Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
Ndi liti pamene anthu a Mulungu anakhala akapolo a Babulo Wamkulu?
Ukapolo umenewo unayamba pambuyo pa caka ca 100 C.E., ndipo unatha m’caka ca 1919. N’cifukwa ciani kamvedwe kathu katsopano kameneka n’koyenelela ndiponso kolondola?
Maumboni onse akuonetsa kuti mu 1919, Akristu odzozedwa anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu, ndipo anasonkhanitsidwa mumpingo woyeletsedwa. Ganizilani izi: Kucokela pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila kumwamba m’caka ca 1914, anthu a Mulungu anayesedwa ndipo mwa pang’onopang’ono anayeletsedwa mwakuuzimu. * (Onani mau a munsi.) (Malaki 3:1-4) Kenako, m’caka ca 1919, Yesu anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azipeleka “cakudya pa nthawi yoyenela” kwa anthu a Mulungu. (Mateyu 24:45-47) M’caka cimeneco, anthu a Mulungu anamasulidwa ku ukapolo wophiphilitsila wa Babulo Wamkulu. (Chivumbulutso 18:4) Koma kodi anthu a Mulungu anakhala liti akapolo a Babulo Wamkulu?
Kumbuyoku, tinafotokoza kuti anthu a Mulungu anakhala akapolo a Babulo Wamkulu kwa kanthawi kocepa kuyambila mu 1918. Nsanja ya Olonda ya March 15, 1992, inakamba kuti mofanana ndi mmene Aisiraeli anakhalila akapolo ku Babulo, m’caka ca 1918 atumiki a Yehova anakhala akapolo a Babulo Wamkulu. Koma pambuyo pofufuza moonjezeleka, tazindikila kuti anthu a Mulungu anakhala akapolo kwa zaka zambili cisanafike caka ca 1918.
Ulosi wolembedwa pa Ezekieli 37:1-14 unanenelatu kuti anthu a Mulungu adzakhala akapolo, ndipo pambuyo pake adzamasulidwa. Ezekieli anaona masomphenya a cigwa cimene cinali ndi mafupa okhaokha. Yehova anati: “Mafupawa akuimila nyumba yonse ya Isiraeli.” (Vesi 11) Zimenezi zinali kudzacitikila mtundu wa Isiraeli ndiponso “Isiraeli wa Mulungu,” amene ndi Akristu odzozedwa. (Agalatiya 6:16; Machitidwe 3:21) M’masomphenya amenewo, mafupa anakhala ndi moyo, kenako anakhala gulu lalikulu lankhondo. Zimenezi zinaonetsa mmene anthu a Mulungu anamasulidwila ku ukapolo wa Babulo Wamkulu mu 1919. Koma kodi ulosi umenewu umaonetsa bwanji kuti Akristu oona anali akapolo kwa nthawi yaitali?
Ezekieli 37:2, 11) Zimenezi zikuonetsa kuti anthuwo anali akufa kwa nthawi yaitali. Caciŵili, Ezekieli anaona anthu akufa akukhala ndi moyo mwapang’onopang’ono osati mwadzidzidzi. Iye anamva ‘phokoso la mafupa kuti gobedegobede, ndipo pa nthawiyo mafupawo anali kubwela pamodzi n’kumalumikizana.’ Kenako iye anaona “mitsempha ndi mnofu zitakuta mafupawo.” Ndiyeno, khungu linabwela pamwamba pa mnofu. Pambuyo pake, ‘mpweya unalowa mwa anthuwo, ndipo iwo anakhala ndi moyo.’ Comalizila, anthuwo atakhala ndi moyo, Yehova anawapatsa dziko kuti akhalemo. Kuti zinthu zonsezi zicitike, panafunika kutenga nthawi.—Ezekieli 37:7-10, 14.
Coyamba, Ezekieli anaona mafupa “ouma kwambili” a anthu akufa. (Monga mmene ulosiwu unanenela, Aisiraeli anakhala akapolo kwa nthawi yaitali. Iwo anagwidwa ukapolo m’caka ca 740 B.C.E., pamene mafuko 10 a Aisiraeli amene anali kupanga ufumu wa kumpoto, anagwidwa ukapolo ndi kucoka m’dziko lao. Pambuyo pake, m’caka ca 607 B.C.E., mzinda wa Yerusalemu unaonongedwa ndi Ababulo. Ndipo mafuko aŵili a Aisiraeli, amene anali kupanga ufumu wa kum’mwela wa Ayuda, anagwidwa ukapolo ndi kucoka m’dziko lao. Ndiyeno, mu 537 B.C.E., Aisiraeli anamasulidwa ku ukapolo pamene kagulu kakang’ono ka Ayuda kanabwelela ku Yerusalemu kukamanganso kacisi ndi kulambilanso Yehova.
Conco, mfundo zimenezi zikuonetsa kuti Akristu odzozedwa anali akapolo a Babulo Wamkulu kwa nthawi yaitali, osati cabe kucokela mu 1918 kufika mu 1919. Yesu anali kukamba za nthawi yaitali imeneyi pamene anati Akristu onama, amene ndi namsongole, adzakulila limodzi ndi “ana a Ufumu” amene ndi tiligu. (Mateyu 13:36-43) Pa nthawi yaitali imeneyo, panali Akristu oona ocepa. Ambili a amene anali kudzicha Akristu, anatengela ziphunzitso zonama ndipo anakhala ampatuko. Ndiye cifukwa cake tingakambe kuti mpingo Wacikristu unali kapolo wa Babulo Wamkulu. Ukapolo umenewu unayamba pambuyo pa caka ca 100 C.E., kufikila pamene kacisi wauzimu wa Mulungu anayeletsedwa m’nthawi ya mapeto.—Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3, 6; 1 Yohane 2:18, 19.
M’zaka zambili zimenezo, atsogoleli a machalichi ndiponso olamulila andale anali kufuna kumalamulila anthu. Mwacitsanzo, anthu sanali kuloledwa kukhala ndi Baibulo kapena kuliŵelenga m’cinenelo cimene angamvetsetse mosavuta. Anthu ena amene anali kuŵelenga Baibulo anali kutenthedwa pa mtengo. Ndipo amene anali kutsutsa zimene atsogoleli anali kuphunzitsa, anali kulangidwa mwankhanza. Zinali zovuta kwambili kuti munthu aphunzile coonadi kapena kuti aphunzitse wina.
Masomphenya a Ezekieli asonyeza kuti anthu a Mulungu anakhalanso ndi moyo, ndiponso anamasulidwa ku cipembedzo conama pang’onopang’ono. Kodi zimenezi zinayamba liti kucitika? Nanga zinacitika bwanji? Ezekieli anamvela phokoso lakuti “gobedegobede.” Zimenezi zinayamba kucitika kutatsala zaka mahandeledi ocepa kuti masiku otsiliza ayambe. M’zaka zimenezo, panali anthu ena okhulupilika amene anali kufuna kudziŵa coonadi ndi kutumikila Mulungu ngakhale kuti ziphunzitso zonama zinali zofala. Iwo anali kuphunzila Baibulo ndipo anali kucita zimene angathe kuti auzeko ena zimene anali kuphunzila. Ena anacita khama kumasulila Baibulo m’zinenelo zimene anthu anali kumva mosavuta.
Ndiyeno, kumapeto kwa zaka za m’ma 1800, zinali ngati kuti mnofu ndi khungu zayamba kukuta mafupa. M’bale Charles Taze Russell ndi anzake anacita khama kuti apeze coonadi ca m’Baibulo ndi kutumikila Yehova. Iwo anathandiza anthu ena kumvetsetsa coonadi pogwilitsila nchito magazini a Zion’s Watch Tower ndi zofalitsa zina. M’kupita kwa nthawi, mu 1914, anatulutsa “Sewero la Pakanema la Chilengedwe,” ndipo mu 1917 anatulutsa buku lochedwa The Finished Mystery. Zofalitsa zimenezi zinalimbitsa cikhulupililo ca anthu a Yehova. Kenako mu 1919, zinali ngati kuti anthu a Mulungu akhalanso amoyo ndipo apatsidwa dziko latsopano. Kucokela pamenepo, anthu amene ali ndi ciyembekezo cokhala padziko lapansi kwamuyaya agwilizana ndi Akristu odzozedwa. Onsewa amalambila Yehova mogwilizana ndipo apanga “khamu lalikulu la gulu lankhondo.”—Ezekieli 37:10; Zekariya 8:20-23. *—Onani mau a munsi.
Cotelo, n’zoonekelatu kuti anthu a Mulungu anakhala akapolo a Babulo Wamkulu pambuyo pa caka ca 100 C.E. Panthawi imeneyo, ambili anakhala ampatuko mwa kutsatila ziphunzitso za zipembedzo zonama ndi kukana coonadi. Kwa zaka zambili, cinali covuta kuti anthu atumikile Yehova monga mmene cinalili covuta kwa Aisiraeli pamene anali akapolo. Koma masiku ano, coonadi cikulalikidwa kwa aliyense. Ndife osangalala kwambili kuti tikukhala m’nthawi imene ‘anthu ozindikila awala’ kwambili. Masiku ano, anthu ambili ‘adziyeletsa’ ndi ‘kuyengedwa’ ndipo ayamba kulambila koona.—Danieli 12:3, 10.
Pamene Satana anali kuyesa Yesu, kodi anamutenga ndi kupita naye ku kacisi, kapena anangomuonetsa kacisiyo m’masomphenya?
Sitidziŵa bwinobwino mmene Satana anaonetsela Yesu kacisi.
Olemba Baibulo Mateyu ndi Luka analemba zimene zinacitika. Mateyu analemba kuti ‘Mdyelekezi anatenga’ Yesu ndi kupita naye ku Yerusalemu, ndipo “anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kacisi.” (Mateyu 4:5) Luka analemba kuti Mdyelekezi “anamutengela ku Yerusalemu, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kacisi.”—Luka 4:9.
Kale, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti Satana ayenela kuti sanatenge Yesu mwacindunji kupita naye ku kacisi kukamuyesa. Nsanja ya Mlonda ya Cingelezi ya March 1, 1961, inagwilizanitsa zimenezi ndi zimene Satana anacita, pamene anatenga Yesu ndi kupita naye ku phili lalitali kukamuyesa mwa kumuonetsa maufumu onse a padziko lapansi. Inakamba kuti padziko lapansi palibe phili lalitali lakuti munthu angaimililepo n’kuyamba kuona maufumu onse a dziko lapansi. Ndiyeno, Nsanjayo inakamba kuti Satana
ayenela kuti sanatenge Yesu ndi kupita naye ku kacisi weniweni mwacindunji. Komabe, m’kupita kwa nthawi, nkhani zina za mu Nsanja ya Mlonda, zinakamba kuti Yesu akanati adziponye pansi kucokela pamwamba pa kacisi, akanafa.Anthu ambili amakamba kuti popeza kuti Yesu sanali Mlevi, iye sakanaloledwa kuimilila pamwamba pa nyumba yopatulika ya pakacisi. Conco, amakamba kuti Satana ayenela kuti anayesa Yesu m’masomphenya. Zaka zambilimbili zimenezi zisanacitike, Ezekieli nayenso anatengedwela ku kacisi m’masomphenya.—Ezekieli 8:3, 7-10; 11:1, 24; 37:1, 2.
Koma ngati Yesu anatengedwela ku kacisi m’masomphenya, ena angafunse kuti:
-
Kodi Yesu akanaonadi kuti kuziponya pansi kucoka pamwamba pa kacisi n’ciyeso?
-
Panthawi ina, pamene Satana anayesa Yesu, anamuuza kuti asandutse miyala yeniyeni kukhala mkate, ndi kuti amugwadile ndi kum’lambila. Conco, kodi n’kutheka kuti Satana anafuna kuti Yesu adziponye pansi kucoka pamwamba pa kacisi weniweni?
Koma, ngati Satana anatenga Yesu mwacindunji ndi kupita naye ku kacisi weniweni, ena angafunse kuti:
-
Kodi Yesu anaphwanya Lamulo mwa kuimilila pamwamba pa kacisi wopatulika?
-
Kodi Yesu anacoka bwanji ku cipululu kupita ku kacisi ku Yerusalemu?
Tiyeni tikambilane mfundo zina zoonjezela zimene zingatithandize kuyankha mafunso aŵili omalizawa.
Katswili wina dzina lake D. A. Carson analemba kuti, liu lacigiliki lakuti “kacisi” lopezeka m’buku la Mateyu ndi Luka, lingatanthauze malo onse a pa kacisi osati cabe malo opatulika a pakacisi, amene Alevi okha anali kuloledwa kuloŵamo. Pakona ya kum’mwela ca kum’mawa kwa kacisi, panali denga lafulati limene linali lalitali kwambili. Yesu ayenela kuti anaikidwa pa dengalo. Kucokela pansi m’cigwa ca Kidroni kufika pa denga la kacisi panali potalika mamita 140. Wolemba mbili yakale Josephus anakamba kuti malowa anali pamwamba kwambili cakuti ngati munthu waimililapo n’kuyang’ana pansi, “anali kucita cizwezwe.” Ngakhale kuti Yesu sanali Mlevi, akanaimililabe pa dengalo, ndipo palibe amene akanamuletsa.
Koma, kodi Yesu anacoka bwanji ku cipululu kupita ku kacisi ku Yerusalemu? Sitidziŵa bwinobwino. Baibulo limangokamba kuti Yesu anatengedwa kupita ku Yerusalemu. Silikamba kutalika kwa mtunda umene unalipo kucokela kumene Yesu analili kufika ku Yerusalemu, kapena utali wa nthawi imene iye anayesedwa ndi Satana. Conco, n’kutheka kuti Yesu anapita ku Yerusalemu ngakhale kuti zimenezo zikanamutengela nthawi yaitali.
Satana poonetsa Yesu “maufumu onse a dziko lapansi,” ayenela kuti anaseŵenzetsa masomphenya, cifukwa kulibe phili lalitali limene munthu angakwelepo n’kuona maufumu onse a padziko. Izi zingafanane ndi mmene tingaonetsele munthu madela ena a dziko lapansi pogwilitsila nchito TV. Satana anagwilitsila nchito masomphenya, koma anali kufuna kuti Yesu amugwadile zenizeni ndi kumulambila. (Mateyu. 4:8, 9) Conco, pamene Satana anatenga Yesu kupita naye ku kacisi, n’kutheka kuti anafunadi kuti Yesu aike moyo wake pa ngozi mwa kumuuza kuti adziponye pansi kucokela pamwamba pa kacisi. Koma Yesu anakana. Cimeneci sicikanakhala ciyeso cacikulu ngati Satana anayesa Yesu pogwilitsila nchito masomphenya.
Motelo, n’kutheka kuti Yesu anapita ku Yerusalemu ndi kuimilila pamwamba penipeni pa kacisi. Koma malinga ndi zimene takamba kuciyambi kwa nkhani ino, sitidziŵa bwinobwino mmene Satana anaonetsela Yesu kacisi. Zimene tidziŵa n’zakuti Satana anapitiliza kuyesa Yesu kuti acite cinthu coipa, koma nthawi zonse Yesu anali kukana molimba mtima.
^ par. 2 Onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsamba 16-18, ndime 5-8, 12.
^ par. 2 Malemba a Ezekieli 37:1-14, ndi Chivumbulutso 11:7-12, amanena za zinthu zimene zinacitika mu 1919. Ulosi wa pa Ezekieli 37:1-14, umanena za anthu onse a Mulungu amene anayambanso kulambila koona mu 1919, pambuyo pa zaka zambili za ukapolo. Koma lemba la Chivumbulutso 11:7-12, limanena za kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene akhala akutsogolela anthu a Mulungu. Kwa kanthawi, abale amenewa analibe ufulu wocita zinthu zauzimu. Koma mu 1919, anayambilanso kucita zinthu zauzimu.