Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU

Kukumbukila Malemba

Kukumbukila Malemba

Kodi munavutikapo kukumbukila lemba limene mumakonda? Lembalo lingakhale limene limakutonthozani kapena kukuthandizani kugonjetsa maganizo olakwika. Mwina ndi limene munali kufuna kuuzako wina. (Sal. 119:​11, 111) Nazi njila zina zimene zingakuthandizeni kukumbukila malemba.

  • Gwilitsani nchito JW Library®. Pangani tag (tagi) a n’kuipatsa dzina lakuti “Malemba Apamtima.” Muziika malemba amene mufuna kukumbukila mu tagi imeneyi.

  • Ikani lembalo pamene mungamalione mosavuta. Mungalembe vesi limene mukufuna kumakumbukila pa pepala, n’kuika pepalalo pamalo amene mungalione kawilikawili. Ena amaika lembalo pafupi ndi galasi yodziyang’anilapo, ndipo enanso amaika pa citseko ca filiji. Ndipo ena amajambula cithunzi ca lembalo n’kuciika pa sikilini ya kompyuta yawo kapena pa foni.

  • Gwilitsani nchito pepala. Mungalembe lembalo kumbali imodzi ya pepala ndi kulemba mawu ake kumbali inayo. Yesani kuona mawuwo n’kukumbukila lembalo, kapena kuona lemba n’kukumbukila mawu ake, kapenanso mungaone mawuwo n’kuyesa kukumbukila kumene lembalo limapezeka m’Baibo.

a Kuti mudziwe zambili pa nkhani ya matagi, penyelelani vidiyo yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa​—Mfundo Zothandiza Poseŵenzetsa JW Library pa jw.org.