Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 10

Kukonda Yehova na Kum’yamikila Kudzakusonkhezelani Kubatizika

Kukonda Yehova na Kum’yamikila Kudzakusonkhezelani Kubatizika

Cikundiletsa kubatizidwa n’ciani?”​—MAC. 8:36.

NYIMBO 37 Kutumikila Yehova na Moyo Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Malinga na Machitidwe 8:27-31, 35-38, n’ciani cinasonkhezela nduna ya ku Itiyopiya kubatizika?

KODI mumafuna kubatizika kuti mukhale wophunzila wa Khristu? Kukonda Yehova na kumuyamikila kwasonkhezela anthu ambili kupanga cosankha cimeneci. Ganizilani citsanzo ca nduna ina imene inali kutumikila mfumukazi ya ku Itiyopiya.

2 Munthu wa ku Itiyopiya ameneyu anabatizika mwamsanga atakhutila na zimene anaphunzila m’Malemba. (Ŵelengani Machitidwe 8:27-31, 35-38.) N’ciani cinamusonkhezela kubatizika? N’zoonekelatu kuti anali kukonda Mawu a Mulungu. Iye anali kuŵelenga mavesi a m’buku la Yesaya pamene anali kuyenda pa galeta yake kucokela ku Yerusalemu. Ndipo Filipo atakambilana naye lembalo, iye anayamikila kwambili zimene Yesu anamucitila. Koma kodi n’cifukwa ciani iye anapita ku Yerusalemu? Anapita kukalambila Yehova. Izi zionetsa kuti anali atakulitsa kale cikondi pa Yehova. Zioneka kuti munthu ameneyu anasiya cipembedzo ca makolo ake na kuyamba kulambila pamodzi na mtundu wokhawo umene unali wodzipatulila kwa Mulungu woona. Kukonda Yehova n’kumenenso kunamusonkhezela kupanga cosankha cofunika kwambili ca kubatizika kuti akhale wophunzila wa Khristu.—Mat. 28:19.

3. N’ciani cingalepheletse munthu kubatizika? (Onani bokosi yakuti “ Kodi Mtima Wanu Ni Wotani?”)

3 Kukonda Yehova kungakusonkhezeleni na imwe kuti mubatizike. Koma nthawi zina cikondi cingakulepheletseni kubatizika. Motani? Ganizilani zitsanzo zingapo izi: Mwina mumakonda kwambili abululu anu na anzanu osakhulupilila, ndipo mumada nkhawa kuti mukabatizika, adzayamba kukuzondani. (Mat. 10:37) Kapena mwina muli na zizoloŵezi zina zimene mudziŵa kuti Mulungu amadana nazo, koma muona kuti n’zovuta kuzileka. (Sal. 97:10) Ndiponso n’kutheka kuti kuyambila muli wamng’ono mwakhala mukucita zikondwelelo na miyambo yokhudzana na cipembedzo conama. Ndipo mwina mumakonda zinthu zokondweletsa zimene zimacitika pa zikondwelelo zimenezo. Pa cifukwa cimeneci, mungaone kuti n’zovuta kuleka miyambo yosakondweletsa Yehova imeneyo. (1 Akor. 10:20, 21) Conco, mufunika kusankha kuti n’ciani cimene mudzakonda kwambili, kapena n’ndani amene mudzakonda kwambili.

AMENE MUYENELA KUM’KONDA KWAMBILI

4. Kodi n’ciani cacikulu cimene cingakusonkhezeleni kubatizika?

4 Pali zinthu zambili zabwino zimene mumakonda na kuziyamikila. Mwacitsanzo, ngakhale musanayambe kuphunzila na Mboni za Yehova, mwina munali mutayamba kale kuikonda kwambili Baibo. N’kuthekanso kuti munali mutayamba kale kukonda Yesu. Ndipo popeza tsopano mwadziŵana na Mboni za Yehova, mwina mumakonda kuceza nawo. Koma kukonda cabe zinthu zimenezi sikungakusonkhezeleni kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika. Cacikulu cimene cingakusonkhezeleni kubatizika ni kukonda Yehova Mulungu. Ngati mumakonda Yehova kuposa cina ciliconse, simudzalola ciliconse kapena aliyense kukulepheletsani kuyamba kum’tumikila. Kukonda Yehova kudzakusonkhezelani kubatizika ndiponso kudzakuthandizani kupitiliza kum’tumikila mokhulupilika.

5. Kodi tikambilana mafunso ati?

5 Yesu anakamba kuti tifunika kukonda Yehova na mtima wathu wonse, moyo, maganizo, na mphamvu zathu zonse. (Maliko 12:30) Kodi mungacite ciani kuti muyambe kukonda kwambili Yehova na kum’lemekeza? Kuganizila cikondi cimene Yehova amationetsa, kudzatisonkhezela kuti nafenso tizimukonda. (1 Yoh. 4:19) Kodi ni makhalidwe ena ati amene tidzakhala nawo tikayamba kukonda Yehova? *

6. Malinga na Aroma 1:20, kodi njila imodzi imene tingaphunzilile za Yehova ni iti?

6 Phunzilani za Yehova mwa kuona na kuganizila zimene analenga. (Ŵelengani Aroma 1:20; Chiv. 4:11) Muziganizila mmene Yehova anapangila zomela na zinyama. Ndipo muzisinkha-sinkha mmene zimenezi zimaonetsela kuti iye ni wanzelu kwambili. Phunzilankoni za mmene Yehova anapangila thupi lathu lodabwitsa. (Sal. 139:14) Cinanso, ganizilani za mphamvu zoopsa zimene dzuŵa lili nazo. Ndipo musaiŵale kuti dzuŵa ni limodzi cabe mwa nyenyezi mabiliyoni ambili-mbili amene Yehova analenga. * (Yes. 40:26) Mukamacita zimenezi, mudzayamba kumulemekeza kwambili Yehova. N’zoona kuti kudziŵa kuti Yehova ni wanzelu komanso wamphamvu kwambili n’kofunika kuti mukhale naye pa ubwenzi. Koma ici ni ciyambi cabe. Kuti mufike pomukonda kwambili Yehova, mufunika kudziŵa zambili za iye.

7. Kodi mufunika kukhulupilila ciani kuti muyambe kumukonda kwambili Yehova?

7 Mufunika kukhulupilila kuti Yehova amakukondani kwambili. Kodi cimakuvutani kukhulupilila kuti Mlengi wa kumwamba na dziko lapansi amakukondani na kukuonani kuti ndimwe wofunika? Ngati n’conco, kumbukilani kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:26-28) Iye “amasanthula mitima yonse,” komanso monga mmene Davide anauzila Solomo, Yehova analonjeza kuti ‘mukam’funafuna, adzalola kuti mum’peze.’ (1 Mbiri 28:9) Ndipo pali pano mumaphunzila Baibo cifukwa cakuti Yehova ‘anakukokani.’ (Yer. 31:3) Mukadziŵa bwino zimene Yehova wakucitilani, m’pamenenso mudzayamba kumukonda kwambili.

8. Mungaonetse bwanji kuti mumayamikila cikondi ca Yehova?

8 Njila imodzi imene mungaonetsele kuti mumayamikila cikondi ca Yehova ni kukamba naye m’pemphelo. Cikondi canu pa Yehova cidzakula ngati mumuuza nkhawa zanu na kumuyamikila pa zonse zimene amakucitilani. Ndipo mukaona mmene Yehova amayankhila mapemphelo anu, ubwenzi wanu na iye udzalimba. (Sal. 116:1) Mudzafika pokhulupililadi kuti amakumvetsetsani. Koma kuti mukhalebe naye pa ubwenzi wolimba, mufunika kumvetsetsa mmene iye amaonela zinthu. Mufunikanso kudziŵa zimene amafuna kuti imwe muzicita. Palibe cina cimene cingakuthandizeni kudziŵa zimenezi, koma kuphunzila Mawu ake Baibo.

Njila yabwino kwambili yolimbitsila ubwenzi wathu na Mulungu komanso yodziŵila zimene amafuna kuti tizicita ni kuŵelenga Baibo (Onani ndime  9) *

9. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumaikonda Baibo?

9 Phunzilani kukonda Mawu a Mulungu, Baibo. Baibo yokha ndiyo imakamba zoona ponena za Yehova na colinga cake. Mungaonetse kuti mumakonda Baibo mwa kuiŵelenga tsiku lililonse, kukonzekela phunzilo lanu la Baibo, ndiponso kuseŵenzetsa zimene mumaphunzila. (Sal. 119:97, 99; Yoh. 17:17) Kodi muli na ndandanda ya kuŵelenga Baibo panokha? Kodi mumayesetsa kuitsatila mwa kuŵelenga Baibo tsiku lililonse?

10. Kodi cimodzi cimene cimapangitsa Baibo kukhala buku lapadela kwambili n’ciani?

10 Cinthu cimodzi cimene cimapangitsa Baibo kukhala buku lapadela kwambili n’cakuti muli nkhani zofotokoza umoyo wa Yesu zolembedwa ndi anthu amene anamuonapo. Ni buku lokhalo limene limakamba zoona pa nkhani ya zimene Yesu wakucitilani. Pamene muphunzila zimene Yesu anakamba na kucita, mwacionekele mudzafuna kukhala naye pa ubwenzi.

11. Mungacite ciani kuti muyambe kukonda Yehova?

11 Phunzilani kukonda Yesu, ndipo cikondi canu pa Yehova cidzakula. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa Yesu anatengela kwambili makhalidwe a Atate wake. (Yoh. 14:9) Conco, pamene muphunzila zambili za Yesu, m’pamenenso mudzamudziŵa bwino kwambili Yehova na kumukonda. Ganizilani cifundo cimene Yesu anali kuonetsa kwa anthu amene anali kuonedwa ngati onyozeka. Mwacitsanzo, ganizilani mmene anali kucitila zinthu ndi anthu osauka, odwala, na ofooka. Ganizilaninso za malangizo othandiza amene iye amakupatsani, komanso mmene umoyo wanu wasinthila cifukwa comvela malangizowo.—Mat. 5:1-11; 7:24-27.

12. Kodi kuphunzila za Yesu kungakusonkhezeleni kucita ciani?

12 Cikondi canu pa Yesu cidzalimbilako mukamaganizila kwambili za mmene iye anapelekela moyo wake monga dipo kuti macimo athu akhululukidwe. (Mat. 20:28) Kudziŵa kuti Yesu anadzipeleka kukufelani, kungakulimbikitseni kuti mulape na kupempha Yehova kuti akukhululukileni. (Mac. 3:19, 20; 1 Yoh. 1:9) Mukayamba kukonda Yehova na Yesu, mwacidziŵikile mudzafuna kugwilizana ndi anthu amenenso amakonda Yehova na Yesu.

13. Kodi Yehova wakupatsani ciani?

13 Phunzilani kukonda banja la Yehova. Abululu anu na mabwenzi anu amene si Mboni mwina sangamvetsetse cifukwa cake mufuna kudzipatulila kwa Yehova. Iwo angayambe kukutsutsani. Koma Yehova adzakuthandizani mwa kukupatsani abale na alongo, amene ni banja lauzimu. Ngati muyesetsa kuyanjana na banja lauzimu limeneli, mudzapeza mabwenzi amene adzakukondani na kukuthandizani. (Maliko 10:29, 30; Aheb. 10:24, 25) M’kupita kwa nthawi, abululu anu nawonso angayambe kutumikila Yehova na kutsatila mfundo zake za makhalidwe abwino.—1 Pet. 2:12.

14. N’ciani cimene mwaona pa umoyo wanu coonetsa kuti mfundo ya pa 1 Yohane 5:3, ni ya zoona?

14 Phunzilani kukonda mfundo za Yehova na kuzitsatila mu umoyo wanu. Mukalibe kudziŵa Yehova, mwina munali na mfundo zanu zimene munali kuyendela mu umoyo. Koma tsopano mumaona kuti mfundo za Yehova ndizo zabwino kwambili. (Sal. 1:1-3; ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Ganizilani malangizo amene Baibo imapeleka kwa amuna, akazi, makolo, ndi ana. (Aef. 5:22–6:4) Kodi mwaona kuti banja lanu layamba kukhala lacimwemwe cifukwa cotsatila malangizo amenewa? Kodi mwakwanitsa kuthetsa zizoloŵezi zoipa cifukwa cotsatila malangizo a Yehova okhudza kusankha mabwenzi mwanzelu? Kodi tsopano ndimwe munthu wacimwemwe? (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33) Mwacidziŵikile, mwayankha kuti inde pa mafunso amenewa.

15. N’ciani cimene mungacite kuti mudziŵe mmene mungaseŵenzetsele mfundo za m’Baibo?

15 Nthawi zina, simungadziŵe moseŵenzetsela mfundo za m’Baibo zimene mukuphunzila. Ndiye cifukwa cake Yehova kupitila m’gulu lake, amapeleka zofalitsa zofotokoza Baibo zimene zingakuthandizeni kudziŵa coyenela na cosayenela. (Aheb. 5:13, 14) Pamene muŵelenga na kuphunzila zofalitsa zimenezi, mudzaona kuti mfundo zake n’zothandiza komanso mudzadziŵa mmene mungaziseŵenzetsele pa umoyo wanu. Ndipo mosakayikila izi zidzapangitsa kuti muyambe kufuna kugwilizana na gulu la Yehova.

16. Kodi Yehova wakhazikitsa dongosolo lotani pakati pa anthu ake?

16 Phunzilani kukonda gulu la Yehova na kulicilikiza. Yehova anakonza zakuti anthu ake akhale m’mipingo, ndipo Mwana wake, Yesu, ndiye mutu wa mipingo yonse imeneyi. (Aef. 1:22; 5:23) Yesu anasankha kagulu kocepa ka amuna odzozedwa kuti azitsogolela pa nchito yolalikila imene afuna kuti icitike masiku ano. Iye anakamba kuti kagulu ka amuna kameneka ni “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Kapolo ameneyu amakupatsani cakudya cauzimu na kukutetezani mwauzimu, ndipo sauona mopepuka udindo umenewu. (Mat. 24:45-47) Njila ina imene kapolo wokhulupilika amakusamalilani ni mwa kuonetsetsa kuti pali akulu oyenelela oti azikutsogolelani na kukutetezani. (Yes. 32:1, 2; Aheb. 13:17; 1 Pet. 5:2, 3) Akulu amacita zonse zotheka kuti akulimbikitseni na kukuthandizani kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova. Koma cina cofunika kwambili cimene amacita ni kukuthandizani kudziŵa mmene mungaphunzitsile ena za Yehova.—Aef. 4:11-13.

17. Malinga na Aroma 10:10, 13, 14, n’cifukwa ciani timauzako ena za Yehova?

17 Phunzitsani ena kukonda Yehova. Yesu anauza ophunzila ake kuti aziphunzitsa anthu za Yehova. (Mat. 28:19, 20) N’zotheka Mkhristu kugwila nchito imeneyi cabe cifukwa cakuti ni lamulo. Koma pamene cikondi canu pa Yehova cikukula, mudzayamba kumvela monga mmene mtumwi Petulo na mtumwi Yohane anamvelela, pamene anati: “Ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Kuthandiza munthu kuyamba kukonda Yehova ni cinthu cokondweletsa ngako. Ganizilani cabe cimwemwe cimene mlaliki Filipo anakhala naco atathandiza munthu wa ku Itiyopiya uja kumvetsetsa coonadi ca m’Malemba na kubatizika! Ngati mutengela citsanzo ca Filipo mwa kumvela lamulo la Yesu lakuti tizilalikila, mudzaonetsa kuti mufunadi kukhala Mboni ya Yehova. (Ŵelengani Aroma 10:10, 13, 14.) Mukamacita zimenezi, mosakayikila na imwe mudzafunsa funso ngati limene munthu wa ku Itiyopiya uja anafunsa lakuti: “Cikundiletsa kubatizidwa n’ciani?”—Mac. 8:36.

18. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 Kubatizika ni cosankha cacikulu kwambili cimene mungapange pa umoyo wanu. Popeza cosankha cimeneci n’cacikulu, mufunika kuganizila mosamala kwambili tanthauzo la ubatizo. Kodi muyenela kudziŵa ciani pa nkhani ya ubatizo? Kodi mufunika kucita ciani mukalibe kubatizika komanso pambuyo pobatizika? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

^ ndime 5 Anthu ena amene amakonda Yehova amakayikila ngati ni okonzeka kubatizika kuti akhale Mboni ya Yehova. Ngati umu ni mmene imwe mumamvelela, nkhani ino idzakuthandizani kuganizila zinthu zina zimene mufunika kucita kuti mukabatizike.

^ ndime 5 Popeza kuti anthu amasiyana-siyana, sikuti onse angacite zinthu zochulidwa m’nkhani ino potsatila mmene zayalidwila.

^ ndime 6 Kuti mupeze zitsanzo zina, onani mabulosha awa: Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? komanso yakuti Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo akugaŵila thilakiti kwa mtsikana amene wakumana naye pamene agula zinthu.