MBILI YANGA
N’natsimikiza Mtima Kuti Sinidzabwelela M’mbuyo
“ADADI,” “ABABA,” “MALUME.” Umu ni mmene acicepele ambili pa Beteli amanichulila kaŵili-kaŵili. Ndipo popeza ndine wacikulile wa zaka 89, nimakondwela akamanichula mwanjila imeneyi. Nimaona mau acikondi amenewo monga mbali ya madalitso amene Yehova wanipatsa cifukwa com’tumikila kwa zaka 72 mu utumiki wanthawi zonse. Ndipo cifukwa ca zimene naona mu utumikiwu, nimalimbikitsa acicepele amenewa na mtima wonse kuti ‘asagwe ulesi, pakuti adzapeza mphoto cifukwa ca nchito yawo.’—2 Mbiri 15:7.
ABALE ANGA
Makolo anga anacoka ku Ukraine na kukakhala ku Canada. Iwo anakakhala m’tauni ya Rossburn, ku Manitoba. Amayi anabala ana 16, anyamata 8 na atsikana 8, ndipo panalibe amphundu. Ine n’nali wa namba 14. Atate anali kuikonda Baibo moti anali kutiŵelengela m’maŵa mulimonse pa Sondo. Koma anali kuona kuti cipembedzo ni njila yacinyengo yotengela ndalama kwa anthu. Ndipo nthawi zambili moseka anali kukamba kuti, ‘Kaya anali kulipila Yesu n’ndani pa nchito yake yolalikila na kupanga ophunzila?”
Abale anga 8, amuna 4 na akazi 4, m’kupita kwa nthawi anaphunzila coonadi. Mlongosi wanga Rose anatumikila monga mpainiya, mpaka pamene anamwalila. Kwa masiku angapo asanamwalile, iye anali kutilimbikitsa tonse kuti tizimvela na kucita zimene Mau a Mulungu amakamba. Anali kukamba kuti, “Nifuna tikaonane m’dziko latsopano.” Mkulu wanga Ted, poyamba anali kulalikila za moto wa helo. M’maŵa uliwonse pa Sondo, anali kulalikila pa wailesi. Anali kuyofyeza anthu mwa kuwauza kuti ocimwa adzashokewa kwamuyaya m’moto wosatha ku helo. Koma m’kupita kwa nthawi, iyenso anakhala mtumiki wa Yehova wokhulupilika ndi wacangu.
MMENE N’NAYAMBILA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
Tsiku lina mu June 1944, n’tabwela kucokela ku sukulu, n’napeza kabuku pa thebulo m’cipinda codyela. Kanali na mutu wakuti The Coming World Regeneration (Dziko Lokonzedwanso Limene Likubwela). * N’naŵelenga peji yoyamba, kenako yaciŵili, ndipo sin’naleke kuŵelenga mpaka kukatsiliza konse. N’tatsiliza, n’napanga ciganizo cakuti niyamba kutumikila Yehova monga mmene Yesu anacitila.
Kodi n’ndani anabweletsa kabuku kameneko? Mkulu wanga Steve anakamba kuti amuna aŵili “ogulitsa” mabuku anafika pa nyumba pathu. Iye anati: “Nagulako kabuku kameneka, cifukwa kanali
kochipa.” Wiki yotsatila pa Sondo, anthu aja anabwelanso. Iwo anatiuza kuti ni a Mboni za Yehova na kuti amaseŵenzetsa Baibo poyankha mafunso amene anthu amakhala nawo. Izi zinatikondweletsa cifukwa makolo athu anatiphunzitsa kulemekeza Mau a Mulungu. A Mboniwo anatiuzanso kuti posacedwa adzakhala na msonkhano waukulu ku Winnipeg, kumene mlongosi wanga Elsie anali kukhala. N’naganiza zokapezekapo pamsonkhanowo.N’nayenda msenga wa makilomita pafupi-fupi 320 na njinga kupita ku Winnipeg. Koma n’naimako m’tauni ya Kelwood, kumene kunali kukhala amuna aŵili aja a Mboni amene anabwela ku nyumba kwathu. Nili kumeneko, n’napezekapo pa msonkhano wa mpingo, ndipo apa m’pamene n’nadziŵa kuti mpingo n’ciani. N’nazindikilanso kuti aliyense, kaya akhale mwamuna, mkazi, kapena wacicepele ayenela kumalalikila ku nyumba na nyumba mmene Yesu anali kucitila.
Ku Winnipeg, n’nakumana na mkulu wanga Jack, amenenso anabwela ku msonkhano kucokela ku Ontario. Pa tsiku loyamba la msonkhanowo, m’bale analengeza kuti kudzakhala ubatizo. Ine na Jack tinaganiza zobatizika pa msonkhanowo. Tonse tinapanga ciganizo coyamba kutumikila monga apainiya tikangobatizika. Titangocoka ku msonkhanowo, Jack anayamba upainiya. Pa nthawiyo n’nali na zaka 16. Conco n’nabwelela ku sukulu. Koma caka cotsatila, na ine n’nayamba upainiya wa nthawi zonse.
N’NAPHUNZILA ZAMBILI PAMENE N’NALI KUCITA UPAINIYA
N’nayamba kutumikila monga mpainiya pamodzi na Stan Nicolson m’tauni ya Souris, ku Manitoba. Posapita nthawi, n’nazindikila kuti kucita upainiya si kopepuka nthawi zonse. Ndalama zimene tinali nazo zinali kucepela-cepela, koma sitinaleke kulalikila. Nthawi ina pambuyo polalikila kwa tsiku lonse, tinafika pa nyumba tilibiletu olo ngwee, komanso titafa na njala. Zinali zokondweletsa cotani nanga kupeza saka yaikulu ya zakudya pa khomo la nyumba yathu. Mpaka lomba, sitidziŵa amene anaikapo sakayo. Madzulo amenewo, tinadya bwino monga mabwana. Tinadalitsidwa kwambili cifukwa cosabwelela m’mbuyo pa utumiki wathu. Ndipo mwezi umenewo, m’malo moyonda, n’nainilako.
Patapita miyezi ingapo, tinauzidwa kuti tikatumikile m’tauni ya Gilbert Plains, imene inali pa msenga wa makilomita 240 kumpoto kwa tauni ya Souris. M’masiku amenewo, mpingo uliwonse unali kukhala na chati yaikulu ku pulatifomu, yoonetsa zimene mpingo wacita mwezi uliwonse pa nchito yolalikila. Mwezi wina n’taona kuti nchito za mpingo zatsika, n’nakamba nkhani mwamphamvu yolimbikitsa abale na alongo kuti awongolele. Pambuyo pa msonkhanowo, mlongo wina wacikulile amene anali mpainiya, komanso amene mwamuna wake sanali Mboni, anabwela kwa ine misozi ikunjelama m’maso noniuza kuti, “N’nayesetsa ndithu, koma apa m’pamene mphamvu zanga zinapelela.” Izi zinanikhudza kwambili cakuti na ine n’nagwetsa misozi, ndipo n’nawapepesa.
Monga mmene ine n’nacitila, abale acinyamata angalakwitse zinthu zina n’kuyamba kudziimba mlandu kwambili. Koma nazindikila kuti m’malo mobwelela m’mbuyo tikalakwitsa, ni bwino kuphunzilapo kanthu pa zimene talakwitsazo. Tikapitiliza kutumikila mokhulupilika, Yehova adzatidalitsa.
NKHONDO YA KU QUEBEC
Nili na zaka 21, n’nakhala na mwayi waukulu woloŵa kilasi ya namba 14 ya Sukulu ya Gileadi. Tinatsiliza maphunzilo athu mu February 1950. Ophunzila pafupi-fupi 25 a m’kilasi yathu anatumizidwa ku cigawo ca Quebec ku Canada, kumene kuli anthu okamba Cifulenchi. Pa nthawiyo, Mboni zinali kuzunzidwa kwambili kumeneko. Ine n’nauzidwa kuti nikatumikile ku Val-d’Or, tauni imene kuli migodi ya golide. Tsiku lina kagulu kathu kanapita kukalalikila ku mudzi winawake wapafupi, wochedwa Val-Senneville. Wansembe wa ku delalo anatiyofyeza kuti adzatimenya ngati sitidzacoka m’mudziwo mwamsanga. N’napita kukhoti kukam’gulila saimoni wansembeyo cifukwa cotiyofyeza mwanjila imeneyi. Pamapeto pake, wansembeyo anamulipilitsa. *
Cocitika cimeneci na zina zambili zinakhala mbali ya cimene tingati “Nkhondo ya ku Quebec.” Cigawo ca Quebec cinali kulamulidwa na chechi ya Katolika
kwa zaka zoposa 300. Atsogoleli acipembedzo na andale anali kuzunza Mboni za Yehova. Inali nthawi yovuta, ndipo tinali ocepa. Koma sitinabwelele m’mbuyo. Anthu oona mtima a ku Quebec anali kulabadila coonadi. Mwacitsanzo, n’nali na mwayi wophunzila Baibo na anthu angapo, amene pambuyo pake anakhala Mboni. N’nalinso na mwayi wophunzila Baibo na banja la anthu 10. M’kupita kwa nthawi, banja lonse linayamba kutumikila Yehova. Kulimba mtima kwawo kunalimbikitsa ena kucoka m’cipembedzo ca Katolika. Tinapitilizabe kulalikila, ndipo pothela pake tinapambana nkhondoyo.KUPHUNZITSA ABALE M’CITUNDU CAWO
Mu 1956, n’napemphedwa kukatumikila ku dziko la Haiti. Amishonale ambili atsopano kumeneko anali kulephela kukamba Cifulenchi. Koma anthu anali acidwi. M’mishonale wina, dzina lake Stanley Boggus anakamba kuti, “Tinacita cidwi kuona kuti anthu anali kuyesetsa kutiphunzitsa Cifulenchi.” Poyamba sizinali zovuta kwa ine cifukwa n’nali n’taphunzilako Cifulenchi pamene n’nali ku Quebec. Koma pasanapite nthawi itali, n’nazindikila kuti abale ambili a kumeneko anali kukamba cabe Cikiliyo. Conco kuti ise amishonale tizilalikila mogwila mtima, tinaphunzila citundu cimeneco. Ndipo Mulungu anatidalitsa cifukwa ca khama lathu.
Pofuna kuthandiza abale a kumeneko mowonjezeleka, Bungwe Lolamulila linativomeleza kuyamba kumasulila Nsanja ya Mlonda na zofalitsa zina m’Cikiliyo ca ku Haiti. Zotulukapo zake, mwamsanga ciŵelengelo ca opezeka pa misonkhano cinawonjezeka m’dziko lonselo. Mu 1950, ku Haiti kunali ofalitsa 99, koma pofika caka ca 1960, ciŵelengeloci cinawonjezeka kupitilila pa 800. Pa nthawiyo, n’nauzidwa kuti nikatumikile pa Beteli. Mu 1961, n’nali na mwayi wokhala mmodzi wa alangizi pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Tinaphunzitsa akulu na apainiya apadela okwana 40. Pa msonkhano wacigawo wa mu January 1962, tinalimbikitsa abale a kumeneko kuwonjezela zocita mu utumiki wawo. Ndipo ena a iwo anaikidwa kukhala apainiya apadela. Kucita izi kunali kothandiza ngako cifukwa citsutso cinali pafupi kuyamba.
Pa January 23, 1962, titangotsiliza msonkhano wa cigawo, ine na mmishonale wina dzina lake Andrew D’Amico tinagwidwa na apolisi tili ku ofesi ya nthambi. Ndipo anatilanda magazini onse a Galamukani! ya January 8, 1962 (a m’Cifulenchi) amene tinali nawo. Anacita izi cifukwa cakuti magaziniyo * Koma abale a m’dzikolo anapitilizabe kutumikila Yehova modzipeleka kwambili. Masiku ano, nimakondwela nikaganizila kupilila kumene anaonetsa na kupita kwawo patsogolo mwauzimu. Iwo lomba ali na Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Cikiliyo ca ku Haiti. Kalelo zinali kuoneka monga zosatheka kukhala na Baibo imeneyi m’citundu cimeneci.
inagwila mau nyuzipepa inayake ya Cifulenchi, imene inakamba kuti anthu a ku Haiti amacita zamizimu. Anthu ena sanakondwele na nkhaniyi, ndipo anakamba kuti nkhaniyo tinailembela pa ofesi yathu ya nthambi. Patapita mawiki angapo, amishonale onse anawacotsa m’dzikolo nowatumiza kumaiko awo.KUGWILA NCHITO YOMANGA KU CENTRAL AFRICAN REPUBLIC
Pambuyo potumikila ku Haiti, n’natumizidwa ku Central African Republic kuti nikatumikile monga mmishonale. Nili kumeneko, n’natumikilakonso monga woyang’anila woyendela komanso monga woyang’anila nthambi.
M’masiku amenewo, Nyumba za Ufumu zambili zinali zosaoneka bwino. N’naphunzila kumweta udzu na kuvika Nyumba za Ufumu. Anthu opita na njila akaniona ine mzungu nikugwila nchitoyi, anali kudabwa kwambili. Kucita izi kunalimbikitsanso abale kukhala odzipeleka kwambili pa nchito yomanga na kukonzanso Nyumba zawo za Ufumu. Atsogoleli azipembedzo anali kutiseka poona kuti Nyumba zathu za Ufumu zinali zamaudzu, pamene machechi awo anali a malata. Izi sizinatigwetse ulesi. Tinapitilizabe kusonkhana m’Nyumba za Ufumu za mitenje ya udzu. Iwo analeka kutiseka pamene cimphepo camkuntho cinaomba dela lonse la Bangui, likulu la dzikolo. Cimphepoco cinavumbula mtenje wa imodzi mwa machechiwo na kukautaya mu msewu waukulu. Koma mitenje ya Nyumba zathu za Ufumu siinavumbuke. Kuti nchito ya Ufumu iziyang’anilidwa bwino, tinamanga ofesi ya nthambi yatsopano na nyumba ya amishonale m’miyezi 5 cabe. *
N’NAKWATILA MKAZI WACANGU
Mu 1976, nchito ya Ufumu inaletsedwa mu Central African Republic, ndipo ine n’natumizidwa kuti nikatumikile ku N’Djamena, likulu la dziko la Chad. Kumeneko, n’nakondwela kukumana ndi Happy, mpainiya wapadela wacangu wocokela ku Cameroon. Tinakwatilana pa April 1, 1978. M’mwezi umenewo, m’dzikolo munabuka nkhondo. Conco ise na anthu ena ambili tinathaŵila kum’mwela kwa dzikolo. Pamene nkhondo inasila, tinabwelela kwathu, koma tinapeza kuti nyumba yathu anaisandutsa malo okhala asilikali. Tinapezanso kuti zonse atitengela—mabuku, weding’i diresi ya Happy komanso mphatso zimene tinalandila pa cikwati. Koma izi sizinatibweze m’mbuyo. Ubwino wake tonse tinali moyo, ndipo tinali okonzeka kuwonjezela zocita mu utumiki wathu.
Patapita zaka ziŵili, ciletso pa nchito yathu ku Central African Republic cinacotsedwa. Tinabwelela m’dzikolo ndipo ine n’nayamba kutumikila monga woyang’anila woyendela. Nyumba yathu inali motoka. Mkati munali bedi, dilamu yaikulu yokwana malita 200 a madzi, filiji, na stovu ya gasi. Ulendo unali kukhala wovuta. Tsiku lina tili pa ulendo, tinaimitsidwa na apolisi pa malodi buloko oposa 117.
Nthawi zambili kunali kutentha kwambili kufika pa madigiri 50. Nthawi zina pa misonkhano ya dela zinali zovuta kupeza madzi okwanila a ubatizo. Conco abale anali kukumba m’mitsinje youma kuti apeze madzi. Ndipo pang’ono m’pang’ono anali kupeza madzi okwanila. Nthawi zambili anthu anali kuwabatizila m’dilamu.
N’NATUMIKILANSO M’MAIKO ENA A KU AFRICA
Mu 1980 tinasamutsidwila ku Nigeria. Kumeneko, kwa zaka ziŵili na hafu tinathandiza pa nchito yokonzekela kumanga ofesi ya nthambi yatsopano. Abale anagula cinyumba cosungilamo katundu ca nsanjika ziŵili, cimene cinafunika kupasulidwa kuti akamange ofesi ya nthambi. Tsiku lina m’maŵa, n’nakwela pamwamba pa cinyumbaco kuti nithandize pa nchito yopasula. Cakumasana, n’nayamba kuseluka kupitila kumene n’nakwelela. Koma sin’nadziŵe kuti zinthu zina zimene n’naponda pokwela zinali zitagwa pamene tinali kukasula. Conco, poseluka n’naphonya kuponda n’kugwa mpaka pansi. Zinaoneka monga
nadzicita kwambili, koma adokota ataniona na kunipima pa eksileyi, anauza mkazi wanga kuti: “Musade nkhawa. Angodzicita pang’ono, ndipo wiki ino kapena ya maŵa adzakhala bwino.”Mu 1986 tinapita ku Côte d’Ivoire, kumene n’nayamba kutumikila monga woyang’anila woyendela. Pocita utumikiwu, tinali kukafika mpaka ku Burkina Faso. Sin’nali kudziŵa kuti m’tsogolo, tidzakhala ku Burkina Faso kwa zaka ndithu.
N’nacoka ku Canada mu 1956. Koma mu 2003, pambuyo pa zaka 47, n’nabwelela ku Canada na kuyamba kutumikila pa nthambi. Panthawiyi n’nali na mkazi wanga Happy. Tinali nzika za dziko la Canada, koma tinali kudziona monga a ku Africa.
Mu 2007, nili na zaka 79 n’nabwelelanso ku Africa. Pa nthawiyi, tinatumizidwa ku Burkina Faso. Kumeneko, n’nayamba kutumikila monga mmodzi wa abale a m’Komiti ya Nthambi. M’kupita kwa nthawi, ofesi ya nthambi ya kumeneko anaisandutsa ofesi yomasulila mabuku, ndipo inayamba kuyang’anilidwa na nthambi ya ku Benin. Mu August 2013, tinauzidwa kuti tikatumikile ku Beteli ya ku Benin.
Olo kuti thanzi yanga siili bwino kweni-kweni, nchito yolalikila nimaikonda kwambili. M’zaka zitatu zapitazi, n’nali na mwayi woona maphunzilo anga a Baibo aŵili, Gédéon na Frégis, akubatizika. Izi zinatheka mwa thandizo la akulu na mkazi wanga. Pali pano, Gédéon na Frégis akutumikila Yehova mwacangu.
Posacedwapa, cifukwa ca mmene thanzi yanga ilili, ine na mkazi wanga tinatumizidwa ku nthambi ya ku South Africa, kumene banja la Beteli likunisamalila mwacikondi. Dziko la South Africa ni la namba 7 pa maiko a mu Africa amene natumikilako. Ndiyeno mu October 2017, tinakhala na mwayi waukulu wokapezeka pa mwambo wopatulila likulu lathu la padziko lonse ku Warwick, mu mzinda wa New York. Ndithudi! Ici cinali cocitika cosaiŵalika kwa ise.
Buku la Cizungu la Yearbook la mu 1994, pa peji 255 limati: “Onse amene apilila pa nchitoyi kwa zaka zambili, tikuwalimbikitsa kuti: ‘Khalani olimba mtima ndipo musagwe ulesi, pakuti mudzapeza mphoto cifukwa ca nchito yanu.’—2 Mbiri 15:7.” Ine na mkazi wanga Happy, ndise otsimikiza mtima kutsatilabe malangizo amenewa na kulimbikitsanso ena kucita cimodzi-modzi.
^ par. 9 Kofalitsidwa na Mboni za Yehova mu 1944, koma lomba analeka kukapulinta.
^ par. 18 Onani nkhani yakuti “Quebec Priest Convicted for Attack on Jehovah’s Witnesses” (Wansembe wa ku Quebec Apezeka ndi Mlandu Cifukwa Coopseza Mboni za Yehova), mu Galamukani! ya Cizungu ya November 8, 1953, mape. 3-5.
^ par. 23 Nkhaniyi inafotokozedwa bwino m’buku la Cizungu la Yearbook of Jehovah’s Witnesses la mu 1994, mape. 148-150.
^ par. 26 Onani nkhani yakuti “Building on a Solid Foundation” (Kumanga pa Maziko Olimba) mu Galamukani! ya Cizungu ya May 8, 1966, peji 27.