Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 46

Kodi Mumasamalila Cishango Canu Cacikulu Cacikhulupililo?

Kodi Mumasamalila Cishango Canu Cacikulu Cacikhulupililo?

“Nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo.”​—AEF. 6:16.

NYIMBO 119 Tikhale na Cikhulupililo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) Malinga na Aefeso 6:16, n’cifukwa ciani tifunikila “cishango cacikulu cacikhulupililo”? (b) Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

KODI muli na “cishango cacikulu cacikhulupililo”? (Ŵelengani Aefeso 6:16.) Mwacionekele muli naco. Mofanana na cishango cacikulu cimene cimateteza mbali yaikulu ya thupi, cikhulupililo cathu cimatiteteza ku zinthu zoipa za m’dzikoli, monga ciwelewele, ciwawa na makhalidwe ena oipa.

2 Komabe, popeza tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ cikhulupililo cathu cidzapitiliza kuyesedwa. (2 Tim. 3:1) Kodi mungacite ciani kuti mudziŵe ngati cikhulupililo canu n’colimba? Nanga mungacite ciani kuti mugwilitsitse cishango canu cacikhulupililo? Tiyeni tikambilane mayankho pa mafunso amenewa.

PENDANI MOSAMALA KUTI MUONE MMENE CISHANGO CANU CILILI

Pambuyo pomenya nkhondo, asilikali anali kuonetsetsa kuti akonzanso zishango zawo (Onani ndime 3)

3. Kodi kale msilikali anali kucita ciani na cishango cake? Nanga n’cifukwa ciani anali kucita zimenezo?

3 M’nthawi yakale, kaŵili-kaŵili msilikali anali kukhala na cishango cokutidwa na cikumba. Iye anali kupaka mafuta cishangoco kuti cisacite nguwe, komanso kuti cikumba cake cisawole. Msilikali akaona kuti cishango cake cawonongeka, anali kuyesetsa kucikonza n’colinga cakuti akhale wokonzeka nthawi zonse kumenya nkhondo. Kodi citsanzo cimeneci citiphunzitsa ciani za cikhulupililo cathu?

4. N’cifukwa ciani tifunika kupenda mosamala kuti tione mmene cishango cathu ca cikhulupililo cilili? Nanga tingacite bwanji zimenezi?

4 Mofanana na asilikali a m’nthawi yakale, nthawi zonse tifunika kupenda mosamala kuti tione mmene cishango cathu ca cikhulupililo cilili, na kucilimbitsa kuti tikhale okonzeka nthawi zonse kumenya nkhondo yauzimu. Monga Akhristu, tili pa nkhondo yolimbana na mizimu yoipa. (Aef. 6:10-12) Mkhristu aliyense payekha ali na udindo wosamalila cishango cake cacikhulupililo kuti cikhalebe colimba. Kodi mungacite ciani kuti cikhulupililo canu cidzakhalebe colimba mukadzakumana na mayeselo? Coyamba, mufunika kupempha thandizo kwa Mulungu. Ndiyeno, muyenela kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu kuti mukwanitse kudziona mmene Mulungu amakuonelani. (Aheb. 4:12) Baibo imati: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu.” (Miy. 3:5, 6) Pokumbukila mfundo imeneyi, ganizilani zosankha zimene munapanga posacedwapa. Mwacitsanzo, kodi munakumana na vuto lalikulu la za cuma? Ngati n’telo, kodi pa nthawiyo munaganizilapo za lonjezo la Yehova la pa Aheberi 13:5 lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono”? Kodi lonjezo limeneli linakupatsani cidalilo cakuti Yehova adzakuthandizani? Ngati n’conco, zimenezi zionetsa kuti mumayesetsa kusamalila cishango canu cacikhulupililo kuti cikhalebe colimba.

5. Kodi mungapeze ciani pambuyo popenda cikhulupililo canu?

5 Pambuyo popenda mosamala cikhulupililo canu, mungadabwe na zimene mungapeze. Mungazindikile kuti muli na zofooka zimene simunali kuziona. Mwacitsanzo, mungazindikile kuti nkhawa yopambanitsa, mabodza, na zolefula zayamba kuwononga cikhulupililo canu. Ngati za conco zakucitikilani, kodi mungateteze bwanji cikhulupililo canu kuti cisawonongekeletu?

DZITETEZENI KU NKHAWA ZOPAMBANITSA, MABODZA, NA ZOLEFULA

6. Kodi nkhawa zina zabwino ni ziti?

6 Nkhawa zina n’zabwino. Mwacitsanzo, timakhala na nkhawa yofuna kukondweletsa Yehova na Yesu. (1 Akor. 7:32) Ngati tacita chimo lalikulu, timakhala na nkhawa yofuna kukonzanso ubwenzi wathu na Mulungu. (Sal. 38:18) Timakhalanso na nkhawa yofuna kukondweletsa mnzathu wa m’cikwati na kusamalila a m’banja lathu. Komanso, timadela nkhawa za umoyo wa Akhristu anzathu.—1 Akor. 7:33; 2 Akor. 11:28.

7. Malinga na Miyambo 29:25, n’cifukwa ciani sitifunika kuopa anthu?

7 Komabe, nkhawa yopambanitsa ingawononge cikhulupililo cathu. Mwacitsanzo, tingamadele nkhawa nthawi zonse kuti tidzapeza bwanji cakudya na zovala zokwanila. (Mat. 6:31, 32) Cifukwa ca nkhawa imeneyi, tingayambe kutaya nthawi yambili pofuna-funa zinthu zakuthupi. Tingafike ngakhale poyamba kukonda ndalama. Tikalola zimenezi kuticitikila, cikhulupililo cathu mwa Yehova cingafooke, ndipo izi zingawononge ubwenzi wathu na iye. (Maliko 4:19; 1 Tim. 6:10) Cinanso, tingayambe kudela nkhawa kwambili za mmene anthu ena amationela. Izi zingapangitse kuti tiziopa kwambili anthu. Tingafike pololela kucita zinthu zimene Yehova amazonda cifukwa coopa kunyozedwa kapena kuzunzidwa ndi anthu. Conco, tifunika kupempha Yehova kuti atiwonjezele cikhulupililo na kutithandiza kukhala olimba mtima kuti tisamaope anthu.—Ŵelengani Miyambo 29:25; Luka 17:5.

(Onani ndime 8) *

8. Tiyenela kucita ciani tikamvela mabodza okhudza Yehova na gulu lake?

8 Satana, “tate wake wa bodza,” amaseŵenzetsa anthu amene amawalamulila pofalitsa mabodza onena za Yehova, komanso abale na alongo athu. (Yoh. 8:44) Mwacitsanzo, ampatuko amafalitsa mabodza pofuna kuwononga mbili ya gulu la Yehova. Amacita zimenezi kupitila pa mawebusaiti, pa TV, na m’njila zina. Mabodza amenewo ni ina mwa “mivi . . . yoyaka moto” ya Satana. (Aef. 6:16) Kodi tiyenela kucita ciani ngati munthu wina wayamba kutiuza mabodza aconco? Sitiyenela kumvetsela! Cifukwa ciani? Cifukwa timakhulupilila Yehova komanso timadalila abale athu. Conco, timapewa kukambilana na ampatuko mwa njila ina iliyonse. Sitikangana nawo pa zilizonse, olo kuti zimene akamba tacita nazo cidwi.

9. Kodi zolefula zingatikhudze bwanji?

9 Zolefula zingafooketse cikhulupililo cathu. Nthawi zina, tingafooke cifukwa ca mavuto amene takumana nawo. N’zoona kuti tikakumana na mavuto, sitiyenela kungowalekelela. Koma si bwino kumangoganizila za mavuto athu nthawi zonse. Tikatelo, tingaiŵale zinthu zabwino zimene Yehova watilonjeza. (Chiv. 21:3, 4) Ndiponso tingalefuke kwambili cakuti tingaleke kutumikila Yehova. (Miy. 24:10) Koma tisalole kuti zaconco ziticitikile.

10. Mwaphunzila ciani m’kalata imene mlongo wina analemba?

10 Ganizilani za mlongo wina wa ku America. Iye wasungabe cikhulupililo cake cili colimba, ngakhale kuti akusamalila mwamuna wake wodwala kwambili. Mlongoyo analembela kalata likulu lathu la pa dziko lonse. M’kalatayo, iye anati: “Nthawi zina, vuto limeneli limatisoŵetsa mtendele na kutilefula, koma ciyembekezo cathu n’colimba. Nimam’yamikila ngako Yehova kaamba ka zonse zimene amatiphunzitsa, cifukwa zimatithandiza kulimbitsa cikhulupililo kuti tisafooke. Kukamba zoona, timafunikila kwambili malangizo na cilimbikitso cimeneci. Zimatithandiza kupitiliza kutumikila Yehova na kupilila mayeselo ocokela kwa Satana.” Citsanzo ca mlongoyu citiphunzitsa kuti n’zotheka kukhalabe olimba tikakumana na mavuto. Motani? Muziona mavuto anu kuti ni mayeselo ocokela kwa Satana. Muzidalila Yehova kuti akutonthozeni. Ndipo muziyamikila cakudya cauzimu cimene amapeleka.

Kodi mumasamalila “cishango” canu “cacikulu cacikhulupililo” kuti cikhalebe colimba? (Onani ndime 11) *

11. Ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa kuti tione ngati cikhulupililo cathu n’colimba?

11 Kodi pali mbali zina za cishango canu cacikhulupililo zimene mufunika kulimbitsa? Pa miyezi ingapo yapita, kodi munakwanitsa kupewa nkhawa yopambanitsa? Kodi munapewa kumvetsela kwa anthu ampatuko kapena kukangana nawo kaamba ka mabodza amene amafalitsa? Nanga kodi munakwanitsa kukhalabe olimba mutakumana na zolefula? Ngati n’conco, ndiye kuti cikhulupililo canu n’colimba. Koma tifunika kukhala maso, cifukwa Satana ali na zida zina zimene amaseŵenzetsa polimbana nafe. Tsopano, tiyeni tikambilane cimodzi mwa zida zimenezo.

DZITETEZENI KU MZIMU WOKONDA ZINTHU ZAKUTHUPI

12. N’ciani cingacitike ngati tayamba kukonda zinthu zakuthupi?

12 Kukonda zinthu zakuthupi kungafooketse cikhulupililo cathu, ndiponso kungacepetse cangu cathu potumikila Yehova. Mtumwi Paulo anati: “Msilikali amene ali pa nkhondo sacita nawo zamalonda zimene anthu wamba amacita, pofuna kukondweletsa amene anamulemba usilikali.” (2 Tim. 2:4) Asilikali aciroma sanali kuloledwa kucita malonda a mtundu uliwonse. Kodi n’ciani cikanacitika ngati msilikali sanatsatile malangizo amenewa?

13. N’cifukwa ciani msilikali sanali kufunika kucita malonda?

13 Tiyelekezele motele: Tinene kuti m’maŵa gulu la asilikali likuyeseza momenyela nkhondo, koma mmodzi wa iwo palibe. Iye ali bize ku msika kugulitsa zakudya m’shopu. M’madzulo, asilikaliwo apatula nthawi yonola malupanga awo na kuona ngati zida zawo zankhondo zili bwino. Koma pa nthawiyi, msilikali amene ali na shopu uja akukonza zakudya zokagulitsa tsiku lotsatila. M’maŵa tsiku lotsatila, adani akuukila mwadzidzidzi. Kodi ni msilikali uti amene adzakhala wokonzeka kumenya nkhondo na kukondweletsa mkulu wa asilikali? Nanga bwanji ngati munali kumenya nawo nkhondoyo? Kodi mukanakonda kuima pafupi na msilikali wokonzekela bwino kapena uja amene anali bize na malonda?

14. Monga asilikali a Khristu, n’ciani cimene timaona kuti n’cofunika kwambili?

14 Mofanana na asilikali okonzekela bwino aja, sititangwanika na zinthu zina. Timaikabe maganizo athu pa colinga cathu cacikulu, comwe ni kukondweletsa Atsogoleli athu, Yehova na Yesu. Timaona kuti kuyanjidwa na Yehova na Yesu n’kofunika kwambili kuposa ciliconse cimene tingapeze m’dziko la Satanali. Ndiye cifukwa cake timayesetsa kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu potumikila Yehova. Komanso, timayesetsa kusamalila cishango cathu ca cikhulupililo na zida zina zonse za nkhondo yauzimu kuti zikhalebe zolimba.

15. Ni cenjezo lotani limene Paulo anapeleka? Nanga n’cifukwa ciani?

15 Tifunika kukhala maso nthawi zonse. Cifukwa ciani? Mtumwi Paulo anacenjeza kuti “anthu ofunitsitsa kulemela” ‘amasoceletsedwa n’kusiya cikhulupililo.’ (1 Tim. 6:9, 10) Mawu akuti ‘amasoceletsedwa’ aonetsa kuti tingayambe kutangwanika kwambili posakila zinthu zakuthupi zosafunika kweni-kweni. Izi zingapangitse kuti tikhale na ‘zilakolako zambili zopweteketsa,’ ndiponso tingayambe kucita ‘zinthu mopanda nzelu.’ Conco, tisalole zilakolako zimenezi kuzika mizu mu mtima mwathu. Koma tikumbukile kuti izi ni zida zimene Satana amaseŵenzetsa pofuna kufooketsa cikhulupililo cathu.

16. Kodi nkhani yolembedwa pa Maliko 10:17-22 iyenela kutisonkhezela kuganizila mafunso ati?

16 Tiyelekezele kuti muli na ndalama zokwanila zimene mungagulile zinthu zambili. Kodi mungalakwitse ngati mungagule zinthu zimene mufuna koma zosafunika kweni-kweni? Osati kweni-kweni. Koma ganizilani mafunso awa: Olo kuti mungakwanitse kugula zinthu zimenezo, kodi mudzakhala na nthawi na mphamvu zokwanila zoseŵenzetsa zinthuzo na kuzisamalila? Kodi mwina mungayambe kukonda kwambili zinthu zakuthupi zimenezo? Komanso, kodi kukonda zinthu zakuthupi kungakupangitseni kucita zinthu ngati mnyamata uja amene anakana pempho la Yesu lakuti acite zambili potumikila Mulungu? (Ŵelengani Maliko 10:17-22.) Izi ziwonetsa kuti ni bwino kukhala na umoyo wosalila zambili kuti tiziseŵenzetsa nthawi yathu ya mtengo wapatali na mphamvu zathu pocita cifunilo ca Mulungu.

GWILITSITSANI CISHANGO CANU CACIKHULUPILILO

17. Kodi sitiyenela kuiŵala ciani?

17 Sitifunika kuiŵala kuti tili pa nkhondo yauzimu. Conco, tifunika kukhala okonzeka kumenya nkhondoyo tsiku lililonse. (Chiv. 12:17) Abale na alongo athu sangatinyamulile cishango cathu cacikhulupililo. Aliyense wa ife ali na udindo wogwila mwamphamvu cishango cake cacikhulupililo.

18. N’cifukwa ciani m’nthawi yakale asilikali anali kugwilitsitsa zishango zawo akakhala ku nkhondo?

18 M’masiku akale, msilikali anali kulemekezedwa ngati ni wolimba mtima pa nkhondo. Koma akafika ku nyumba alibe cishango cake, anali kucita manyazi. Wolemba mbili waciroma, dzina lake Tacitus, analemba kuti: “Zinali zocititsa manyazi kwambili ngati msilikali wasiya cishango cake ku nkhondo.” Ici n’cimodzi mwa zifukwa zimene zinali kupangitsa asilikali kugwilitsitsa zishango zawo akakhala ku nkhondo.

Mlongo akugwilitsitsa cishango cake cacikhulupililo mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, na kugwila nchito yolalikila mokangalika (Onani ndime 19)

19. Tingacite ciani kuti tigwilitsitse cishango cathu cacikhulupililo?

19 Timagwilisitsa cishango cathu cacikhulupililo mwa kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, komanso kuuzako ena za dzina la Yehova na Ufumu wake. (Aheb. 10:23-25) Kuwonjezela apo, timaŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse na kupempha Yehova kuti atithandize kuseŵenzetsa malangizo na mfundo za m’Baibo m’zocita zathu zonse. (2 Tim. 3:16, 17) Tikatelo, palibe cida ciliconse ca Satana cimene cidzatha kutiwononga kothelatu. (Yes. 54:17) “Cishango” cathu “cacikulu cacikhulupililo” cidzatiteteza. Tidzakhalabe olimba potumikila pamodzi na abale na alongo athu. Ndipo tidzapambana nkhondo ya cikhulupililo imene timamenya tsiku lililonse. Koposa zonse, tidzasangalala kukhala ku mbali ya Yesu pamene adzapambana pa nkhondo yolimbana na Satana komanso onse amene ali ku mbali yake.—Chiv. 17:14; 20:10.

NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

^ ndime 5 Asilikali anali kufunikila cishango kuti akhale otetezeka ku nkhondo. Cikhulupililo cathu cili ngati cishango. Msilikali anali kufunika kusamalila cishango cake. Nafenso tifunika kusamalila cikhulupililo cathu kuti cikhalebe colimba. M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tingacite kuti “cishango” cathu “cacikulu cacikhulupililo” cikhalebe colimba.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene lipoti ya ampatuko yokamba za Mboni za Yehova iyamba kuulutsidwa, banja la Mboni likuzimitsa TV yawo nthawi yomweyo.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Ndiyeno, pa kulambila kwa pabanja, tate akuseŵenzetsa Baibo polimbitsa cikhulupililo ca banja lake.