NKHANI YOPHUNZILA 40
Limbikilani Monga Anacitila Petulo
“Ambuye, cokani pali ine pano, cifukwa ndine munthu wocimwa.”—LUKA 5:8.
NYIMBO 38 Adzakulimbitsa
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Kodi Petulo anamva bwanji atapha nsomba mozizwitsa?
PETULO anacezela usiku wonse osaphako nsomba iliyonse. Mosayembekezela, Yesu anamuuza kuti: “Palasila kwakuya, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” (Luka 5:4) Petulo anakayikila ngati angaphe nsomba, koma anacitabe zimene Yesu anamuuza. Maukondewo anayamba kung’ambika cifukwa ca kuculuka kwa nsomba zimene anapha. Atazindikila kuti cinali cozizwitsa, Petulo na asodzi anzake “anadabwa kwambili.” Iye anati: “Ambuye, cokani pali ine pano, cifukwa ndine munthu wocimwa.” (Luka 5:6-9) Mwacionekele, Petulo anadziona kuti ni wosayenela kukhala pafupi na Yesu.
2. N’cifukwa ciyani kukambilana citsanzo ca Petulo n’kothandiza kwa ife?
2 Petulo anakambadi zoona kuti anali “munthu wocimwa.” Malemba amaonetsa kuti nthawi zina, iye anali kukamba na kucita zinthu zimene pambuyo pake anali kudziimba nazo mlandu. Monga Petulo, kodi inunso mwakhala mukulimbana na cifooko kapena cizolowezi coipa? Ngati n’telo, citsanzo ca Petulo cingakulimbikitseni. Motani? Ganizilani izi: Yehova akanafuna, sakanalola kuti zophophonya za Petulo zilembedwe m’Baibo. Komabe, zinalembedwa mouzilidwa kuti titengepo phunzilo. (2 Tim. 3:16, 17) Petulo anali munthu ngati ife tomwe, ndipo anali na zifooko. Conco, kuphunzila za iye kungatithandize kudziŵa kuti Yehova satiyembekezela kucita zinthu mwangwilo. Iye amafuna kuti tilimbikile, tisafooke, mosasamala kanthu za zophophonya zathu.
3. N’cifukwa ciyani tiyenela kupilila?
3 N’cifukwa ciyani tiyenela kulimbikila? Paja amati kanthu ni khama. Mwacitsanzo, munthu zingam’tengele zaka kuti aphunzile kuliza gitala. Pophunzila angamaphonyetse. Koma akalimbikila amafika podziŵa bwino kuliza gitala. Ngakhale atakhala katswili, nthawi zina angamaphonyetsebe. Komabe, iye salefuka. Amapitilizabe kukulitsa luso lake. Mofananamo, pambuyo pogonjetsa cizolowezi cinacake, tingabwelezenso cizolowezi coipaco. Koma timalimbikilabe kuti tikwanilitse colinga cathu. Tonsefe tingakambe zosayenela kapena kucita zinthu zimene pambuyo pake timadziimba nazo mlandu. Komabe, ngati sitibwelela m’mbuyo, Yehova adzatithandiza kuti tipitilize kucita bwino. (1 Pet. 5:10) Tiyeni tikambilane citsanzo ca Petulo cakulimbikila. Cifundo cimene Yesu anamuonetsa mosasamala kanthu za zophophonya zake, cingatilimbikitse nafenso kutumikilabe Yehova.
ZOPHOPHONYA ZA PETULO NA MADALITSO AMENE ANALANDILA
4. Malinga na Luka 5:5-10, kodi Petulo anati ciyani za iye mwini? Nanga Yesu anam’tsimikizila ciyani?
4 Malemba safotokoza cifukwa cake Petulo anadzicha “munthu wocimwa,” kapena macimo amene anali kuganizila. (Ŵelengani Luka 5:5-10.) Koma n’kutheka kuti iye anacita zolakwa zazikulu. Yesu anazindikila kuti Petulo anali na mantha, mwina cifukwa codziona kuti sangakwanitse kucita zoyenela. Yesu anadziŵanso kuti Petulo angakhalebe wokhulupilika. Conco, mwacikondi iye anamuuza kuti: “Usawope.” Cidalilo ca Yesu mwa Petulo cinasintha umoyo wake. Petulo na m’bale wake Andireya anasiya nchito yawo ya usodzi, n’kukhala otsatila a Mesiya. Cisankho cimeneci cinawabweletsela madalitso osaneneka.—Maliko 1:16-18.
5. Kodi Petulo anapindula bwanji cifukwa cosalola maganizo olefula kumulepheletsa kulabadila ciitano ca Yesu?
5 Pokhala wotsatila wa Khristu, Petulo anali na mwayi woona zozizwitsa za Yesu. Anaona Yesu akucilitsa odwala, kutulutsa ziŵanda, ngakhale kuukitsa akufa. b (Mat. 8:14-17; Maliko 5:37, 41, 42) Analinso na mwayi woona ulemelelo wa Yesu monga Mfumu yam’tsogolo. Petulo sanaiŵale cocitikaci. (Maliko 9:1-8; 2 Pet. 1:16-18) Inde, akanapanda kukhala wotsatila wa Yesu, iye sakanaona zonsezi. Mwacionekele, Petulo anakondwela kwambili poona kuti sanalole maganizo olefula kumulepheletsa kulandila madalitso onsewa.
6. Kodi cinali copepuka kwa Petulo kuthetsa zifooko zake? Fotokozani.
6 Mosasamala kanthu za zimene anaona komanso kumva, Petulo anali kulimbanabe na zifooko zake. Onankoni zitsanzo izi. Yesu atafotokoza mmene adzavutikile komanso kuphedwa kwake pokwanilitsa ulosi wa m’Baibo, Petulo anam’dzudzula. (Maliko 8:31-33) Mobweleza-bweleza, Petulo na atumwi anzake anali kukangana za amene anali wamkulu pakati pawo. (Maliko 9:33, 34) Pa usiku wakuti maŵa lake Yesu aphedwa, mopupuluma Petulo anadula khutu la munthu wina. (Yoh. 18:10) Ndipo usiku womwewo, cifukwa coopa anthu, Petulo anakana bwenzi lake Yesu katatu konse kuti sam’dziŵa. (Maliko 14:66-72) Izi zinapangitsa Petulo kulila mopwetekedwa mtima ngako.—Mat. 26:75.
7. Kodi Petulo anapatsidwa mwayi wotani Yesu ataukitsidwa?
7 Yesu sanamusiye mtumwi wake wolefulidwayo. Yesu ataukitsidwa, anapeleka mwayi kwa Petulo wakuti aonetse ngati akali kum’konda. Yesu anaika Petulo kukhala m’busa wodzicepetsa wa nkhosa zake. (Yoh. 21:15-17) Iye anauvomela udindo umenewo. Pa tsiku la Pentekosite, Petulo anali ku Yerusalemu, ndipo anali pagulu la Akhristu oyamba kudzozedwa na mzimu woyela.
8. Ni colakwa cacikulu citi cimene Petulo anacita ali ku Antiokeya?
8 Ngakhale pambuyo pokhala Mkhristu wodzozedwa, Petulo anali kulimbanabe na zifooko zake. Mu 36 C.E, Petulo anaona kamaso pamene Koneliyo, munthu wosadulidwa, anadzozedwa na mzimu woyela. Uwu unali umboni woonekelatu wakuti “Mulungu alibe tsankho,” komanso kuti anthu amitundu ina angakhale mu mpingo wacikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa izi, Petulo anali womasuka kudyela pamodzi na anthu a mitundu ina, zimene kumbuyoku sakanacita. (Agal. 2:12) Komabe, Akhristu ena aciyuda anali kuona kuti Ayuda na anthu amitundu ina sayenela kudyela pamodzi. Ayuda ena atafika ku Antiokeya, Petulo analeka kudya na Akhristu a mitundu ina, mwina poopa kukhumudwitsa Akhristu aciyuda. Mtumwi Paulo anaona kuti cimeneco n’cinyengo. Conco, anam’dzudzula pamaso pa anthu. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti Petulo anaphonyetsanso, sanabwelele m’mbuyo. N’ciyani cinam’thandiza?
N’CIYANI CINATHANDIZA PETULO KUSABWELELA M’MBUYO?
9. Kodi Yohane 6:68, 69 ionetsa bwanji kuti Petulo anali wogonjela?
9 Petulo anali wokhulupilika, ndipo sanalole ciliconse kumulepheletsa kutsatila Yesu. Pa nthawi ina, anaonetsa kukhulupilika kwake pamene Yesu anakamba zinthu zimene ophunzila ake sanadzimvetse. (Ŵelengani Yohane 6:68, 69.) M’malo mopempha Yesu kuti awafotokozele tanthauzo lake, anthu ambili analeka kum’tsatila. Koma Petulo sanatelo. Iye anazindikila kuti Yesu yekhayo ndiye ali na “mawu amoyo wosatha.”
10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kum’dalila Petulo? (Onaninso cithunzi.)
10 Yesu sanam’siye Petulo. Usiku wakuti maŵa lake aphedwa, iye anadziŵa kuti Petulo na atumwi ena adzam’thaŵa. Ngakhale n’telo, anali na cidalilo mwa Petulo cakuti iye adzabwelela na kukhalabe wokhulupilika. (Luka 22:31, 32) Yesu anamvetsa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Maliko 14:38) Ngakhale kuti Petulo anam’kana, Yesu sanam’taye mtumwi wake ameneyu. Ndipo iye ataukitsidwa, anaonekela kwa Petulo, amene mwacionekele anali yekha. (Maliko 16:7; Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Tangoganizilani mmene zinam’limbikitsila mtumwi wacisoniyo!
11. Kodi Yesu anam’tsimikizila motani Petulo kuti Yehova adzam’thandiza?
11 Yesu anam’tsimikizila Petulo kuti Yehova adzam’thandiza. Iye ataukitsidwa, anacitanso cozizwitsa kwa Petulo na atumwi anzake powathandiza kupha nsomba. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikila, cozizwitsa cimeneci cinatsimikizila Petulo kuti Yehova adzasamalila zosoŵa zake zakuthupi. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukila mawu a Yesu akuti Yehova adzasamalila anthu amene ‘apitiliza kufuna-funa Ufumu coyamba.’ (Mat. 6:33) Izi zinapangitsa Petulo kuika utumikila patsogolo m’malo mwa nchito yake ya usodzi. Iye molimba mtima analalikila pa Pentekosite mu 33 C.E., ndipo anthu masauzande analabadila uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake, iye anathandiza Asamariya na anthu amitundu ina kuphunzila za Khristu na kum’tsatila. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Zoonadi, Yehova anam’gwilitsa nchito kwambili pokoka anthu a mitundu yonse kuti abwele mu mpingo.
ZIMENE TIPHUNZILAPO
12. Kodi citsanzo ca Petulo cingatithandize bwanji ngati tikulimbana na cifooko cacikulu?
12 Yehova angatithandize kuti tisafooke. Cingakhale covuta kupilila, maka-maka ngati takhala tikulimbana na zifooko zathu kwa nthawi yaitali. Nthawi zina, zofooka zathu zingakhale zazikulu kuposa zimene Petulo anali nazo. Koma Yehova angatipatse mphamvu kuti tisafooke. (Sal. 94:17-19) Mwacitsanzo, m’bale wina anali kucita mathanyula kwa zaka zambili asanaphunzile coonadi. Olo kuti analeka khalidweli, nthawi zina zilakolako zoipa zimabwelabe m’maganizo mwake. N’ciyani cimam’thandiza kusagonja? Mwiniwake anati: “Yehova amatilimbitsa.” Anatinso: “Mwa thandizo la mzimu woyela . . . , naona kuti n’zotheka kukhalabe na umoyo wokondweletsa Yehova . . . Iye wakhala akunigwilitsa nchito, ndipo amanilimbitsa mosasamala kanthu za zifooko zanga.”
13. Monga ionetsela Machitidwe 4:13, 29, 31, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Petulo? (Onaninso cithunzi.)
13 Monga taonela, Petulo analakwitsapo zinthu kangapo konse cifukwa coopa anthu. Koma pemphelo, linam’thandiza kucita zinthu molimba mtima. (Ŵelengani Machitidwe 4:13, 29, 31.) Nafenso tingathe kugonjetsa mantha athu. Onani zinacitika kwa m’bale wacinyamata dzina lake Horst panthawi ya ulamulilo wa Nazi ku Germany. Kangapo konse kusukulu, anakamba mawu otamanda Hitler cifukwa com’kakamiza. Makolo ake sanam’dzudzule ayi, koma anapemphela naye kuti Yehova am’thandize kukhala wolimba mtima. Mwa thandizo la makolo ake komanso kudalila kwake Yehova, m’kupita kwa nthawi m’bale Horst anakhala wolimba mtima. Pa nthawi ina, iye anati: “Yehova anali nane nthawi zonse.” c
14. Kodi akulu acikondi angawathandize bwanji amene akulimbana na zofooketsa?
14 Yehova na Yesu sadzakusiyani. Petulo atakana Khristu, anayenela kupanga cisankho cofunika kwambili. Kodi adzangosiya kulimbana na zifooko zake, kapena adzapitiliza kukhala wophunzila wa Khristu? Yesu anali atapemphela kwa Yehova kuti cikhulupililo ca Petulo cisafooke. Iye anauza Petulo za pemphelo limenelo, ndipo anali na cidalilo cakuti patsogolo pake adzalimbikitsa abale ake. (Luka 22:31, 32) Kukumbukila mawu a Yesu amenewa, kunali kum’limbikitsa ngako Petulo! Tikafuna kupanga cisankho cofunika kwambili, Yehova angagwilitse nchito akulu acikondi kuti atithandize kukhalabe okhulupilika. (Aef. 4:8, 11) Izi n’zimene amacita mkulu wina ciyambakale dzina lake Paul. Amapempha aja amene akuona kuti akufuna kugonja ku zifooko zawo, kuti aganizile cimene cinapangitsa Yehova akuti awakokele m’coonadi. Kenako, amawatsimikizila kuti cikondi cosasintha ca Yehova sicingamulole kuti awasiye. M’bale Paul anati: “Naona Yehova akuthandiza anthu ambili olefuka kuti akhalenso olimba.”
15. Kodi citsanzo ca Petulo, na ca m’bale Horst zionetsa bwanji kuti mfundo ya pa Mateyu 6:33 ni yoona?
15 Monga mmene Yehova anasamalila zosoŵa za kuthupi za Petulo na atumwi anzake, adzacitanso cimodzimodzi kwa ife tikaika Ufumu wake patsogolo. (Mat. 6:33) Nkhondo yaciŵili ya padziko lonse itatha, m’bale Horst amene tam’chula uja, anaganiza zoyamba upainiya. Iye anali wosauka kwambili, ndipo anakayikila ngati adzakwanitsa kudzisamalila kwinaku akucita upainiya. Kodi anatani? Anaganiza zomuyesa Yehova mwa kuthela mlungu wonse mu ulaliki pomwe wadela anacezela mpingo wawo. Kumapeto kwa mlunguwo, sanakhulupilile pamene wadela anam’patsa envelopu, koma sanamuuze kumene yacokela. Mu envelopu imeneyo munali ndalama zimene zinam’thandiza kwa miyezi ingapo pocita upainiya. M’bale Horst anaona kuti mphatso imeneyi ni citsimikizo cakuti Yehova adzam’samalila. Iye anathela moyo wake wonse mu utumiki wanthawi zonse.—Mal. 3:10.
16. N’cifukwa ciyani citsanzo ca Petulo, na zimene analemba n’zopindulitsa kwa ife?
16 Petulo anakondwela kwambili poona kuti Yesu sanam’siye. Ndipo Khristu sanaleke kuphunzitsa Petulo kukhala mtumwi wokhulupilika, komanso wacitsanzo cabwino kwa Akhristu. Masiku ano, titengapo maphunzilo ambili pa zimene Petulo anaphunzila kwa Yesu. Ndipo zimene anaphunzilazo anauzako ena kupyolela m’makalata aŵili amene analembela mipingo ya m’zaka za zana loyamba. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mfundo zocepa za m’makalata amenewo, na mmene tingazigwilitsile nchito.
NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu
a Nkhani ino alembela aja amene amalimbana na zifooko zawo, pofuna kuwatsimikizila kuti n’zotheka kuzigonjetsa, komanso kuti asabwelele m’mbuyo potumikila Yehova.
b Malemba ambili m’nkhani ino acokela mu Uthenga Wabwino wa Maliko. Zioneka kuti iye analemba zimene anamva kwa Petulo, amene anali mboni yoona na maso zocitikazo.
c Mbili ya m’bale Horst Henschel mungaipeze m’nkhani yakuti, “Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu,” mu Galamukani! ya Chichewa ya February 22, 1998.
d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Monga tionela pa cithunzi ici, makolo a m’bale Horst Henschel anali kupemphela naye na kum’thandiza kukhalabe wolimba