila kapena kuti sadzasoŵapo.
Panali nthawi zina pamene Davide anavutika kwambili. Nthawi ina ndi pamene anali kuthaŵa Sauli. Ndipo zakudya zinam’cepela cakuti anapempha mkate kuti iye ndi anthu ake adye. (1 Sam. 21:1-6) Conco panthawiyo, Davide anali ‘kupemphapempha cakudya.’ (Sal. 37:25) Komabe, panthawi yovuta imeneyo iye anadziŵa kuti Yehova sanamusiye. Zoona zake n’zakuti, palibe pamene timaŵelenga kuti Davide anali wopemphapempha kuti apeze cakudya.
Pa Mateyu 6:33, pali mau a Yesu olimbikitsa akuti Mulungu adzasamalila zosoŵa za atumiki ake okhulupilika amene amaika zinthu za Ufumu patsogolo. Yesu anati: “Pitilizani kufunafuna ufumu coyamba ndi cilungamo cake, ndipo zina zonsezi [kuphatikizapo zakudya, zakumwa, ndi zovala] zidzaonjezedwa kwa inu.” Komabe, Yesu anaonetsanso kuti cifukwa ca cizunzo, “abale” ake angasoŵe cakudya. (Mat. 25:35, 37, 40) Zimenezo zinacitika kwa mtumwi Paulo, amene nthawi zina anasoŵa zakudya ndi zakumwa.—2 Akor. 11:27.
Yehova amatiuza kuti tidzazunzidwa m’njila zosiyanasiyana. Iye angalole kuti tisoŵe zinthu zina kuti tithandizile kuyankha mabodza a Mdyelekezi. (Yobu 2:3-5) Mwacitsanzo, abale athu ena, monga aja amene anaikidwa m’misasa yacibalo ya Nazi, anakumana ndi mavuto aakulu cifukwa ca cizunzo. Anasautsa Mboni mwa kuzipatsa cakudya cosakwanila kuti afooketse cikhulupililo cao. Mboni zokhulupilika zinapitilizabe kumvela Yehova, ndipo iye sanazisiye. Analola kuti ziyesedwe mwanjila imeneyi, monga mmene amalolela Akristu onse kukumana ndi mayeselo osiyanasiyana. Koma sitikaikila kuti Yehova amathandiza onse amene amavutika cifukwa ca dzina lake. (1 Akor. 10:13) Tizikumbukila mau apa Afilipi 1:29 akuti: “Munapatsidwa mwai. Osati mwai wokhulupilila Kristu wokha, komanso wovutika cifukwa ca iye.”
Yehova walonjeza kuti adzakhala ndi atumiki ake. Mwacitsanzo, lemba la Yesaya 54:17 limati: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana.” Lonjezo ili ndi ena ofanana nalo amatitsimikizila kuti anthu a Mulungu adzatetezedwa monga gulu. Koma Mkristu payekha angakumane ndi mayeselo, ndipo ngakhale kuphedwa kumene.