NKHANI YOPHUNZILA 29
NYIMBO 121 Kudziletsa N’kofunika
Khalani Maso Kuti Musagonje pa Mayeselo
“Khalani maso ndipo mupitilize kupemphela kuti musaloŵe mʼmayeselo.”—MAT. 26:41.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Kufunika kopewa macimo, komanso zimene zingatitsogolele ku chimo.
1-2. (a) Kodi Yesu anawacenjeza za ciyani ophunzila ake? (b) Koma n’cifukwa ciyani ophunzilawo anathaŵa na kumusiya yekha? (Onaninso zithunzi.)
“ZOONA, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” a (Mat. 26:41b) Pokamba mawu amenewa, Yesu anaonetsa kuti amamvetsa kuti ndife opanda ungwilo, komanso kuti tingalakwitse zina zake. Koma mawu akewo analinso cenjezo lakuti tiyenela kupewa kudzidalila. Pamene Yesu ananena mawu amenewa, ophunzila ake anali atanenetsa modzitama usiku womwewo kuti sadzamusiya yekha Mbuye wawo. (Mat. 26:35) Iwo anali na colinga cabwino ponena mawu amenewa. Koma sanazindikile kuti angafooke mosavuta akakumana na mayeso. Ndiye cifukwa cake Yesu anawacenjeza kuti: “Khalani maso ndipo mupitilize kupemphela kuti musaloŵe m’mayeselo.”—Mat. 26:41a.
2 N’zacisoni kuti ophunzilawo analephela kukhalabe maso. Kodi Yesu atamangidwa, ophunzila ake anakhalabe naye kapena anacita mantha n’kuthaŵa? Cifukwa cakuti ophunzilawo sanakhalebe maso, zimene ananenetsa kuti sangacite n’zimene anacita. Anamuthaŵa Yesu na kumusiya yekha.—Mat. 26:56.
3. (a) N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa kudzidalila kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 Tisadzidalile m’pang’ono pomwe. N’zoona kuti sitifuna kucita ciliconse cokhumudwitsa Yehova. Ngakhale n’telo, ndife opanda ungwilo ndipo tingathe kugonjabe pa mayeselo. (Aroma 5:12; 7:21-23) Mosayembekezela, tingakumane na cocitika cimene cingatikope kuti ticite zosayenela. Kuti tikhalabe okhulupilika kwa Yehova na Mwana wake, tiyenela kutsatila ulangizi wa Yesu wakuti tizikhalabe maso ku mayeselo amene angaticimwitse. Nkhani ino itithandiza kucita zimenezi. Coyamba, tikambilane zinthu zimene tiyenela kusamala nazo kwambili. Kenako, tikambilane mmene tingakhalile maso kuti tisagonje pa mayeselo. Cothela, tikambilane mmene tingakhalile maso nthawi zonse.
ZINDIKILANI ZOFOOKA ZANU
4-5. N’cifukwa ciyani n’kofunika kupewa ngakhale macimo ang’ono-ang’ono?
4 Ngakhale macimo aang’ono angafooketse ubale wathu na Yehova. Ndipo angatitsogolele ku macimo akulu-akulu.
5 Tonsefe timakumana na mayeselo amene angaticimwitse. Koma aliyense wa ife payekha-payekha ali na mayeselo amene angamugonjetse mosavuta, mwina ni kukhotelela ku chimo lalikulu, kapena ku makhalidwe odetsa, kapenanso kutengela maganizo a dzikoli. Mwa citsanzo, wina angamalimbane na mayeselo ocita ciwelewele. Ndipo wina angamalimbane na mayeselo ocita makhalidwe odetsa, monga kudzipukusa kumalisece, kapena kuonela za malisece. Ndiponso wina angamalimbane na cofooka ca kuopa anthu, mzimu wosafuna kuuzidwa zocita, mtima wapacala, kapena cofooka ciliconse. Ndiye cifukwa cake Yakobo ananena kuti “munthu aliyense amayesedwa ndi cilakolako cake cimene cimamukopa ndi kumukola.”—Yak. 1:14.
6. Kodi tiyenela kukhala oona mtima pa ciyani?
6 Kodi mumazidziŵa zofooka zanu? Kungakhale kupanda nzelu kunyalanyaza zofooka zathu n’kumadzinamiza kuti sitingagonje ku mayeselo. (1 Yoh. 1:8) Kumbukilani kuti Paulo ananena kuti “amene ndi oyenelela mwauzimu,” angagonje ku mayeselo akapanda kukhalabe maso. (Agal. 6:1) Tizikhala oona mtima na kuvomeleza zofooka zathu.—2 Akor. 13:5.
7. Ni mbali ziti zimene tiyenela kuikapo cisamalilo cacikulu? Fotokozani citsanzo.
7 Kodi tiyenela kutani tikazindikila zofooka zathu? Tizicita zonse zotheka kuti tikhwimitse citetezo pa zofookazo! Mwa citsanzo, m’nthawi zochulidwa m’Baibo, mbali zimene zinali zofooka kwambili ku mpanda wa mzinda zinali mageti ake. Ndiye cifukwa cake pa mageti panali kuikidwa alonda ambili. Mofananamo, ifenso tiyenela kuika cisamalilo cacikulu pa mbali zimene tikudziŵa kuti ndife ofookelapo.—1 Akor. 9:27.
MMENE TINGAKHALILEBE MASO
8-9. Kodi mnyamata wa pa Miyambo caputa 7 anayenela kucita ciyani kuti apewe kucita chimo lalikulu? (Miyambo 7:8, 9, 13, 14, 21)
8 Kodi tingadziteteze bwanji ku mayeselo? Onani zimene tiphunzilapo kwa mnyamata wochulidwa pa Miyambo caputa 7. Iye anacita ciwelewele na hule imeneyo. Vesi 22 imakamba kuti “mwadzidzidzi” mnyamatayo anayamba kulondola mkaziyo. Koma monga mmene mavesi apambuyo aonetsela, mnyamatayo anacita zinthu zimene mwapang’ono-pang’ono zinam’tsogolela kucita chimo.
9 N’ciyani cinam’tsogolela kucita chimolo? Coyamba, cakumadzulo “iye ankadutsa mumsewu pafupi ndi mphambano [kumene kunali kukhala mkazi waciweleweleyo], ndipo ankalowela kunyumba ya mkaziyo.” (Ŵelengani Miyambo 7:8, 9.) Ndipo ataona mkaziyo sanamupewe. M’malo mwake, iye analola kuti mkaziyo amupsompsone, ndipo anamvetselanso pamene mkaziyo anali kufotokoza za nsembe zimene anapeleka. Mwina mkaziyo anafotokoza zimenezi kuti mnyamatayo amuone kuti ni munthu wabwino. (Ŵelengani Miyambo 7:13, 14, 21.) Mnyamatayo akanapewa zinthu zoipa zimene zinam’tsogolela kuti acimwe, akanadziteteza ku mayeselowo, komanso kuti asacite chimo.
10. Kodi munthu masiku ano angagwele bwanji m’chimo monga anacitila mnyamata wochulidwa m’buku la Miyambo?
10 Nkhani ya mnyamatayu itionetsa zimene zingacitikile mlambili aliyense wa Yehova. Aliyense angagwele m’chimo lalikulu, pambuyo pake n’kuganiza kuti chimolo linacitika “mwadzidzidzi.” Kapena anganene kuti, “Zinangocitika.” Koma akaganizila mofatsa zimene zinacitikazo, angazindikile kuti pali zina zimene sanasamale nazo zimene zinam’tsogolela ku chimo lalikulu. Zimenezo zingaphatikizepo kukhala na mabwenzi oipa, zosangalatsa zosayenela, komanso kupezeka pa malo olakwika nthawi zambili, kapena pa intaneti. Mwinanso iye analeka kupemphela, kuŵelenga Baibo, kusonkhana, komanso kutengako mbali mu nchito yolalikila. Monga zinacitikila kwa mnyamata wochulidwa m’buku la Miyambo, chimo la munthuyu sikuti linacitika mwadzidzidzi ayi, panali zinthu zina zimene zinam’tsogolela ku chimolo.
11. Tingacite ciyani kuti tipewe kugwela m’chimo?
11 Tiphunzilapo ciyani pa nkhaniyi? Tisapewe cabe kucita chimo, koma tipewenso zimene zingatitsogolele ku chimolo. Solomo anamveketsa bwino mfundo imeneyi pomwe anafotokoza za mnyamata na mkazi waciwelewele. Ponena za mkaziyo, Solomo ananena kuti: “Musasocele nʼkuyamba kuyenda mʼnjila zake.” (Miy. 7:25) Anapitiliza kunena za mkaziyo kuti: “Ukhale kutali kwambili ndi iye. Usayandikile pakhomo la nyumba yake.” (Miy. 5:3, 8) Inde, timadziteteza kuti tisagwele m’chimo popewa zilizonse zimene zingatitsogolele ku chimo. b Izi ziphatikizapo kupewa zinthu zimene mwa izo zokha si zolakwika kwa Akhristu, koma ngati tidziŵa kuti zingatitsogolele kucita chimo, tiyenela kuzipewa.—Mat. 5:29, 30.
12. Kodi Yobu anacita pangano lotani? Ndipo kucita izi kunam’thandiza bwanji? (Yobu 31:1)
12 Kuti tipewe zimene zingatitsogolele ku chimo, tiyenela kupanga cisankho mu mtima mwathu cakuti tizikhala osamala pocita zinthu. Izi n’zimene Yobu anacita. Iye anacita “pangano ndi maso” ake kuti azipewa kuyang’anitsitsa akazi ena mowakhumbila. (Ŵelengani Yobu 31:1.) Kusunga kwake pangano limeneli kunam’thandiza kupewa kucita chimo la cigololo. Nafenso tingacite bwino kukhala otsimikiza mtima kupewelatu ciliconse cimene cingatigwetsele m’mayeselo.
13. N’cifukwa ciyani tiyenela kuteteza maganizo athu? (Onaninso zithunzi.)
13 Tiyenelanso kuteteza maganizo athu. (Eks. 20:17) Anthu ena amaona kuti palibe vuto kuyelekezela kuti ukucita zinthu zoipa m’maganizo mwako, malinga ngati suzicitadi zinthuzo. Kaganizidwe kameneka n’kolakwika. Munthu amene amayelekeza zinthu zoipa, amakulitsa cikhumbo cofuna kucita zimene akuyelekezela m’maganizo ake. Pocita zimenezi, amakhala akudzikonzela yekha mayeselo amene amakhala ovuta kwambili kuwagonjetsa. N’zoona kuti nthawi zina maganizo olakwika angabwele m’maganizo mwathu. Cinsinsi cake ni kuwacotsa maganizo oipawo mwamsanga na kuyamba kuganizila zinthu zabwino. Kucita zimenezi sikudzapatsa mpata maganizo oipa kuti akule n’kukhala zilakolako zamphamvu zovuta kuzigonjetsa, zimenenso zingatsogolele ku chimo lalikulu.—Afil. 4:8; Akol. 3:2; Yak. 1:13-15.
14. N’ciyani cina cingatithandize kuti tisagwele m’mayeselo?
14 N’ciyaninso cimene tingacite kuti tidziteteze ku mayeselo? Tisakaikile ngakhale pang’ono kuti nthawi zonse timapindula tikatsatila malamulo a Yehova. Nthawi zina cingakhale covuta kwa ife kuganiza kapena kuona zinthu mmene Yehova akufunila. Koma ngati tiyesetsa mwakhama kucita zimenezi, tidzapeza mtendele wa mumtima.
15. Kodi kukhala na zokhumba zabwino kudzatiteteza bwanji ku mayeselo?
15 Tiziyesetsa kukhala na zokhumba zabwino. Tikayamba ‘kudana ndi coipa’ na ‘kukonda cabwino’ tidzakhala ofunitsitsa kucita zoyenela na kupewa zimene zinatitsogolela ku chimo. (Amosi 5:15) Zokhumba zabwino zimatipatsa mphamvu yokaniza mayeselo amene tingakumane nawo mosayembekezela kapena osapeweka.
16. Kodi kucita zinthu zauzimu kumatiteteza bwanji ku mayeselo? (Onaninso zithunzi.)
16 Tingacite bwanji kuti tikhale na zokhumba zabwino? Tiyenela kukhala okangalika mmene tingathele pocita zinthu zauzimu. Tikakhala pa misonkhano ya mpingo kapena mu ulaliki, timapewa mayeselo ambili. Ndiponso timakhala na mtima wofunitsitsa kukondweletsa Yehova. (Mat. 28:19, 20; Aheb. 10:24, 25) Tikamaŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha, timakulitsa mtima wofuna kucita zabwino, ndipo timadana na zoipa. (Yos. 1:8; Sal. 1:2, 3; 119:97, 101) Kumbukilani kuti Yesu anauza atumwi ake kuti: “Mupitilize kupemphela kuti musalowe mʼmayeselo.” (Mat. 26:41) Tikamapatula nthawi yokamba na Atate wathu wa kumwamba m’pemphelo, timakhala na mwayi wom’pempha kuti atithandize kukhala wofunitsitsa kucita zinthu zom’kondweletsa.—Yak. 4:8.
KHALANIBE MASO
17. Kodi Petulo anagonja kaŵili konse pa cofooka canji?
17 N’zotheka kugonjetsa zina mwa zofooka zathu. Koma zilipo zina zimene tingalimbane nazo kwa nthawi yaitali. Ganizilani zinacitika kwa mtumwi Petulo. Pa nthawi inayake iye anakana Yesu katatu cifukwa coopa anthu. (Mat. 26:69-75) Koma anaoneka ngati anali atawathetsa mantha amenewo pamene analalikila molimba mtima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. (Mac. 5:27-29) Komabe pambuyo pa zaka, iye kwakanthawi analeka kudya pamodzi na Akhristu a mitundu ina, ‘cifukwa ankaopa anthu odulidwa.’ (Agal. 2:11, 12) Mantha a Petulo anali atabwelelanso. N’kutheka kuti anali asanawathetseletu mantha amenewo.
18. N’ciyani cingaticitikile pa zofooka zathu zina?
18 Zaconco zingaticitikile nafenso. Motani? Cofooka cimene tinali kuona monga tinacithetsa, cingabwelelenso na kuyamba kutivutitsa. Mwa citsanzo, m’bale wina anavomeleza kuti: “N’naleka kuonelela zolaula kwa zaka 10, ndipo n’natsimikiza kuti vutolo linathelatu. Koma kwenikweni silinatheletu. Zinali ngati linali kungoyembekezela nthawi yabwino kuti lionekelenso.” Cosangalatsa n’cakuti iye sanagonje. Anazindikila kuti afunika kulimbana nalo vutolo tsiku lililonse, mwinanso kwa moyo wake wonse mu dongosolo lino la zinthu. Na thandizo la mkazi wake komanso akulu mu mpingo, iye anacita zonse zotheka kuti agwebane nalo vuto lake loonelela zolaula.
19. Kodi tiyenela kucita bwanji ngati tili na cofooka cosathelapo?
19 Tiyenela kucita ciyani kuti tigonjetse cofooka cosathelapo? Tizitsatila ulangizi wa Yesu pa nkhani ya mayeselo wakuti: “Khalanibe maso.” Ngakhale pa nthawi zimene mukumva kuti ndinu olimba, pewanibe malo kapena zinthu zimene zingakubweletseleni mayeselo. (1 Akor. 10:12) Limbikilanibe kucita zinthu zimene zinakuthandizani kugonjetsa cofooka cimeneco kumbuyoku. Miyambo 28:14 imakamba kuti: “Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake.”—2 Pet. 3:14.
MAPINDU AMENE TINGAPEZE TIKAKHALABE MASO
20-21. (a) Timapeza mapindu anji tikapitilizabe kudziteteza ku mayeselo? (b) Kodi Yehova adzaticitila ciyani tikacita mbali yathu? (2 Akorinto 4:7)
20 Tisakaikile zakuti kukhalabe maso polimbana na mayeselo kumatipindulila. Pocita chimo, ‘tingasangalale kwa nthawi yocepa,’ koma kutsatila miyeso ya Yehova kumatipatsa cimwemwe ceniceni. (Aheb. 11:25; Sal. 19:8) Izi zili conco cifukwa tinapangidwa kuti tizitsatila njila za Yehova. (Gen. 1:27) Tikatelo, tidzakhala na cikumbumtima coyela, komanso na ciyembekezo ca moyo wosatha.—1 Tim. 6:12; 2 Tim. 1:3; Yuda 20, 21.
21 Zoonadi, “thupi ndi lofooka.” Koma izi sizitanthauza kuti sitingacitepo kanthu pa zofooka zathu. Yehova amakhala wokonzeka kuti atipatse mphamvu zofunikila. (Ŵelengani 2 Akorinto 4:7.) Dziŵani kuti iye amapeleka mphamvu yoposa yacibadwa. Komabe, coyamba tiyenela kuseŵenzetsa mphamvu zathu zacibadwa kuti tidziteteze ku mayeselo a tsiku na tsiku. Tikacita mbali yathu, tiyeni tipemphele kwa Yehova kuti atipatse mphamvu yoposa yacibadwa. Ndipo sitikaikila kuti iye adzayankha mapemphelo athu. (1 Akor. 10:13) Inde, na thandizo la Yehova, tingadziteteze kuti tisagwele m’mayeselo.
NYIMBO 47 Pemphela kwa Yehova Tsiku na Tsiku
a KUFOTOKOZELA MAWU ENA: “Mzimu” wochulidwa pa Mateyo 26:41 ni mphamvu ili mwa ife yotipangitsa kumva kukhudzika mtima kapena kucita zimene tikufuna. “Thupi” liimilako kupanda ungwilo kwathu. Conco tingakhale na colinga cabwino cofuna kucita zoyenela, koma tikapanda kusamala, tingagonje ku mayeselo ocita zosemphana na Baibo.
b Munthu yemwe wacita chimo lalikulu angapeze thandizo m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! phunzilo 57 mfundo 1-3, komanso m’nkhani yakuti “Yang’anani Kutsogolo” mu Nsanja ya Mlonda ya November 2020, tsamba 27-29, ndime 12-17.
c MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale akuŵelenga lemba la tsiku m’maŵa, akuŵelenga Baibo pa nthawi yopuma ku nchito, ndipo ali pa msonkhano wa mkati mwa mlungu madzulo.