Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 44

NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako

Zimene Zingatithandize Kupilila Zopanda Cilungamo

Zimene Zingatithandize Kupilila Zopanda Cilungamo

“Musalole kuti coipa cikugonjetseni, koma pitilizani kugonjetsa coipa pocita cabwino.”AROMA 12:21.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene zingatithandize kupilila zopanda cilungamo m’njila imene ingapangitse kuti zinthu zisaipileko.

1-2. Kodi tingacitilidwe zinthu zopanda cilungamo m’njila ziti?

 YESU anakamba fanizo la mkazi wamasiye amene mobweleza-bweleza anapempha woweluza kuti amuthandize. Anali kupempha thandizo cifukwa munthu wina wake anali kumucitila zopanda cilungamo. Mosakaikila, ophunzila ambili a Yesu inawafika pamtima nkhaniyi, cifukwa panthawiyo anthu wamba nthawi zambili anali kucitidwa zopanda cilungamo. (Luka 18:​1-5) Tingamvetse mmene mkazi wa m’fanizolo anamvela cifukwa tonsefe panthawi ina tinacitidwapo zopanda cilungamo.

2 Lelolino m’dzikoli, zinthu monga tsankho, kukhala osakoma mtima, komanso kupondelezana, n’zofala kwambili. Ndiye cifukwa cake sitidabwa tikacitidwa zopanda cilungamo. (Mlal. 5:8) Ndipo zingakhale zokhumudwitsa kwambili ngati m’bale kapena mlongo ndiye waticitila zinthu mopanda cilungamo. Komabe mosiyana na anthu amene amatitsutsa kapena kutizunza, abale na alongo athu si adani a coonadi. Iwo angaticitile zinthu mopanda cilungamo cifukwa ni opanda ungwilo. Tingaphunzile zambili poona mmene Yesu anacitila pamene anacitilidwa zinthu mopanda cilungamo na anthu otsutsa. Ngati timakwanitsa kucita zinthu moleza mtima anthu otitsutsa akaticita zopanda cilungamo, ndiye kuti tiyenela kukhala oleza mtima kwambili na okhulupilila anzathu! Kodi Yehova amamva bwanji Akhristu anzathu kapena anthu amene si mboni akaticita zopanda cilungamo? Kodi amasamala?

3. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amasamala ena akaticita zopanda cilungamo?

3 Yehova amasamala kwambili za mmene anthu amacitila nafe zinthu. “Yehova amakonda cilungamo.” (Sal. 37:28) Yesu anatitsimikizila kuti Yehova ‘adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika . . . mwamsanga’ panthawi yake yoyenela. (Luka 18:​7, 8) Posacedwa, iye adzacotsapo mavuto onse komanso kupanda cilungamo kwa mtundu uliwonse.—Sal. 72:​1, 2.

4. Kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano?

4 Tikuyembekezela nthawi pamene Yehova adzacotsapo mavuto onse amene amabwela cifukwa ca zopanda cilungamo. Koma pali pano, iye amatithandiza kupilila tikacitidwa zopanda cilungamo. (2 Pet. 3:13) Mwacitsanzo, iye amatiphunzitsa mmene tingacitile zinthu mwanzelu kuti tisaonjezele mavuto, anthu ena akaticitila zopanda cilungamo. Amacita izi mwa kutionetsa mmene Mwana wake anacitila zinthu pamene anacitidwa zopanda cilungamo. Amatipatsanso malangizo othandiza amene tingaseŵenzetse tikacitidwa zopanda cilungamo.

CITANI ZINTHU MWANZELU MUKACITIDWA ZOPANDA CILUNGAMO

5. N’cifukwa ciyani tiyenela kucita zinthu mosamala tikacitidwa zopanda cilungamo?

5 Anthu ena akaticita zopanda cilungamo, tingakhumudwe kwambili kapena kuvutika maganizo. (Mlal. 7:7) Atumiki okhulupilika, monga Yobu na Habakuku, nawonso anamvapo mwa njila imeneyi. (Yobu 6:​2, 3; Hab. 1:​1-3) M’pomveka kumva conco. Ngakhale n’telo, tiyenela kukhala osamala kuti tisacite zolakwika.

6. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Abisalomu? (Onaninso cithunzi.)

6 Munthu wina akaticitila zopanda cilungamo tingafune kumubwezela, koma kucita zimenezi kungaonjezele mavuto. Onani zimene Abisalomu mwana wa Mfumu Davide anacita. Iye anakwiya kwambili pamene m’bale wake Aminoni anagwilila mlongo wawo Tamara. Malinga na Cilamulo ca Mose, Aminoni anayenela kuphedwa cifukwa ca zimene anacita. (Lev. 20:17) M’pomveka kuti Abisalomu anakwiya, koma iye analakwa kupha Aminoni.—2 Sam. 13:​20-23, 28, 29.

Tamara atagwililidwa, Abisalomu analephela kulamulila mkwiyo wake (Onani ndime 6)


7. Kodi zopanda cilungamo zinakhudza bwanji maganizo a wamasalimo wina kwa kanthawi?

7 Tikaona kuti anthu amene amacita zopanda cilungamo sakulandila cilango, tingayambe kuganiza kuti kucita zoyenela kulibe phindu. Wamasalimo wina anaona kuti anthu oipa zinthu zinali kuwayendela bwino ndipo anali kupondeleza anthu olungama. Iye anati: “Izi nʼzimene oipa amacita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.” (Sal. 73:12) Wamasalimoyu anakhumudwa kwambili cifukwa ca zopanda cilungamo zimene anaona, moti anayamba kuganiza kuti kutumikila Yehova kulibe phindu. Anafika pokamba kuti: “Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi, zinali zopweteka kwa ine.” (Sal. 73:​14, 16) Iye anavomeleza kuti: “Koma ine mapazi anga anangotsala pang’ono kusocela, mapazi anga anangotsala pang’ono kuteleleka.” (Sal. 73:2) Zofanana na zimenezi zinacitikila m’bale wina amene tangomuchula kuti Alberto.

8. Kodi zopanda cilungamo zinam’khudza bwanji m’bale wina?

8 Alberto ananamizilidwa kuti anali kuba ndalama za mpingo. Cifukwa ca zimenezi anamutsitsa paudindo, ndipo ambili amene anamva za nkhani imeneyi mumpingo analeka kumulemekeza. Iye anati: “Zimenezi zinanikwiyitsa kwambili ndipo n’nakhumudwa.” M’baleyu anakwiya kwambili, moti analeka kusonkhana ndipo anakhala wozilala kwa zaka 5. Cocitikaci cionetsa zimene zingacitike ngati talola mkwiyo kutilamulila tikacitidwa zopanda cilungamo.

TENGELANI CITSANZO CA YESU MUKACITIDWA ZOPANDA CILUNGAMO

9. Ni zopanda cilungamo ziti zimene Yesu anapilila? (Onaninso cithunzi.)

9 Yesu anatipatsa citsanzo cabwino ca zimene tingacite kuti tipilile zopanda cilungamo. Yesu anacitilidwapo zopanda cilungamo kucokela kwa acibale ake, komanso kwa anthu amene sanali acibale ake. Acibale ake amene sanamukhulupilile anakamba kuti wacita misala. Nawonso atsogoleli acipembedzo anakamba kuti iye anatenga mphamvu zake kwa ziŵanda. Kuwonjezela apo, asilikali Aciroma anamunyoza ndipo anamupha. (Maliko 3:​21, 22; 14:55; 15:​16-20, 35-37) Ngakhale n’telo, Yesu anapilila zopanda cilungamo zonse zimene anamucitila, ndipo sanabwezele. Tiphunzilapo ciyani ku citsanzo cake?

Yesu anatisiyila citsanzo cabwino ca mmene tingacitile tikacitidwa zopanda cilungamo (Onani ndime 9-10)


10. Kodi Yesu anacita ciyani atacitidwa zopanda cilungamo? (1 Petulo 2:​21-23)

10 Ŵelengani 1 Petulo 2:​21-23. a Yesu anatisiyila citsanzo cabwino kwambili cimene tingatsatile tikamakumana na zopanda cilungamo. Anali kudziŵa nthawi yolankhula komanso yokhala cete. (Mat. 26:​62-64) Nthawi zina, anthu ena akamunenela mabodza iye anali kukhala cete. (Mat. 11:19) Ndipo Yesu akalankhula, sanali kuwanyoza anthu omuvutitsa kapena kuwaopseza. Iye anali wodziletsa cifukwa “anasiya zonse mʼmanja mwa Woweluza amene amaweluza mwacilungamo.” Yesu anadziŵa kuti Yehova anali kuona zopanda cilungamo zimene zinali kumucitikila. Iye anali na cikhulupilillo cakuti Yehova adzacotsapo kupanda cilungamo konse panthawi yake.

11. Tingaonetse bwanji kudziletsa m’zokamba zathu? (Onaninso zithunzi.)

11 Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kukhala osamala na zimene timakamba munthu wina akaticitila zopanda cilungamo. Zopanda cilungamo zina zimakhala zazing’ono ndipo tingangozinyalanyaza. Kapena tingangokhala cete kuti tipewe kukamba zinthu zimene zingawonjezele mavuto. (Mlal. 3:7; Yak. 1:​19, 20) Koma nthawi zina tingafunike kulankhula tikaona kuti wina akucitidwa zopanda cilungamo kapena tikafunika kukhalila kumbuyo coonadi. (Mac. 6:​1, 2) Koma tikasankha kulankhula, tifunika kuyesetsa kucita zimenezo mofatsa komanso mwaulemu.—1 Pet. 3:15. b

Tikacitidwa zopanda cilungamo, tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kusankha nthawi imene tingakambe komanso mmene tingakambile (Onani ndime 11-12)


12. Kodi timasiya bwanji zinthu zonse m’manja mwa “Woweluza amene amaweluza mwacilungamo”?

12 Tingatengelenso citsanzo ca Yesu mwa kusiya zonse m’manja mwa “Woweluza amene amaweluza mwacilungamo.” Anthu ena akationa molakwika kapena kuticitila zinthu mopanda cilungamo, timadziŵa kuti Yehova ndiye adziŵa zoona za nkhaniyo. Kukhala na cidalilo cimeneci kungatithandize kupilila tikacitidwa zopanda cilungamo. Timapilila cifukwa tidziŵa kuti panthawi yake Yehova adzakonza zonse. Tikasiya zonse m’manja mwa Yehova, tidzapewa kukwiya kwambili komanso kusungila ena cakukhosi. Kukhala okwiya kungatipangitse kuti ticite zinthu zoipa, kungatilande cimwemwe, ndiponso kungawononge ubale wathu na Yehova.—Sal. 37:8.

13. N’ciyani cingatithandize kupilila zopanda cilungamo moleza mtima?

13 N’zoona kuti sitingakwanitse kutengela citsanzo ca Yesu mosalakwitsa. Nthawi zina tingacite kapena kukamba zinthu zimene pambuyo pake tingadziimbe nazo mlandu. (Yak. 3:2) Ndipo zopanda cilungamo zina zingatipweteke na kutisokoneza maganizo kwa moyo wathu wonse. Ngati umu ni mmene zilili kwa inu, musakaikile kuti Yehova adziŵa zimene mukupitamo. Ndipo Yesu amamvetsa mmene mukumvela cifukwa nayenso anacitidwapo zopanda cilungamo. (Aheb. 4:​15, 16) Kuwonjezela pa citsanzo cabwino kwambili ca Yesu, Yehova amatipatsanso malangizo amene amatithandiza tikakumana na zopanda cilungamo. Tiyeni tsopano tikambilane mavesi aŵili opezeka m’buku la Aroma amene angatithandize.

“SIYILANI MALO MKWIYO WA MULUNGU”

14. Ni motani mmene ‘timasiyila malo mkwiyo wa Mulungu’? (Aroma 12:19)

14 Ŵelengani Aroma 12:19. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti: “Siyilani malo mkwiyo wa Mulungu.” Timasiyila malo mkwiyo wa Yehova mwa kumulola kuti abweletse cilungamo panthawi yake, komanso m’njila imene aona kuti ni yoyenela. M’bale wina dzina lake John anacitilidwa zinthu mopanda cilungamo ndipo anati: “N’nafunika kudziletsa kuti nisacite zolakwika mwa kubwezela. Koma kucita izi kunali kovuta. Lemba la Aroma 12:19 linanithandiza kuti niyembekezele Yehova.”

15. N’cifukwa ciyani n’canzelu kuyembekezela Yehova kuti akonze zinthu?

15 Timapindula tikamayembekezela kuti Yehova akonze zinthu. Tikatelo, tidzapewa kukwiya kwambili kapena kukhumudwa cifukwa coyesa kukonza zinthu patokha. Yehova amafunitsitsa kutithandiza. Zimakhala monga akutiuza kuti, ‘Zopanda cilungamo zikakucitikilani, siyani nkhani imeneyo kwa ine ndipo nidzakonza zinthu panthawi yoyenela.’ Tikakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti “ndidzawabwezela ndine,” timaiŵalako za nkhaniyo tili na cidalilo cakuti adzaisamalila m’njila yabwino koposa. Izi n’zimene zinathandiza John amene tamuchula m’ndime 14. Iye anati: “Nikayembekezela kuti Yehova asamalile nkhaniyi, iye adzaisamalila m’njila yabwino kwambili kuposa mmene ningacitile.”

“PITILIZANI KUGONJETSA COIPA POCITA CABWINO”

16-17 Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kupitiliza “kugonjetsa coipa pocita cabwino”? (Aroma 12:21)

16 Ŵelengani Aroma 12:21. Paulo analimbikitsanso Akhristu kuti: “Pitilizani kugonjetsa coipa pocita cabwino.” Pa ulaliki wake wa pa phili, Yesu anakamba kuti: “Pitilizani kukonda adani anu na kupemphelela amene amakuzunzani.” (Mat. 5:44) Ndipo izi n’zimene iye anacita. Yesu anapilila pamene asilikali Aciroma anamuzunza mwankhanza. Iwo anamukhomelela pa mtengo, kumunyazitsa, komanso kumucita zopanda cilungamo. Sitingamvetse mofikapo zovuta zimene Yesu anakumana nazo.

17 Yesu sanagonje pamene anali kukumana na zopanda cilungamo. M’malo mowafunila zoipa asilikaliwo, iye anapemphela kuti: “Atate, akhululukileni, cifukwa sakudziŵa zimene akucita.” (Luka 23:34) Kupemphelela anthu amene amaticita zopanda cilungamo, kungatithandize kucepetsa mkwiyo wathu komanso kupewa kuwasungila cakukhosi. Kungatithandizenso kusintha mmene timawaonela.

18. Kodi pemphelo linathandiza bwanji Alberto na John kupilila zopanda cilungamo?

18 Pemphelo linathandiza abale aŵili amene tawachula m’nkhani ino kupilila zopanda cilungamo zimene anakumana nazo. Alberto anati: “Ninawapemphelela abale amene ananicitila zopanda cilungamo. Ndipo kangapo konse n’napempha Yehova kuti anithandize kuiŵalako zopanda cilungamo zimene iwo ananicitila.” Tsopano Alberto ali na cimwemwe ndipo anayambanso kutumikila Yehova mokhulupilika. John anakamba kuti: “Nthawi zambili n’nali kumupemphelela m’bale amene ananikhumudwitsa. Mapemphelo amenewo ananithandiza kuti nizimuona moyenela m’baleyo na kupewa kumuweluza. Mapemphelowo ananithandizanso kuti nikhale na mtendele wa mumtima.”

19. Tiyenela kucita ciyani poyembekezela mapeto a dzikoli? (1 Petulo 3:​8, 9)

19 Malinga ngati tikukhala m’dziko loipali, sitingadziŵe zopanda cilungamo zimene zingaticitikile. Mosasamala kanthu za zimene zingaticitikile, tisasiye kupemphela kwa Yehova kuti atithandize. Tizitengelanso citsanzo ca Yesu ca mmene anacitila zinthu anthu ena atamucitila zopanda cilungamo. Tipitilizenso kuseŵenzetsa malangizo othandiza opezeka m’Baibo. Tikatelo, tidzakhala na cidalilo cakuti Yehova adzatidalitsa.—Ŵelengani 1 Petulo 3:​8, 9.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

a M’buku la 1 Petulo caputala 2 na 3, mtumwi Petulo anafotokoza zopanda cilungamo zimene zinali kucitikila Akhristu a m’zaka za zana loyamba. Akapolo anali kucitidwa zopanda cilungamo na ambuye wawo, ndipo akazi a Cikhristu anali kuvutitsidwa na amuna awo osakhulupilila.—1 Pet. 2:​18-20; 3:​1-6, 8, 9.