Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Aisiraeli analiko na zakudya zina kupatulapo mana na zinzili m’cipululu?

Kwa zaka 40 pomwe Aisiraeli anali m’cipululu cakudya cawo cacikulu cinali mana. (Eks 16:35) Koma kaŵili konse, Yehova anawapatsanso zinzili kuti adye. (Eks 16:​12, 13; Nu 11:31) Komabe, Aisiraeli analinso na zakudya zina zocepa.

Mwacitsanzo, Yehova nthawi zina anali kuwatsogolela ku “malo oti amangepo msasa” kumene anali kupezako madzi na zakudya zina. (Num. 10:33) Amodzi mwa malo amenewa anali Elimu “kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza” imene mosakaikila inali na zipatso. (Eks 15:27) Buku lakuti Plants of the Bible inafotokoza kuti “mtengo wa kanjedza umamela m’malo osiyana-siyana,. . . ndipo ndico cakudya cimene cimapezeka kwambili m’cipululu. Mtengowu umapeleka zakudya, mafuta komanso pokhala kwa anthu mamiliyoni.”

N’kutheka kuti Aisiraeli anaimililako pa dziŵe lina lake m’cipululu ca Sinai. Dziŵelo masiku ano limadziŵika kuti Feiran ndipo ili mbali ya cigwa ca Wadi Feiran. a Buku lakuti Discovering the World of the Bible inati, “cigwa cimeneci n’cacikulu kufika makilomita 130 ndipo n’cimodzi mwa zigwa zazikulu, zokongolola ngako komanso zodziŵika kwambili m’cipululu ca Sinai.” Inapitiliza kuti, “munthu akayenda makilomita 45 kucokela komwe cigwaci cimakumana na nyanja, amapeza dziŵe lokongola la Feiran lozungulidwa na mitengo ya kanjedza. Dziŵe limeneli niyozama mamita 610 ndipo n’lalitali makilomita 4.8. Kukongola kwake anakuyelekezela na munda wa Edeni. Kwa zaka zambili, anthu amapita kucigawo cimeneci kuti akaone mitengo ya kanjedza yopitilila masauzande.”

Mitengo ya kanjedza m’cigwa ca Feiran

Potuluka mu Iguputo, Aisiraeli ananyamula ufa wokanda komanso ziwiya zokandilamo ufa umenewo ndipo n’kutheka kuti ananyamulako mbewu ya zakudya zina komanso mafuta ophikila. Koma n’zoonekelatu kuti zinthu zimenezi sizinakhale nthawi yaitali. Ponyamuka “anapitanso ndi nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zambilimbili.” (Eks. 12:​34-39) Cifukwa ca mikhalidwe yovuta ya m’cipululu, n’zoonekelatu kuti ziŵeto zambili zinafa. Ziŵeto zina ayenela kuti anaziphika monga cakudya ndipo n’kutheka kuti zina anadzipeleka nsembe ngakhale kwa milungu yonyenga. b (Mac 7:​39-43) Komanso, n’zoonekelatu kuti ziŵeto zina zinabelekana. Tikutelo cifukwa ca mawu amene Yehova anauza anthu ake pambuyo pakuti am’cimwila, iye anati “ana anu adzakhala abusa m’cipululu kwa zaka 40.” (Num 14:33) Conco, ziŵetozo zinapatsa Aisiraeli mkaka komanso nyama monga cakudya. Koma zimenezi sizinali zokwanila kwa anthu pafupifupi 3 miliyoni kwa zaka 40. c

Kodi nyama zinali kupeza kuti madzi na cakudya? d N’kutheka kuti kalelo m’cipululu munali kugwa mvula yambili ndipo munali zomela zambili. Buku la Insight on the Scriptures Volume 1 imati zaka 3,500 zapitazo, “kumalo komwe Aisiraeli anadutsa kunali madzi ambili kuposa amene aliko masiku ano. Tidziŵa zimenezi cifukwa kumalo amenewa masiku ano kuli zigwa zonoka zomwe zinapangidwa na mitsinje yomwe inaliko kalelo.” Ngakhale n’telo, cipululu anali malo opanda pokhala komanso oopsa. (Deut. 8:​14-16 ) Yehova akanapanda kupeleka madzi mozizwitsa kwa Aisiraeli, iwo akanafa na nyama zawo.—Eks 15:​22-25; 17:​1-6; Num 20:​2, 11.

Mose anauza Aisiraeli kuti Yehova anawadyetsa mana kuti ‘adziŵe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mawu onse ocokela m’kamwa mwa Yehova.’—Deut. 8:3.

a Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1992, masamba 24-25.

b Baibo imachula nthawi ziŵili pomwe Aisiraeli anapeleka nsembe kwa Yehova m’cipululu. Nthawi yoyamba inali pamene anali kudzoza ansembe ndiponso pomwe anali kucita Pasika. Zocitika zonsezi zinacitika m’caka ca 1512 B.C.E., comwe cinali caka caciŵili kucokela pomwe Aisiraeli anatuluka mu Iguputo—Lev. 8:14–9:24; Num. 9:​1-5.

c Cakumapeto kwa ulendo wawo wa zaka 40 wa m’cipululu, Aisiraeli anafunkha nyama masauzande ambili kunkhondo. (Num 31:​32-34) Ngakhale n’telo, iwo anapitiliza kudya mana mpaka ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.—Yos 5:​10-12.

d Palibe ciliconse coonetsa kuti nyama nazonso zinali kudya mana. Yehova anawauza kuti aliyense azitolela mana mogwilizana na muyeso umene angadye ndipo sanachulepo za nyama.—Eks 16:​15, 16.