MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU
Muzibwelelamo mu Mfundo Zikulu-zikulu
Kodi mumavutika kukumbukila zimene mwacoka kuŵelenga? Zimenezo zimacitika kwa aliyense wa ife nthawi zina. N’ciyani cingatithandize kuti tizikumbukila zimene taŵelenga? Ni kubwelelamo mu mfundo zikulu-zikulu.
Pamene mukuŵelenga, nthawi na nthawi muziima na kuganizila mfundo zikulu-zikulu. Mtumwi Paulo anathandiza amene anali kuŵelenga kalata yake kuganizila mfundo zikulu-zikulu za m’kalatayo. Anacita zimenezi mwa kuŵauza kuti: “Pa zimene tikunenazi, mfundo yaikulu ndi yakuti.” (Aheb. 8:1) Kucita zimenezi kunathandiza amene anali kuŵelenga kalata yake kumvetsa zimene anali kuŵelenga. Kunawathandizanso kuona mmene mfundo iliyonse inali kugwilizanila na nkhani yonse.
Mukamaliza kuŵelenga, mwina mungapatule mphindi 10 kuti musinkhesinkhe mfundo zikulu-zikulu zimene mwaŵelenga. Ngati simukwanitsa kukumbukila mfundo zimene mwaŵelenga, mungaonenso tumitu twa mkati, kapena kuŵelenga ciganizo coyamba ca ndime iliyonse. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kukumbukila mfundo zikulu-zikulu. Mukaphunzila mfundo yatsopano, yesani kuifotokoza m’mawu anu-anu. Kubwelelamo mu mfundo zikulu-zikulu kudzakuthandizani kuti muzikumbukila zimene mwaŵelenga. Kudzakuthandizaninso kuseŵenzetsa zimene mwaŵelengazo pa umoyo wanu.