NKHANI YOPHUNZILA 49
Kodi Yehova Adzayankha Mapemphelo Anga?
“Mudzaitanila pa ine komanso mudzabwela ndi kupemphela kwa ine ndipo ine ndidzakumvetselani.”—YER. 29:12.
NYIMBO 41 Mvelani pemphelo Langa Conde
ZIMENE TIKAMBILANE a
1-2. N’ciyani cingacititse kuti nthawi zina tiziona kuti Yehova samamvetsela mapemphelo athu?
“SANGALALALA mwa Yehova ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.” (Sal. 37:4) Lonjezo losangalatsa zedi! Koma kodi tiziyembekezela kuti Yehova adzatipatsa ciliconse cimene tingam’pemphe nthawi yomweyo? N’cifukwa ciyani funsoli n’lofunika? Ganizilani zocitika izi. Mlongo yemwe ni mbeta wakhala akupemphela kuti akaloŵe nawo Sukulu ya Alengezi a Ufumu, koma zaka zambili zapitapo osaitanidwa. M’bale wacinyamata wakhala akupemphela kwa Yehova kuti acile matenda ake ofooketsa thanzi kotelo kuti azicita zambili mu mpingo. Koma thanzi lake sikukhalabe bwino. Makolo acikhristu akhala akupemphela kuti mwana wawo asasiye coonadi. Koma mwana wawoyo akusiya kutumikila Yehova.
2 Mwina inunso mwakhala mukupemphelela cinacake kwa Yehova, koma simukucipezabe. Mwa ici, mungaganize kuti Yehova amayankha mapemphelo a anthu ena koma osati anu. Mwinanso mungaganize kuti munalakwitsa cinacake. Mlongo wina dzina lake Janice b anaganizapo conco. Iye na mwamuna wake anali kupemphelela colinga cawo cokakatumikila pa Beteli. Iye anati: “N’nali otsimikiza kuti posakhalitsa tidzaitanidwa ku Beteli.” Koma zaka zinapitapo iwo osaitanidwa. Pambuyo pake iye anati: “N’nakhumudwa ndipo sin’namvetse. N’nali kudzifunsa kuti ‘kodi n’namulakwila ciyani Yehova?’ N’nali kupemphela mocita kuchula ndithu kuti nifuna kupita ku Beteli. Nanga n’cifukwa ciyani sanaliyankhe pemphelo langa?”
3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 Nthawi zina tingadzifunse ngati Yehova amamvetsela mapemphelo athu. Ngakhale amuna ena acikhulupililo a m’nthawi zakale anaganizapo conco. (Yobu 30:20; Sal. 22:2; Hab. 1:2) N’ciyani cingakutsimikizileni kuti Yehova adzayankha mapemphelo anu? (Sal 65:2) Kuti tiyankhe funsoli, coyamba tiyenela kuyankha mafunso otsatilawa: (1) Kodi tiyenela kuyembekezela ciyani kwa Yehova? (2) Kodi Yehova amayembekezela ciyani kwa ife? (3) N’cifukwa ciyani nthawi zina tingafunike kusintha zimene timapemphelela?
KODI TIYENELA KUYEMBEKEZELA CIYANI KWA YEHOVA?
4. Malinga na Yeremiya 29:12, kodi Yehova akutilonjeza ciyani?
4 Yehova akulonjeza kuti adzamvetsela mapemphelo athu. (Ŵelengani Yeremiya 29:12.) Mulungu wathu amawakonda alambili ake okhulupilika ndipo sadzanyalanyaza mapemphelo awo. (Sal. 10:17; 37:28) Komabe izi sizitanthauza kuti iye adzatipatsa zilizonse zimene timam’pempha. Tingafunike kuyembekeza mpaka m’dziko latsopano kuti tikalandile zina mwa zinthu zimene timapempha.
5. Kodi Yehova amafuna kuona ciyani akamamvetsela mapemphelo athu? Fotokozani.
5 Yehova amafuna kuona ngati mapemphelo athu amagwilizana na colinga cake cacikulu. (Yes. 55:8, 9) Colinga cimeneco ciphatikizapo kudzaza dziko lapansi na anthu acimwemwe komanso ogwilizana pansi pa ulamulilo wake. Koma Satana amanena kuti anthu angakhale osangalala atazilamulila okha. (Gen. 3:1-5) Pofuna kuonetsa kuti maganizo a Mdyelekezi amenewa ni abodza, Yehova walola kuti anthu adzilamulile okha. Ndipo ulamulilo wa anthu wabweletsa mavuto ambili amene aliko masiku ano. (Mlal. 8:9). Tidziŵa kuti Yehova sadzacotsapo mavuto onsewa pali pano. Akanatelo, anthu ena akaganiza kuti ulamulilo wa anthu uli bwino, ndipo umatha kuthetsa mavuto.
6. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala otsimikiza kuti nthawi zonse Yehova amacita zinthu mwacikondi komanso mwacilungamo?
6 Yehova angayankhe mapemphelo ofanana m’njila zosiyana. Mwacitsanzo, Mfumu Hezekiya atadwala kwakayakaya, anapempha Yehova kuti am’cilitse. Ndipo Yehova anam’cilitsadi. (2 Maf. 20:1-6) Komabe, mtumwi Paulo atacondelela Yehova kuti am’cotsele “munga m’thupi,” umene mwina unali vuto la thanzi, Yehova sanalicotse vutolo. (2 Akor 12:7-9) Ganizilaninso citsanzo ca mtumwi Yakobo na mtumwi Petulo. Onse aŵili anafuna kuphedwa na Mfumu Herode. Mpingo unapemphelela Petulo, ndipo mwacionekele unapemphelelanso Yakobo. Koma Yakobo anaphedwa pomwe Petulo anapulumutsidwa mozizwitsa. (Mac. 12:1-11) Ndiye tingadzifunse kuti, ‘N’cifukwa ciyani Yehova sanapulumutse onse aŵili?’ Baibo sikambapo zilizonse. c Koma cimene tidziŵa n’cakuti Yehova “sacita cosalungama.” (Deut. 32:4) Tidziŵanso kuti Yehova anali kuwakonda onse aŵili Petulo na Yakobo. (Chiv. 21:14) Nthawi zina mapemphelo angayankhidwe m’njila imene sitinayembekezele. Sitidandaula na mmene Yehova amasankhila kuyankha mapemphelo athu. Cifukwa ciyani? Cifukwa tili na cidalilo conse kuti nthawi zonse mayankho ake amakhala acikondi komanso acilungamo.—Yobu 33:13.
7. Kodi timayesetsa kupewa ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani?
7 Timapewa kuyelekezela mikhalidwe yathu ni ya anthu ena. Mwacitsanzo, tingapemphe kuti Yehova atithandize pa mbali inayake, koma pempho lathu osayankhidwa. Pambuyo pake, tingamve za munthu wina amene anapeleka pemphelo imodzimodzi ndipo zioneka kuti Yehova analiyankha pemphelo lake. Zotelezi zinamucitikilapo mlongo Anna. Iye anali kupemphela kuti mwamuna wake Matthew acile matenda a khansa. Pa nthawi imodzimodziyo, alongo aŵili acikulile analinso kudwala khansa. Anna anali kupemphelela mwamuna wake komanso alongowo. Alongowo anacila koma Matthew anamwalila. Poyamba Anna anadzifunsa kuti, ngati alongowo anacila cifukwa cakuti Yehova anawathandiza, n’cifukwa ciyani mapemphelo ake sanayankhidwe akuti mwamuna wake acile? N’zoona kuti sitikudziŵa kwenikweni cifukwa cake alongowa anacila. Koma cimene tidziŵa n’cakuti Yehova adzathetselatu mavuto onse amene alipowa. Ndipo amacita kulakalaka kudzaukitsa mabwenzi ake amene anamwalila.—Yobu 14:15
8. (a) Malinga n’kunena kwa Yesaya 43:2, kodi Yehova amatithandiza bwanji? (b) Kodi pemphelo ingatithandize bwanji tikamakumana na mavuto aakulu? (Onelelani vidiyo yakuti Pemphelo Limatithandiza Kupilila.)
8 Yehova amatithandiza nthawi zonse. Monga Tate wathu wacikondi, Yehova samakondwela kutiona tikuvutika. (Yes 63:9) Ngakhale n’telo, iye satichinga ku mavuto onse omwe ali ngati mitsinje komanso lawi lamoto. (Ŵelengani Yesaya 43:2.) Komabe, iye analonjeza kuti adzatithandiza ‘tikamadutsa’ m’mavutowo. Ndipo sadzalola kuti mavutowo ativulaze kothelatu. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyela womwe ni wamphamvu kuti utithandize kupilila. (Luka 11:13; Afil. 4:13). Conco, tiyenela tizikhala otsimikiza kuti nthawi zonse tidzakhala na zonse zofunikila kuti tipilile, komanso kukhalabe okhulupilika kwa iye. d
KODI YEHOVA AMAYEMBEKEZELA CIYANI KWA IFE?
9. Malinga na Yakobo 1:6, 7, n’cifukwa ciyani tiyenela kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzatithandiza?
9 Yehova amayembekezela kuti tizimudalila. (Aheb. 11:6) Nthawi zina mavuto athu angaoneke osatheka kuwapilila. Tingayambe kukaikila ngati Yehova adzatithandiza. Koma Baibo imatitsimikizila kuti na thandizo la Mulungu ‘tingakwele khoma’ (Sal. 18:29) Conco m’malo molola kuti zikaiko zimenezi zikule mumtima mwathu, tiyenela kupemphela kwa iye mwacikhulupililo tili na cidalilo cakuti iye adzayankha mapemphelo athu.—Ŵelengani Yakobo 1:6, 7.
10. Pelekani citsanzo ca mmene tingacitilie zinthu mogwilizana na mapemphelo athu.
10 Yehova amatiyembekezela kucita zinthu mogwilizana na mapemphelo athu. Mwacitsanzo, m’bale angapemphe kuti Yehova am’thandize kukamba na bwana wake kuti am’patse nthawi yokapezeka pa msonkhano wa cigawo. Kodi Yehova angayankhe bwanji pemphelo limenelo? Angathandize m’baleyo kuti akhale wolimba mtima kuti akalankhule na bwana wakeyo. Ngakhale n’telo, m’baleyo ayenela kucitapo kanthu mwa kukamba na bwana wake. Ndipo angafunike kucita zimenezo mobweleza-bweleza. Mwina angafunike kusinthana masiku ogwila nchito na wanchito wina. Ndipo ngati n’kofunika, anganene kuti pamasiku omwe sadzagwila nchito, asakalandile malipilo.
11. N’cifukwa ciyani tiyenela kupemphela mobwelezabweleza za vuto lathu?
11 Yehova amatiyembekezela kupemphela mobweleza-bweleza pa mavuto athu. (1 Ates. 5:17) Yesu anaonetsa kuti nthawi zina mapemphelo athu sangayankhidwe nthawi yomweyo. (Luka 11:9) Conco musataye mtima! Ndipo muzipemphela mocokela pansi pa mtima komanso mobweleza-bweleza. (Luka 18:1-7) Ngati tipitiliza kupemphela kwa Yehova pa nkhani imodzimodzi, timamuonetsa kuti nkhaniyo ni yofunikadi. Timaonetsanso cikhulupililo kuti akhoza kutithandiza
N’CIFUKWA CIYANI NTHAWI ZINA TINGAFUNIKE KUSINTHA ZIMENE TIMAPEMPHELELA?
12. (a) Tingadzifunse funso liti ponena za zopempha zathu? Nanga n’cifukwa ciyani? (b) Tingaonetse bwanji kuti mapemphelo athu amalemekeza Yehova (Onani pa danga lakuti “ Kodi Zopempha Zanga Zimaonetsa Ulemu kwa Yehova?”)
12 Ngati sitinalandile cinthu cimene takhala tikupemphelela, tingafunike kudzifunsa mafunso atatu. Loyamba, ‘Kodi nikupemphelela cinthu coyenela?’ Nthawi zambili timaona kuti tidziŵa zoyenela kwa ife. Koma nthawi zina zimene timapemphela sizingatiphindulile kwenikweni. Tikamapemphelela za vuto linalake, pangakhale njila ina yabwino yothetsela vutolo kuposa imene tikupempha. Ndipo nthawi zina zimene timapemphelela sizingakhale zogwilizana na cifunilo ca Yehova. (1 Yoh. 5:14) Mwacitsanzo, ganizilani za makolo amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino. Iwo anapempha Yehova kuti athandize mwana wawo kukhalabe m’coonadi. Pempho limenelo lingakhale lomveka. Koma Yehova sakakamiza aliyense kumutumikila. Iye amafuna kuti tonsefe, kuphatikizapo ana athu, tidzisankhile tokha kum’tumikila. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) Conco m’malomwake, makolo angapemphe kuti Yehova awathandize kum’fika pamtima mwana wawo pom’phunzitsa kuti adzisankhile yekha kukonda Yehova na kukhala bwenzi lake.—Miy. 22:6; Aef. 6:4.
13. Malinga n’kunena kwa Aheberi 4:16, kodi Yehova angatithandize pa nthawi iti? Fotokozani.
13 Funso laciŵili lingakhale lakuti, ‘Kodi ni nthawi yoyenela kuti Yehova ayankhe pemphelo langa?’ Nthawi zina tingaone kuti tifunikila yankho lam’mangu-m’mangu pa pemphelo lathu. Koma Yehova ndiye amadziŵa bwino nthawi yoyenela kutiyankha. (Ŵelengani Aheberi 4:16.) Ngati nthawi yomweyo sitinalandile zimene tapempha, tingaganize kuti yankho la Yehova n’lakuti ‘Iyai.’ Koma yankho lake m’ceni-ceni lingakhale lakuti ‘Osati pali pano.’ Mwacitsanzo, ganizilaninso za m’bale wacinyamata uja yemwe anapempha kuti acilitsidwe matenda ake. Ngati Yehova mozizwitsa akanam’cilitsa m’baleyo, Satana akanati m’baleyo anapitiliza kutumikila Yehova cifukwa cakuti anam’cilitsa. (Yobu 1:9-11; 2:4) Kuwonjezela apo, Yehova anaikilatu kale nthawi pamene adzacotselatu matenda onse. (Yes. 33:24; Chiv. 21:3, 4) Koma pakali pano, tisayembekezele kucilitsidwa mozizwitsa. Conco m’baleyo angapemphe Yehova kuti am’patse mphamvu komanso mtendele wa mumtima, kuti apilile matendawo na kupitiliza kumutumikila mokhulupilika.—Sal 29:11.
14. Mwaphunzilapo ciyani ku cocitika ca Janice?
14 Kumbukilani cocitika ca Janice amene anali na cifuno cokatumikila ku Beteli. Panapita zaka 5 kuti azindikile mmene Yehova anayankhila pemphelo lake. Iye anati, “Yehova anaseŵenzetsa nthawiyo kuniphunzitsa na kuniyenga. N’nafunika kukulitsa cidalilo canga mwa iye, komanso kukulitsa cizolowezi canga cocita phunzilo la munthu mwini. Cina, n’nafunikilanso kupeza cimwemwe cimene cimabwela mosasamala kanthu za kumene munthu akutumikila.” Patapita nthawi, Janice na mwamuna wake anaitanidwa m’nchito yadela. Akayang’ana kumbuyo, Janice amati, “Yehova anayankha pemphelo langa koma m’njila imene sin’nayembekezele. Zinan’tengela nthawi kuti nione ubwino wa yankho lake. Koma niyamikila kuti ananionetsa cikondi komanso kukoma mtima.”
15. N’cifukwa ciyani tingafunike kupempha zinthu zosiyana-siyana kwa Yehova? (Onaninso zithunzi.)
15 Funso lacitatu lingakhale lakuti, Kodi niyambe kupemphelela cinthu cina?’ Zimakhala bwino kuchula zimene tikufuna kwa Yehova mwacindunji. Koma kuti tizindikile cifunilo cake kwa ife, tiyenela kupempha zinthu zosiyana-siyana. Ganizilani citsanzo ca mlongo mbeta amene akhala akupemphela kuti akaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Afuna akaloŵe sukuluyi kuti akatumikile ku malo osoŵa. Conco pamene akupemphela kuti akaloŵe sukuluyi, angacitenso bwino kupempha Yehova kuti am’thandize kuzindikila njila zina zoonjezela utumiki wake. (Mac. 16:9, 10). Ndiyeno angacite zinthu mogwilizana na pemphelo lake mwa kufunsa woyang’anila dela ngati mipingo yapafupi ifunikila apainiya ambili. Kapena angalembele ku ofesi ya nthambi kufunsila za madela amene afunika olalikila ambili. e
16. Tingakhale otsimikiza za ciyani?
16 Monga taonela, tingakhale otsimikiza kuti Yehova amayankha mapemphelo athu mwacikondi komanso mwacilungamo. (Sal. 4:3; Yes. 30:18) Nthawi zina sitingalandile yankho limene tinali kuyembekezela. Koma Yehova sanganyalanyaze mapemphelo athu. Iye amatikonda ngako, ndipo sadzatisiya. (Sal. 9:10) Conco pitilizani ‘kumukhulupilila nthawi zonse’ mwa kum’khutulila za mumtima mwanu kupitila m’pemphelo.—Sal. 62:8.
NYIMBO 43 Pemphelo la Mayamiko
a Nkhani ino ifotokoza cifukwa cake tiyenela kukhala na cidalilo mwa Yehova kuti iye nthawi zonse amayankha mapemphelo athu mwacikondi komanso mwacilungamo.
b Maina ena asinthidwa.
c Onani nkhani yakuti “Kodi Mumakhulupilila Mmene Yehova Amacitila Zinthu?” mu Nsanja ya Mlonda ya February 2022, ndime 3-6.
d Kuti mudziŵe zambili pa mmene Yehova amatithandizila kupilila mavuto, onelelani vidiyo yakuti Pemphelo Limatithandiza Kupilila pa jw.org.
e Kuti mudziŵe zimene mungacite pofuna kudzipeleka kukatumikila m’gawo la nthambi ina, onani buku lakuti Gulu Locita Cifunilo ca Yehova mutu 10, ndime 6-9.
f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Alongo aŵili akupemphela asanadzaze fomu yofunsila Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Patapita nthawi, wina akuitanidwa pamene wina sanaitanidwe. M’malo mokhumudwa, mlongo amene sanaitanidwe akupemphela kwa Yehova kuti am’thandize kuzindikila njila zina zimene angawonjezele utumiki wake. Ndiyeno, akulemba kalata ku ofesi ya nthambi yofunsila kukatumikila ku malo osoŵa.