Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
Mfundo Yothandiza pa Kuŵelenga Kwanu
Loŵezani pa mtima “Nyimbo Zauzimu”
Mlongo Lorraine wa ku America anati “Masiku ena ngati napsinjika maganizo kapena kudziona kukhala wacabe-cabe, Yehova amanilimbikitsa kupitila m’nyimbo za pa JW Broadcasting®.”
Kungoyambila kale-kale, “nyimbo zauzimu” zakhala mbali ya kulambila kwa Cikhristu. (Akol. 3:16) Ngati munaloŵeza nyimbozi pa mtima, zingakulimbikitseni ngakhale pamene mulibe buku la nyimbo kapena cipangizo camakono. Yesani kucita zotsatilazi kuti mukwanitse kuloŵeza nyimbozi pa mtima.
● Ŵelengani mofatsa mawu a m’nyimbo kuti mumvetse tanthauzo lake. N’capafupi kukumbukila cinthu cimene timamvetsa tanthauzo lake. Mawu a nyimbo zathu zonse kuphatikizapo nyimbo zopekedwa koyamba komanso nyimbo za ana, zilipo pa jw.org. Loŵani pa danga lakuti Laibulale kenako dinizani pa Nyimbo.
● Lembani pa pepala mawu a m’nyimbo. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuloŵeza mawuwo pa mtima.—Deut. 17:18.
● Muziyeseza mokweza mawu. Muziŵelenga kapena kuimba nyimbo mobweleza-bweleza.
● Yesani ngati mungathe kukumbukila zimene mwaloŵeza. Yesezani kuimba nyimbo yonse popanda kuona m’buku la nyimbo kapena mawu ake, kenako onani mmene mwacitila.