Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 31

Tiziyamikila Mwayi Wathu wa Pemphelo

Tiziyamikila Mwayi Wathu wa Pemphelo

Pemphelo langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu.”—SAL. 141:2.

NYIMBO 47 Pemphela kwa Yehova Tsiku na Tsiku

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi tikutipo bwanji Yehova potilola kupemphela kwa iye?

 TINAPATSIDWA mwayi wapadela kwambili wopemphela kwa Mlengi wakumwamba na dziko lapansi. Tangoganizani: Tingakhuthule za mu mtima mwathu kwa Yehova panthawi iliyonse komanso m’cinenelo ciliconse, popanda kupangana naye. Tingapemphele kwa iye tili odwala m’cipatala kapena tili m’ndende, pokhala na cidalilo cakuti Atate wathu wacikondi adzatimvela. Conco, mwayi umenewu sitiutenga mopepuka.

2. Kodi Mfumu Davide anaonetsa bwanji kuti anayamikila mwayi wa pemphelo?

2 Mfumu Davide anayamikila mwayi wa pemphelo. Iye anaimba kwa Yehova kuti: “Pemphelo langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu.” (Sal. 141:1, 2) M’nthawi ya Davide, zofukiza zopatulika zimene ansembe anali kugwilitsa nchito anali kuzikonza mosamala kwambili. (Eks. 30:34, 35) Pochula za zofukiza, Davide anatanthauza kuti anafunikila kusankha bwino mawu amene adzakamba kwa Atate wake wakumwamba m’pemphelo. Nafenso tiyenela kucita cimodzi-modzi. Timafuna kuti Yehova azikondwela na mapemphelo athu.

3. Kodi tiyenela kupemphela motani kwa Yehova? Nanga n’cifukwa ciyani?

3 Tikamapemphela kwa Yehova tizipewa kukamba momuzoloŵela kwambili. M’malo mwake, tiyenela kukamba naye na ulemu waukulu. Ganizilani masomphenya ocititsa cidwi amene Yesaya, Ezekieli, Danieli, na Yohane anaona. Masomphenyawo anali osiyana, koma ni ofanana pa cinthu cimodzi. Onse aonetsa kuti Yehova ni Mfumu yaikulu yaulemelelo. Yesaya anaona “Yehova atakhala pampando wacifumu wolemekezeka umene unali pamalo okwezeka.” (Yes. 6:1-3) Ezekieli anaona Yehova atakhala pa galeta lozungulilidwa na ‘kuwala kooneka ngati utawaleza.’ (Ezek. 1:26-28) Danieli anaona “Wamasiku Ambili” atavala zovala zoyela kwambili, ndipo mpando wake wacifumu unali kuyaka moto walawi-lawi. (Dan. 7:9, 10) Ndipo Yohane anaona Yehova atakhala pa mpando wacifumu wozungulilidwa na utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi. (Chiv. 4:2-4) Kuganizila ulemelelo wa Yehova wosayelekezeka, kumatikumbutsa kuti ni mwayi waukulu kupemphela kwa iye, komanso kuti popemphela tizilankhula naye mwaulemu. Koma kodi ni zinthu zimene tiyenela kupemphelela?

“KOMA INU MUZIPEMPHELA MOTELE”

4. Kodi tiphunzilapo ciyani pa mawu oyamba m’pemphelo lacitsanzo la pa Mateyu 6:9, 10?

4 Ŵelengani Mateyu 6:9, 10. Pa ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anaphunzitsa ophunzila ake mmene angapemphelele m’njila yokondweletsa Mulungu. Atakamba kuti “koma inu muzipemphela motele,” coyamba iye anachula zinthu zofunika zokhudza colinga ca Yehova. Zinthuzo ni kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu, kubwela kwa Ufumu umene udzawononga onse otsutsana na Mulunguyo, komanso madalitso akutsogolo amene iye wasungila mtundu wa anthu na dziko lapansi. Tikamachula zinthu zimenezi m’mapemphelo athu, timaonetsa kuti cifunilo ca Mulungu ndico cofunika kwa ife.

5. Kodi n’koyenela kupemphelela zokhudza ife eni?

5 Cotsatila, Yesu anaonetsa kuti tingapemphelelenso zokhudza ife eni. Tingamupemphe Yehova kuti atipatse cakudya calelo, atikhululukile zolakwa zathu, atiteteze kuti tisaloŵe m’mayeselo, komanso kuti atilanditse kwa woipayo. (Mat. 6:11-13) Tikamapempha Yehova zinthu zimenezi, timaonetsa kuti timam’dalila, komanso kuti tikufuna kuti iye atiyanje.

Ni zinthu ziti zimene mwamuna angachule akamapemphela na mkazi wake? (Onani ndime 6) *

6. Kodi zinthu zochulidwa m’pemphelo lacitsanzo ndizo zokha zimene tingapemphelele? Fotokozani.

6 Yesu sanatanthauze kuti otsatila ake popemphela azichula ndendende mawu a m’pemphelo lacitsanzo. M’mapemphelo ena amene iye anapeleka, anachula zinthu zosiyana-siyana zimene zinali kumudetsa nkhawa pa nthawiyo. (Mat. 26:39, 42; Yoh. 17:1-26) Mofananamo, tingapemphelele ciliconse cimene cikutidetsa nkhawa. Tikafunika kupanga cisankho pa nkhani inayake, tingapemphe nzelu kuti tikhale ozindikila. (Sal. 119:33, 34) Tikapatsidwa nchito yovuta, tingapemphe Mulungu kuti atithandize kudziŵa mocitila mwake. (Miy. 2:6) Makolo angapemphelele ana awo. Nawonso ana angapemphelele makolo awo. Ndipo tonsefe tingapemphelele maphunzilo athu a Baibo, komanso anthu amene timawalalikila. Komabe, popemphela tisamangopempha cabe thandizo kwa Yehova.

Kodi Yehova tingam’tamande na kumuyamikila m’mapemphelo athu pa zinthu ziti? (Onani ndime 7-9) *

7. N’cifukwa ciyani tiyenela kum’tamanda Yehova m’pemphelo?

7 Tizikumbukila kum’tamanda Yehova m’mapemphelo athu. Mulungu ndiye woyenela kulandila citamando kuposa aliyense. Iye ni “wabwino ndipo [ni] wokonzeka kukhululuka.” Cina, ni “wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Sal. 86:5, 15) Conco, tili na cifukwa cabwino cotamandila Yehova kaamba ka makhalidwe ake, komanso zimene amacita.

8. Kodi Yehova tingamuyamikile pa zinthu ziti? (Salimo 104:12-15, 24)

8 Kuwonjezela pa kum’tamanda Yehova m’mapemphelo athu, tiyenelanso kumuyamikila pa zabwino zimene amatipatsa. Mwacitsanzo, tingamuyamikile pa maluŵa amitundu-mitundu, zakudya zabwino zosiyana-siyana, komanso mabwenzi a pamtima otsitsimula. Atate wathu wacikondi amatipatsa zinthu zimenezi na zina zambili kuti tizikondwela. (Ŵelengani Salimo 104:12-15, 24.) Ndipo coposa zonse, timamuyamikila Yehova cifukwa ca cakudya cauzimu ca mwana alilenji cimene amatipatsa, ndiponso ciyembekezo cabwino ca zam’tsogolo.

9. N’ciyani cingatithandize kusaiŵala kumuyamikila Yehova? (1 Atesalonika 5:17, 18)

9 Tikhoza kuiŵala kumuyamikila Yehova pa zonse zimene amaticitila. Ndiye n’ciyani cingatithandize kuti tizikumbukila? Tingalembe mndandanda wa mapempho athu acindunji, ndipo nthawi na nthawi tiziona mmene Yehova watiyankhila. Kenako, timuyamikile pa thandizo lake. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:17, 18.) Ganizilani izi: Timakondwela na kuona kuti anthu amatikonda ngati atiyamikila. Mofananamo, tikakumbukila kumuyamikila Yehova cifukwa coyankha mapemphelo athu, iye amakondwela kwambili. (Akol. 3:15) Koma palinso cifukwa cina cofunika kwambili comuyamikilila Mulungu wathu.

TIZIYAMIKA YEHOVA CIFUKWA CA MWANA WAKE WOKONDEKA

10. Malinga na 1 Petulo 2:21, n’cifukwa ciyani tiyenela kumuyamikila Yehova potumiza Yesu padziko lapansi?

10 Ŵelengani 1 Petulo 2:21. Tiyenela kumuyamikila Yehova potumiza Mwana wake wokondeka kuti adzatiphunzitse. Tikamaphunzila za umoyo wa Yesu, timaphunzila zambili za Yehova, ndiponso zimene tingacite kuti tim’kondweletse. Ngati timakhulupilila nsembe ya Khristu, tingakhale pa ubale wabwino na Yehova Mulungu, na kukhala naye pamtendele.—Aroma 5:1.

11. N’cifukwa ciyani timapemphela m’dzina la Yesu?

11 Timamuyamikila Yehova potipatsa mwayi wopemphela kwa iye kupitila mwa Mwana wake. Yesu ndiye njila imene Yehova amagwilitsa nchito poyankha mapemphelo athu. Yehova amamvetsela na kuyankha mapemphelo amene timapeleka m’dzina la Yesu. Yesu anati: “Ciliconse cimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzacicita, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake.”—Yoh. 14:13, 14.

12. N’cifukwa ciyani timamuyamikila Yehova potipatsa Mwana wake?

12 Yehova amakhululuka macimo athu pa maziko a nsembe ya dipo la Yesu. Malemba amakamba kuti Yesu ni “mkulu wa ansembe [amene] wakhala pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wacifumu wa Wolemekezeka.” (Aheb. 8:1) Komanso, Yesu ni ‘mthandizi wathu amene ali ndi Atate.’ (1 Yoh. 2:1) Timamuyamikila kwambili Yehova potipatsa Mkulu wa Ansembe wacifundo amene amadziŵa kupeleŵela kwathu, komanso amene “amatilankhulila mocondelela kwa Mulungu.” (Aroma 8:34; Aheb. 4:15) Ndife opanda ungwilo. Conco, popanda nsembe ya Yesu sizikanatheka kupemphela kwa Yehova. Kukamba zoona, timacita kusoŵa mawu omuyamikila nawo Yehova cifukwa ca mphatso ya mtengo wapatali ya Mwana wake wokondeka!

TIZIWAPEMPHELELA ABALE NA ALONGO ATHU

13. Usiku wakuti maŵa aphedwa, kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwakonda ophunzila ake?

13 Usiku wakuti maŵa aphedwa, Yesu anapemphela kwa nthawi yaitali popemphelela ophunzila ake. Iye anapempha Atate wake kuti ‘awayang’anile [ophunzilawo] kuopela woipayo.’ (Yoh. 17:15) Apa Yesu anaonetsa kuti amawakonda ophunzila ake. Ngakhale kuti anali pafupi kukumana na mayeso akulu, iye anadela nkhawa atumwi ake.

Ni zinthu ziti zimene tingachule popemphelela abale na alongo athu? (Onani ndime 14-16) *

14. Tingaonetse bwanji kuti timawakonda abale na alongo athu?

14 Potengela citsanzo ca Yesu, tisamangoika maganizo pa zofuna zathu zokha. M’malo mwake, tizipemphelela abale na alongo athu nthawi zonse. Tikatelo, ndiye kuti tikutsatila lamulo la Yesu lakuti tizikondana, komanso timamuonetsa Yehova kuti okhulupilila anzathu timawakonda kwambili. (Yoh. 13:34) Kupemphelela abale na alongo athu kumawathandiza. Mawu a Mulungu amatiuza kuti “pembedzelo la munthu wolungama limagwila nchito mwamphamvu kwambili.”—Yak. 5:16.

15. N’cifukwa ciyani tiyenela kuwapemphelela alambili anzathu?

15 Tiyenela kupemphelela alambili anzathu cifukwa amakumana na mayeso ambili. Tingapemphe Yehova kuti awathandize kupilila matenda, ngozi zacilengedwe, nkhondo, mazunzo, kapena mavuto ena. Tingapemphelelenso abale na alongo amene amadzipeleka kugwila nawo nchito yothandiza pakacitika tsoka la zacilengedwe. Ngati mudziŵako ena amene akukumana na mavuto ngati amenewa, bwanji osachula maina awo m’mapemphelo anu a panokha? Tikamapempha Yehova kuti awathandize kupilila, timaonetsa kuti timawakondadi abale athu.

16. N’cifukwa ciyani tiyenela kuwapemphelela amene akutsogolela pakati pathu?

16 Otsogolela mu mpingo amayamikila tikamawachula m’mapemphelo athu, ndipo mapemphelowo amawathandiza. Mtumwi Paulo anadziŵa kuti anafunikila mapemphelo a ena. Anapempha Akhristu anzake kuti azimupemphelela nayenso. Iye anati: “Citani zimenezi kuti ndikatsegula pakamwa panga kuti ndilankhule, ndizitha kulankhula mwaufulu kuti ndidziwitse ena cinsinsi copatulika ca uthenga wabwino.” (Aef. 6:19) Masiku anonso, tili na abale ambili otsogolela pakati pathu amene amagwila nchito molimbika. Timaonetsa kuti timawakonda mwa kupempha Yehova kuti adalitse nchito yawo.

TIKAMAIMILAKO ENA M’PEMPHELO

17-18. Ni pa zocitika ziti pamene tingapemphedwe kuimilako ena m’pemphelo? Nanga tiyenela kukumbukila ciyani?

17 Nthawi zina, timapemphedwa kuti tiimileko ena m’pemphelo. Mwacitsanzo, mlongo amene akucititsa phunzilo la Baibo angapemphe mlongo mnzake kupeleka pemphelo. Popeza kuti mlongoyo angakhale kuti sakum’dziŵa bwino wophunzilayo, mwina iye angakonde kupeleka pemphelo lotsiliza pa phunzilolo. Izi zingam’patse mwayi wodziŵa zosoŵa za wophunzilayo zimene angachule m’pemphelo.

18 M’bale angapemphedwe kuti apemphele pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki, kapena pa msonkhano wa mpingo. Abale amene apatsidwa mwayi umenewu ayenela kukumbukila colinga ca msonkhanowo. Pemphelo siyenela kukhala njila yopelekela uphungu ku mpingo kapena zilengezo. Pa misonkhano yambili ya mpingo, mphindi 5 zimakhala za nyimbo na pemphelo. Conco, m’bale akapemphedwa kuti apemphele, sayenela kukamba “mawu ambili-mbili,” maka-maka kuciyambi kwa msonkhano.—Mat. 6:7.

TIZIONA PEMPHELO KUKHALA LOFUNIKA KWAMBILI PA UMOYO WATHU

19. N’ciyani cingatithandize kukonzekela tsiku la ciweluzo la Yehova?

19 Pamene tsiku la ciweluzo la Yehova likuyandikila, tiziona pemphelo kukhala lofunika kwambili pa umoyo wathu. Pa nkhaniyi, Yesu anati: “Cotelo khalani maso ndipo muzipemphela mopembedzela nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kucitika.” (Luka 21:36) Inde, kupemphela nthawi zonse kudzatithandiza kukhalabe maso mwauzimu kuti tsiku la Mulungu lisakatidzidzimutse.

20. Kodi tingacite ciyani kuti mapemphelo athu akhale ngati zofukiza za fungo lokoma?

20 Kodi taphunzila ciyani m’nkhani ino? Taphunzila kuti tiziyamikila kwambili mwayi wa pemphelo. Zinthu zofunika kwambili zimene tingapemphelele, ziyenela kukhala zokhudza colinga ca Yehova. Cina, tiyenela kuyamikila Mwana wa Mulungu na Ufumu wake, komanso kupemphelela alambili anzathu. Kuwonjezela apo, tingapemphelele zosoŵa za ife eni zakuthupi ndiponso zauzimu. Tikamaganizila mosamala zimene tidzakamba m’mapemphelo athu, timaonetsa kuti timayamikila mwayi wapadela kwambili wa pemphelo. Mawu athu adzakhala ngati zofukiza za fungo lokoma kwa Yehova, ndipo ‘adzam’sangalatsa.’—Miy. 15:8.

NYIMBO 45 Kusinkha-sinkha kwa Mtima Wanga

^ Timayamikila kwambili kuti Yehova anatipatsa mwayi wopemphela kwa iye. Timafuna kuti mapemphelo athu azikhala ngati zofukiza za fungo lokoma, kuti iye azikondwela nawo. M’nkhani ino, tikambilane zimene tingachule m’mapemphelo athu. Tikambilanenso mfundo zofunika kukumbukila tikapatsidwa mwayi woimilako ena m’pemphelo.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwamuna na mkazi wake akupemphelela mwana wawo kuti akhale wotetezeka kusukulu, thanzi la kholo lawo lokalamba, komanso wophunzila Baibo kuti apite patsogolo.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacinyamata akuyamikila Yehova kaamba ka nsembe ya dipo la Yesu, dziko lapansi malo athu okongola, komanso cakudya copatsa thanzi.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akupempha Yehova kuti adalitse Bungwe Lolamulila na mzimu woyela, athandize awo amene akhudzidwa na matsoka a zacilengedwe, komanso amene akukumana na mazunzo