NKHANI YOPHUNZILA 30
NYIMBO 36 Titeteze Mitima Yathu
Maphunzilo Ofunika Amene Titengapo Kwa Mafumu Aciisiraeli
“Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sakumutumikila.”—MAL. 3:18.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Zimene Yehova anali kuyang’ana kwenikweni mwa mafumu aciisiraeli kuti tidziŵe zimene Yehova amayang’ananso mwa ife masiku ano pa nkhani ya kulambila.
1-2. Kodi Baibo imavumbula ciyani za mafumu ena aciisiraeli?
BAIBO imachula maina ya amuna oposa 40 amene anakhalapo mafumu mu Isiraeli. a Ndipo imatiuzanso mosapita m’mbali zinthu zimene ena a iwo anacita. Mwa citsanzo, ngakhale mafumu abwino anacitapo zinthu zoipa. Ganizilani citsanzo ca mfumu yabwino Davide. Ponena za iye, Yehova anati: “Davide mtumiki wanga . . . anasunga malamulo anga, kunditsatila ndi mtima wake wonse ndiponso kucita zinthu zoyenela zokhazokha pamaso panga.” (1 Maf. 14:8) Ngakhale n’telo, Davide anacita cigololo na mkazi wa mwini, ndipo anapanga ciwembu cakuti mwamuna wake aphedwe ku nkhondo.—2 Sam. 11:4, 14, 15.
2 Kumbali ina, panalinso mafumu ena ambili osakhulupilika amene anacitapo zinthu zabwino. Ganizilani citsanzo ca Rehobowamu. M’maso mwa Yehova, “iye anacita zoipa.” (2 Mbiri 12:14) Ngakhale n’conco, Rehobowamu anamvela lamulo la Mulungu lakuti mafuko 10 a Isiraeli acoke na kukapanga ufumu wawo. Anacitanso zinthu zopindulila anthu ake mwa kulimbitsa citetezo ca mizinda yawo.—1 Maf. 12:21-24; 2 Mbiri 11:5-12.
3. Kodi pamauka funso lofunika liti? Ndipo tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 Ganizilani funso lofunika ili: Ngati mafumu aciisiraeli anacita zabwino komanso zoipa, kodi Yehova anali kuyang’ana ciyani kuti agamule mfumu kukhala yokhulupilika kapena yosakhulupilika? Yankho la funso limeneli lidzatithandiza kudziŵa zimene Yehova amayang’ana mwa ife kuti tim’kondweletse. Tikambilane zinthu zitatu zimene Yehova anali kuyang’ana mwa mafumu aciisiraeli pofuna kudziŵa ngati mfumuyo inali yokhulupilika kapena ayi. Yehova anali kuyang’ana mtima wake, kulapa kwake, na kukangamila kwake pa kulambila koona.
IWO ANATUMIKILA YEHOVA NA MTIMA WATHUNTHU
4. N’ciyani cinasiyanitsa mafumu okhulupilika na mafumu osakhulupilika?
4 Mafumu amene anakondweletsa Yehova anali kum’lambila na mtima wonse. b Mfumu yabwino Yehosafati “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Mbiri 22:9) Ponena za Yosiya, Baibo imati: “Iye asanakhale mfumu, panalibe mfumu ina imene inabwelela kwa Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Maf. 23:25) Nanga bwanji za Solomo amene cakumapeto kwa moyo wake anayamba kucita zoipa? Iye “sanatumikile Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 11:4) Ndipo ponena za mfumu yosakhulupilika Abiya, Baibo imati iye “sanatumikile Yehova Mulungu wake ndi mtima wonse.”—1 Maf. 15:3.
5. Fotokozani tanthauzo la kutumikila Yehova na mtima wonse.
5 Nanga kodi kutumikila Yehova na mtima wonse kumatanthauza ciyani? Munthu wamtima wathunthu satumikila Mulungu mwamwambo cabe ayi. Koma amam’lambila cifukwa ca cikondi komanso kudzipeleka kwake. Kuwonjezela apo, iye amacitabe zimenezi kwa moyo wake wonse.
6. Tingatani kuti tizitumikila Yehova na mtima wathunthu? (Miyambo 4:23; Mateyu 5:29, 30)
6 Tingatengele bwanji zitsanzo za mafumu okhulupilika amene anatumikila Yehova na mtima wathunthu? Tizipewa zilizonse zimene zingatipangitse kukhala osakhulupilika kwa Yehova. Mwa citsanzo, tizisamala na zimene timaonelela na kumvetsela. Tizisamalanso posankha mabwenzi cifukwa angatipangitse kuyamba kukonda cuma. Tikazindikila kuti cinacake cikucepetsa cikondi cathu pa Yehova, ticitepo kanthu msanga-msanga kuti cisasokoneze ubwenzi wathu na iye.—Ŵelengani Miyambo 4:23; Mateyu 5:29, 30.
7. N’cifukwa ciyani m’pofunika kupewa zisonkhezelo zoipa?
7 Tisalole kuti mtima wathu ugawikane. Tikapanda kusamala, tingayambe kudzipusitsa n’kuganiza kuti ngati ticita zambili kuuzimu n’kosafunika kwenikweni kukhala osamala na zimene zingawononge ubwenzi wathu na Yehova. Yelekezani kuti mukuyenda pa msewu pomwe kukuwomba cimphepo komanso kwazizila kwambili. Pamene mwafika kunyumba, mukuyatsa mbaula kuti mumveko kuthuma. N’ciyani cingacitike ngati pamene mukuwotha motowo mwasiya citseko cosatseka? Mphepo yozizila ingaloŵe m’nyumba mwanu ndipo simungamvenso kuthuma. Tiphunzilapo ciyani? Tiyenela kucita zambili kuposa cabe pa kudya zakudya zauzimu zimene zimatithandiza kukhalabe pa ubwenzi wabwino na Yehova. Mofanana na citsanzo cija, nafenso tiyenela kutseka zitseko ku zisonkhezelo zoipa kotelo kuti “mpweya” woipa wa dzikoli kapena kuti kaganizidwe koipa kasaloŵe m’mitima mwathu na kuugaŵanitsa.—Aef. 2:2.
ANALAPA MACIMO AWO
8-9. Kodi Mfumu Davide na Mfumu Hezekiya anacita bwanji atadzudzulidwa? (Onani cithunzi .)
8 Monga taonela kuciyambi kwa nkhani ino, Mfumu Davide anacitapo macimo aakulu. Koma analapa modzicepetsa mneneli Natani atam’dzudzula. (2 Sam. 12:13) Timaona kuti analapadi poona zimene anakamba mu Salimo 51. Kulapa kwa Davide sikunali kwaciphamaso kungoti apusitse Natani kapena kuti apewe cilango ayi.—Sal. 51:3, 4, 17, tumawu twapamwamba.
9 Mfumu Hezekiya nayenso anacimwilapo Yehova. Baibo imati: “Mtima wake unayamba kudzikuza ndipo zimenezi zinacititsa kuti Mulungu amukwiyile iyeyo, Yuda ndiponso Yerusalemu.” (2 Mbiri 32:25) N’ciyani cinapangitsa Hezekiya kuti ayambe kudzikuza? Mwina anadziona kukhala wapamwamba cifukwa ca cuma cake, kugonjetsa kwake Asuri, kapenanso cifukwa cocilitsidwa mozizwitsa. Zioneka kuti kudzikuza n’kumene kunam’cititsa kuti aonetse anthu a ku Babulo cuma cake, zomwe pambuyo pake zinacititsa kuti mneneli Yesaya am’dzudzule. (2 Maf. 20:12-18) Koma Hezekiya analapa monga anacitila Davide. (2 Mbiri 32:26) Pamapeto pake, Yehova anamuona monga mfumu yokhulupilika imene ‘inacita zoyenela.’—2 Maf. 18:3.
10. Kodi Mfumu Amaziya anacita ciyani atapatsidwa uphungu?
10 Mosiyana na zimenezi, Mfumu Amaziya ya ku Yuda anacita zoyenela “koma osati ndi mtima wonse.” (2 Mbiri 25:2) Kodi analakwitsa ciyani? Yehova atam’thandiza kugonjetsa Aedomu, iye anayamba kulambila milungu yawo. c Pomwe mneneli wa Yehova anapita kukakambilana naye za nkhaniyi, iye modzikuza anakana kumvetsela kwa mneneliyo ndipo anam’pitikitsa.—2 Mbiri 25:14-16.
11. Malinga na 2 Akorinto 7:9, 11, tiyenela kucita ciyani kuti Yehova atikhululukile macimo athu? (Onaninso zithunzi.)
11 Kodi tiphunzilapo ciyani pa zitsanzozi? Tiyenela kulapa macimo athu na kucita zonse zotheka kuti tisawabweleze. Nanga bwanji ngati akulu mumpingo atipatsa uphungu ngakhale pa nkhani imene tiona kuti ni yaing’ono? Zikatelo, tisaganize kuti Yehova kapena akulu aleka kutikonda. Ngakhale mafumu abwino aciisiraeli nthawi zina anali kufunika kupatsidwa uphungu komanso cidzudzulo. (Aheb. 12:6) Tikapatsidwa uphungu, tiyenela (1) kuulandila modzicepetsa, (2) kupanga masinthidwe ofunikila, komanso (3) kupitilizabe kutumikila Yehova na mtima wathu wonse. Tikalapa macimo athu, Yehova adzatikhululukila.—Ŵelengani 2 Akorinto 7:9, 11.
IWO ANAKANGAMILABE PA KULAMBILA KOONA
12. N’ciyani maka-maka cinasiyanitsa mafumu okhulupilika na mafumu osakhulupilika?
12 Mafumu amene Yehova anaona kuti ni okhulupilika anali kum’lambila m’njila yoyenela. Ndipo analimbikitsanso anthu a mu ufumu wawo kucita cimodzimodzi. Komabe, nthawi zina iwo anali kulakwitsa zinazake monga mmene taonela. Koma anali odzipeleka kwa Yehova na mtima wawo wonse, ndipo anacita zonse zotheka kuti athetse kulambila mafano. d
13. N’cifukwa ciyani Yehova anagamula kuti Mfumu Ahabu inali yosakhulupilika?
13 Nanga bwanji za mafumu amene Yehova anagamula kuti ni osakhulupilika? Mwacionekele, pali zina zabwino zimene anacitapo. Mwa citsanzo, ngakhale mfumu yoipa Ahabu itamva kuti Naboti waphedwa cifukwa ca iye, inaonetsa kudzicepetsa ndipo anamva cisoni. (1 Maf. 21:27-29) Iye anamanganso mizinda na kugonjetsa adani a Isiraeli. (1 Maf. 20:21, 29; 22:39) Koma cifukwa cosonkhezeledwa na mkazi wake, iye analimbikitsa anthu a mu ufumu wake kulambila mafano. Ndipo sanaleke kucita zimenezi kwa moyo wake wonse.—1 Maf. 21:25, 26.
14. (a) N’ciyani cinacititsa Yehova kuona Mfumu Rehobowamu kuti ni wosakhulupilika? (b) Kodi mafumu osakhulupilika anali kufanana pa ciyani?
14 Tiyeni tikambilanenso za mfumu ina yosakhulupilika, Rehobowamu. Monga taonela kale, iye anacitapo zinthu zabwino pomwe anali kulamulila. Koma ufumu wake utakhala wolimba, iye anasiya kutsatila Cilamulo ca Yehova na kuyamba kulambila mafano. (2 Mbiri 12:1) Pambuyo pake iye anayamba kusintha-sintha, anali kucita kuti walambilako Yehova kenako walambilanso mafano. (1 Maf. 14:21-24) Panalinso mafumu ena kupatulapo Rehobowamu na Ahabu amene anapatuka pa kulambila koona. Mafumu ambili osakhulupilika anali kulambila milungu yonyenga, ndipo anali kulimbikitsanso ena kucita cimodzimodzi. Conco, n’zoonekelatu kuti kukangamila pa kulambila koona n’kumene Yehova anali kuonelapo kuti mfumu ni yabwino kapena yoipa.
15. N’cifukwa ciyani kukangamila pa kulambila koona n’kofunika kwambili kwa Yehova?
15 N’cifukwa ciyani nkhani ya kulambila inali yofunika kwambili kwa Yehova? Cifukwa mafumu ndiwo anali na udindo wotsogolela anthu awo pa kulambila koona. Kuwonjezela apo, kulambila mafano n’kumene kunali kutsogolela ena kucita macimo akulu-akulu, komanso kuti azicitila anzawo zopanda cilungamo. (Hos. 4:1, 2) Komanso, mafumu na anthu awo anali mu mtundu wodzipatulila kwa Yehova. Conco, Baibo imafananitsa kulambila mafano kwawo na kucita cigololo.(Yer. 3:8, 9). Munthu akacita cigololo, amalakwila mnzake wa mu ukwati, ndipo amam’khumudwitsa ngako. Mofananamo, mtumiki wa Yehova wodzipatulila akatengako mbali m’kulambila konyenga, amacimwila Yehova ndipo amam’khumudwitsa ngako. e—Deut. 4:23, 24.
16. N’ciyani maka-maka cimasiyanitsa anthu okhulupilika na osakhulupilika m’maso mwa Yehova?
16 Tingaphunzilepo ciyani? Tiyenela kukhala otsimikiza mtima kupewa ciliconse cogwilizana na kulambila konyenga. Koma tiyenelanso kulambila Yehova m’njila yoyenela na kukhalabe okangalika pom’tumikila. Mneneli Malaki anakamba momveka bwino zimene zimasiyanitsa munthu wabwino na munthu woipa m’maso mwa Yehova. Iye anati: “Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sakumutumikila.” (Mal. 3:18) Conco tisalole ciliconse, ngakhale kupanda ungwilo kwathu na zophophonya zathu, kutifooketsa mpaka kuleka kutumikila Mulungu. Kuleka kutumikila Yehova paiko kokha ni chimo lalikulu.
17. N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala posankha munthu wokamanga naye banja?
17 Ngati ndinu mbeta ndipo mukuganizila zokaloŵa m’banja, mungaone kuti mawu a Malaki onena za kutumikila Yehova amakhudzanso nkhani yosankha munthu woloŵa naye m’banja. N’zoona kuti iye angakhale na makhalidwe abwino, koma ngati munthuyo satumikila Yehova, kodi tinganene kuti ni munthu wokhulupilika m’maso mwa Yehova? (2 Akor. 6:14) Mukadzaloŵa m’banja, kodi munthuyo angadzakuthandizeni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova? Ganizilani za akazi acikunja a Mfumu Solomo. Iwo ayenela kuti anali na makhalidwe abwino, koma sanali kulambila Yehova. Ndipo pang’onom’pang’ono iwo anakopa mtima wa Solomo kuti ayambe kulambila mafano.—1 Maf. 11:1, 4.
18. Kodi makolo ayenela kuŵaphunzitsa ciyani ana awo?
18 Inu makolo, mungaseŵenzetse zitsanzo za mafumu a m’Baibo pothandiza ana anu kutumikila Yehova mokangalika. Athandizeni kumvetsa kuti Yehova anali kuona mfumu kuti ni yabwino kapena yoipa maka-maka poona zimene mfumuyo inacita polimbikitsa kulambila koona. Phunzitsani ana anu mwa mawu anu komanso citsanzo canu kuti zinthu zauzimu—monga kuŵelenga Baibo, kupezeka pa misonkhano, komanso kutengapo gawo pa nchito yolalikila—n’zofunika ngako kuposa zinthu zina zonse. (Mat. 6:33) Mukapanda kutelo, ana anu angafune kukhala Mboni za Yehova poona ngati ni cipembedzo ca banja. Zotsatila zake zingakhale zakuti, iwo angakankhile kumbuyo kulambila koona kapena kucisiyilatu coonadi.
19. Cotheka n’ciyani kwa aja omwe analeka kutumikila Yehova? (Onani danga lakuti “ N’zotheka Kubwelela kwa Yehova!”)
19 Munthu akaleka kutumikila Yehova, kodi n’zosatheka kukakhalanso bwenzi lake? N’zotheka ndithu, cifukwa angalape na kuyambanso kum’lambila. Kuti acite zimenezi ayenela kudzicepetsa na kulandila thandizo locokela kwa akulu mumpingo. (Yak. 5:14) Conco tiyenela kucita zonse zotheka kuti tibwezeletse ubwenzi wathu na Yehova.
20. Kodi Yehova adzationa motani tikatengela citsanzo ca mafumu okhulupilika?
20 Ndiye tingati taphunzila ciyani kwa mafumu aciisiraeli? Tingafanane na mafumu okhulupilika aja ngati tikhalabe odzipeleka na mtima wonse potumikila Yehova. Tiyenela kuphunzilapo kanthu pa zomwe talakwitsa, kulapa, komanso kupanga masinthidwe ofunikila. Ndipo tizikumbukila kufunika kolambila Mulungu woona yekhayo m’njila yovomelezeka. Mukakangamilabe kwa Yehova, iye adzakuonani kuti ndinu wolungama m’maso mwake.
NYIMBO 45 Kusinkha-sinkha kwa Mtima Wanga
a M’nkhani ino, mawu akuti “mafumu aciisiraeli” atanthauza mafumu onse amene analamulilapo anthu a Yehova, kaya analamulila mu ufumu wa mafuko aŵili wa Yuda, wa mafuko 10 wa Isiraeli, kapena mafuko onse 12.
b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Nthawi zambili Baibo imaseŵenzetsa mawu akuti “mtima” ponena munthu wamkati womwe umaphatikizapo zikhumbo za munthu, maganizo ake, mmene amaonela zinthu, zolakalaka zake, zolinga zake, komanso maluso ake.
c Zinali zofala kwa mafumu a mitundu ina kuyamba kulambila mafano ya mitundu imene agonjetsa.
d Mfumu Asa anacita macimo aakulu. (2 Mbiri 16:7, 10) Ngakhale n’telo, Baibo imakamba kuti iye anacita zoyenela m’maso mwa Yehova. Ngakhale kuti poyamba iye anakana uphungu, n’kutheka kuti pambuyo pake analapa. Yehova anaona zabwino zambili zimene iye anacita kuposa zoipa. Ndipo cofunika kwambili n’cakuti iye analambila Yehova yekhayo, ndipo anayesetsa mwamphamvu kuthetsa kulambila mafano mu ufumu wake.—1 Maf. 15:11-13; 2 Mbiri 14:2-5.
e N’zodziŵikilatu kuti malamulo aŵili oyambilila a m’Cilamulo ca Mose analetsa kulambila munthu kapena cinthu cina ciliconse kupatulapo Yehova.—Ex. 20:1-6.
f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu wacinyamata akuthandizila m’bale pa vuto lake la kamwedwe ka moŵa. M’baleyo walandila uphunguwo modzicepetsa, akuwongolela, ndipo akupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika.