Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 6

Kodi Baibo Imatiphunzitsanji za Mwiniwake wa Mawu a m’Bukulo?

Kodi Baibo Imatiphunzitsanji za Mwiniwake wa Mawu a m’Bukulo?

“Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.” —YER. 30:2.

NYIMBO 96 Buku Lake la Mulungu ni Cuma

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’cifukwa ciyani mumayamikila Mulungu kaamba ka Baibo?

 NDIFE oyamikila cotani nanga kwa Yehova Mulungu potipatsa Baibo! Kupitila m’Baibo, iye amatipatsa uphungu wanzelu umene ungatithandize kulimbana na mavuto amene timakumana nawo masiku ano. Watipatsanso ciyembekezo ca tsogolo labwino. Ndipo coposa zonse, Yehova anavumbula makhalidwe ake ambili kupyolela m’Baibo. Tikamasinkhasinkha makhalidwe ake abwino, mitima yathu imakopeka kuti tikhale pa ubwenzi wabwino na Mulungu wathu mwa kumuyandikila.—Sal. 25:14.

2. Kodi Yehova wadzidziŵitsa kwa anthu m’njila ziti?

2 Yehova amafuna kuti anthu amudziŵe. M’masiku akale, anali kuuza anthu zokhudza iye kupitila m’maloto, m’masomphenya, ngakhalenso mwa angelo. (Num. 12:6; Mac. 10:3, 4) Koma kodi zikanatheka bwanji kuti maloto, masomphenya, kapena mauthenga ocokela kwa angelo amenewa tiwaphunzile ngati sakanalembedwa? Ndiye cifukwa cake Yehova anauza amuna ‘kulemba m’buku’ zimene iye anafuna kuti tidziŵe. (Yer. 30:2) Popeza “njila ya Mulungu woona ndi yangwilo,” ndife otsimikiza kuti njila yolankhula nafe imeneyi ni yabwino koposa komanso yopindulitsa.—Sal. 18:30.

3. Kodi Yehova anaonetsetsa motani kuti Baibo yasungika mpaka lelo? (Yesaya 40:8)

3 Ŵelengani Yesaya 40:8. Mawu a Mulungu akhala akupeleka citsogozo cabwino kwa amuna na akazi okhulupilika kwa zaka masauzande. Kodi zimenezi zatheka bwanji? M’pomveka kufunsa funsoli, cifukwa Malembawo analembedwa kale-kale pa zolembapo zosakhalitsa. Conco, masiku ano kulibe mipukutu yake yoyambilila. Koma Yehova anaonetsetsa kuti akatswili akopela malemba opatulika. Ngakhale kuti akatswiliwo anali opanda ungwilo, iwo anakopela malembawo mosamala kwambili. Mwacitsanzo, ponena za Malemba a Ciheberi, katswili wina wa Baibo anakamba kuti: “Ndife otsimikiza kuti palibe buku lamakedzana limene analikopolola molondola kwambili kuposa Baibo.” Conco, ngakhale kuti Baibo inalembedwa kale-kalelo pa zolembapo zosakhalitsa, komanso kuti akatswili amene anakopela malemba anali opanda ungwilo, ndife otsimikiza kuti zimene timaŵelenga m’Baibo ni maganizo a Yehova, Mwiniwake wa Baibo.

4. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

4 Yehova ndiye Gwelo la “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yak. 1:7) Baibo ni imodzi mwa mphatso zabwino koposa zimene Yehova anatipatsa. Munthu akatipatsa mphatso, zimaonetsa kuti iye amatidziŵa bwino komanso amadziŵa zimene timafunikila. N’cimodzi-modzi na Mulungu amene anatipatsa Baibo. Tikamaiŵelenga timaphunzila zambili za Yehova. Timaphunzila kuti iye amatidziŵa bwino komanso zimene timafunikila. M’nkhani ino, tikambilane mmene Baibo imaonetsela makhalidwe atatu a Yehova amene ni nzelu, cilungamo, na cikondi. Koma coyamba, tiyeni tikambilane mmene Baibo imaonetsela nzelu za Mulungu.

MMENE BAIBO IMAONETSELA NZELU ZA MULUNGU

5. Ni njila ina iti imene Baibo imaonetsela nzelu za Mulungu?

5 Yehova amadziŵa kuti tifunikila uphungu wake wanzelu. Ndipo Baibo imene ni mphatso, ni yodzala na nzelu zake. Uphungu wa m’Baibo umathandiza anthu kwambili moti amasintha miyoyo yawo. Pamene Mose analemba mabuku oyambilila a m’Baibo, anauza anthu a Mulungu Aisiraeli kuti: “Amenewa si mawu opanda pake kwa inu, cifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu.” (Deut. 32:47) Amene anamvela mawu amenewa anakhala na moyo wopambana komanso wacimwemwe. (Sal. 1:2, 3) Ngakhale kuti Mawu a Mulungu analembedwa kale-kale kwambili, akali na mphamvu yosintha miyoyo ya anthu. Mwacitsanzo, mukafufuza pa jw.org, nkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” mudzapeza nkhani zoposa 50 pa zocitika zenizeni pa umoyo wa anthu. Nkhanizo zionetsa kuti Baibo yakhala ‘ikugwila nchito mwamphamvu kwambili mwa anthu okhulupilila’ masiku ano.—1 Ates. 2:13.

6. N’cifukwa ciyani tinganene kuti Baibo n’losiyana na mabuku ena onse?

6 Palibe buku lofanana na Mawu a Mulungu Baibo. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa Mwiniwake wa bukulo, Yehova Mulungu, ni wamphamvuzonse, wamuyaya, komanso wanzelu zosayelekezeka. Mabuku oculuka amakhala zaka zambili kuposa amene anawalemba, ndipo m’kupita kwa nthawi malangizo ake amatha nchito. Koma malangizo anzelu a m’Baibo sakutha nchito. Akhala othandiza kwa anthu kuyambila kale-kale mpaka pano. Tikamaŵelenga buku lopatulika limenelo na kusinkhasinkha zimene timaphunzilamo, Mwiniwake wa bukulo amatipatsa mzimu woyela kuti utithandize kuona mmene tingagwilitsile nchito uphungu wa m’Baibo pa umoyo wathu. (Sal. 119:27; Mal. 3:16; Aheb. 4:12) Ndithudi, Mwiniwake wa Baibo, ni wofunitsitsa kukuthandizani. Izi ziyenela kutilimbikitsa kuŵelenga Baibo nthawi zonse!

Kodi Baibo yawathandiza bwanji anthu a Yehova kukhala ogwilizana kuyambila kale mpaka masiku ano? (Onani ndime 7-8)

7. Kodi Baibo inathandiza bwanji anthu a Mulungu kukhala ogwilizana m’nthawi zakale?

7 Baibo imaonetsanso kuti Mulungu ni wanzelu cifukwa ca mmene imathandizila anthu a Mulungu kukhala ogwilizana. Pamene Aisiraeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, iwo anali kukhala m’madela osiyana-siyana. Ena anakhala asodzi, ena abusa, ndipo ena anakhala alimi. Cinali capafupi kwa Aisiraeli kuleka kusamala za Aisiraeli anzawo a kumadela ena. Komabe, Yehova anakonza zakuti Aisiraeli onse azisonkhana pamodzi pa zocitika zina kuti amvetsele pamene Mawu ake akuŵelengedwa na kufotokozedwa. (Deut. 31:10-13; Neh. 8:2, 8, 18) Tangoganizilani cimwemwe ca Mwisiraeli wokhulupilika akafika ku Yerusalemu, na kuona alambili anzake mwina ofika m’mamiliyoni, ocokela m’madela osiyana-siyana a dzikolo. Mwa kutelo, Yehova anali kuwathandiza anthu ake kukhala ogwilizana. Patapita nthawi, mpingo wacikhristu unakhazikitsidwa. Mu mpingomo munali amuna na akazi a zinenelo zosiyana-siyana, zikhalidwe zosiyana-siyana, olemela, komanso osauka. Koma cifukwa cakuti onse anali kukonda Malemba, iwo anakhala ogwilizana polambila Mulungu woona. Aja amene anakhala okhulupilila akanamvetsa Mawu a Mulungu kokha mwa thandizo la okhulupilila anzawo, komanso mwa kusonkhana nawo pamodzi.—Mac. 2:42; 8:30, 31.

8. Kodi Baibo imawathandiza bwanji anthu a Yehova masiku ano kukhala ogwilizana?

8 Mulungu wathu wanzelu akupitiliza kuthandiza anthu ake kukhala ogwilizana pogwilitsa nchito Baibo, imene ndilo gwelo la cakudya cauzimu cimene timalandila. Nthawi zambili timakumana pa misonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo kuti timvetsele pamene Malemba akuŵelengedwa na kufotokozedwa. Conco, Baibo ndiyo cida cacikulu cimene Yehova amaseŵenzetsa pothandiza anthu ake kuti ‘azim’tumikila mogwilizana.’—Zef. 3:9.

9. Ni khalidwe lofunika liti limene lingatithandize kumvetsa uthenga wa m’Baibo? (Luka 10:21)

9 Tiyeni tionenso umboni wina woonetsa nzelu za Yehova. Iye anapangitsa kuti Malemba ambili alembedwe m’njila yakuti anthu odzicepetsa okha ndiwo angathe kuwamvetsa. (Ŵelengani Luka 10:21.) Anthu kulikonse amaiŵelenga Baibo. Katswili wina wa Baibo anati, “Baibo ni buku limene anthu oculuka amaliŵelenga kwambili komanso mosamala kuposa buku lililonse.” Koma ni anthu odzicepetsa okha amene amaimvetsetsa Baibo na kugwilitsa nchito mfundo zake.—2 Akor. 3:15, 16.

10. Kodi Baibo imaonetsa nzelu za Yehova m’njila inanso iti?

10 Baibo imaonetsa nzelu za Yehova m’njila inanso. Yehova amagwilitsa nchito Malemba kuti atiphunzitse monga gulu, komanso kuti alangize na kutonthoza munthu aliyense payekha-payekha. Tonsefe tikamaŵelenga Baibo, timatha kuona kuti Yehova amacita cidwi na aliyense wa ife. (Yes. 30:21) Nthawi zambili mukakumana na vuto, kodi simumaloŵa m’Baibo na kuŵelenga lemba lokhala ngati anacita kulembela inu? Ngakhale n’telo, Baibo imathandiza anthu onse. Nanga zinatheka bwanji kuti ikhale na malangizo okuthandizani inuyo panokha pa zosoŵa zanu? Izi zinatheka cifukwa Mwiniwake wa Baibo ni wanzelu koposa m’cilengedwe conse.—2 Tim. 3:16, 17.

MMENE BAIBO IMAONETSELA CILUNGAMO CA MULUNGU

11. Kodi Mulungu anaonetsa bwanji kuti ni wopanda tsankho pamene Baibo inali kulembedwa?’

11 Cilungamo ni khalidwe linanso la Yehova. (Deut. 32:4) Khalidwe limeneli n’logwilizana kwambili na kupanda tsankho, ndipo Yehova sakondela. (Mac. 10:34, 35; Aroma 2:11) Kupanda tsankho kwake kumaonekela bwino tikaona zinenelo zimene anagwilitsa nchito polemba Baibo. Mabuku 39 oyambilila a m’Baibo analembedwa m’Ciheberi, cinenelo cimene anthu a Mulungu anali kumva mosavuta panthawiyo. Koma podzafika m’nthawi ya Akhristu oyambilila, Cigiriki cinakhala cinenelo cofala kwambili. Conco mabuku 27 othela a m’Baibo analembedwa m’Cigiriki. Yehova sanafune kuti Mawu ake alembedwe m’cinenelo cimodzi cokha ayi. Masiku ano, anthu pafupifupi 8 biliyoni padzikoli amakamba zinenelo zosiyana-siyana. Kodi zingatheke bwanji anthu ambili conco kuphunzila za Yehova?

12. Kodi Danieli 12:4 yakwanilitsika m’njila inanso iti masiku ano otsiliza?

12 Kudzela mwa mneneli Danieli, Yehova analonjeza kuti m’nthawi yamapeto anthu oculuka “adzadziŵa zinthu zambili zoona” zopezeka m’Baibo. (Ŵelengani Danieli 12:4.) Njila imodzi imene yathandiza anthu oculuka kuimvetsa Baibo, ni kupitila m’nchito yomasulila Baibo, na mabuku ofotokozela Baibo, kuwafalitsa, na kuwagaŵila kwa anthu. Baibo ni buku limene lamasulidwa m’zinenelo zambili na kufalitsidwa pa dziko lonse kuposa buku lina lililonse. Mabaibo omwe makampani amalonda amapulinta nthawi zina amakhala odula kwambili. Koma pofika pano, anthu a Yehova amasulila Mawu a Mulungu athunthu kapena mbali yake m’zinenelo zopitilila 240. Ndipo munthu aliyense akhoza kulipeza Baibo popanda kulipila. Cotulukapo n’cakuti anthu a mitundu yonse akumvetsela ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Mulungu wathu wacilungamo akupeleka mwayi kwa anthu ambili kuti amudziŵe mwa kuŵelenga Mawu ake. Akucita zimenezi cifukwa tonsefe amatikonda kwambili.

MMENE BAIBO IMAONETSELA CIKONDI CA MULUNGU

13. N’cifukwa ciyani tingakambe kuti Baibo imaonetsadi cikondi ca Yehova? (Yohane 21:25)

13 Baibo imaonetsa khalidwe lalikulu limene Mwinawake ali nalo, khalidwe la cikondi. (1 Yoh. 4:8) Ganizilani zimene Yehova analemba m’Baibo na zimene sanalembe. Iye anatipatsa malangizo omwe tikufunikila kuti tikhale naye pa ubale wabwino, kuti tikhale acimwemwe tsopano, komanso kuti tikapeze moyo wosatha. Komabe, cifukwa Yehova amatikonda, iye sanatiunjikile malamulo ambili-mbili ovuta kuwatsatila.—Ŵelengani Yohane 21:25.

14. Ni njila inanso iti imene Baibo imaonetsela cikondi ca Mulungu?

14 Yehova amaonetsanso kuti amatikonda polankhula nafe m’Baibo m’njila imene imatilemekeza. Iye sanaikemo malamulo ambili-mbili, kapena kutitsogolela pa kalikonse komwe tingacite pa moyo wathu. M’malo mwake, iye anaikamo zitsanzo zenizeni za anthu, maulosi ocititsa cidwi, komanso uphungu wanzelu wotithandiza kupanga zisankho zabwino. Pa cifukwa cimeneci, Baibo imatisonkhezela kum’konda Mulungu na kumumvela kucokela pansi pa mtima.

N’cifukwa ciyani tiyenela kusinkhasinkha mmene Yehova anacitila na atumiki ake akale? (Onani ndime 15)

15. (a) Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti amasamala za anthu amene amaŵelenga Mawu ake? (b) Malinga na cithunzi ici, kodi kamtsikana aka, m’bale wacinyamata uyu, komanso mlongo wacikulile uyu akusinkhasinkha anthu ati ochulidwa m’Baibo? (Gen. 39:1, 10-12; 2 Maf. 5:1-3; Luka 2:25-38)

15 Baibo imaonetsa kuti Yehova amasamala kwambili za ife. Motani? M’mawu ake muli nkhani zoonetsa mmene anthu amamvela. Tingathe kumvetsa mmene anthuwa anali kumvela cifukwa iwonso anali ‘anthu monga ife tomwe.’ (Yak. 5:17) Coposa zonse, tikaona mmene Mulungu anali kucitila zinthu na anthuwo, timafika pomvetsa bwino kuti “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.”—(Yak. 5:11)

16. Kodi tiphunzila ciyani za Yehova tikamaŵelenga nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo amene anam’cimwila? (Yesaya 55:7)

16 Baibo imaonetsa cikondi ca Yehova m’njila inanso. Malemba amatsimikizila kuti Mulungu wathu sadzatisiya tikalakwa. Mwacitsanzo, Aisiraeli anacimwila Yehova mobweleza-bweleza. Koma iwo akalapa mocokela pansi pa mtima Mulungu anali kuwakhululukila. (Ŵelengani Yesaya 55:7.) Nawonso Akhristu a m’zaka za zana loyamba anali kudziŵa kuti Mulungu amawakonda. Mtumwi Paulo mouzilidwa analimbikitsa Akhristu anzake kuti munthu amene anacita chimo lalikulu uja koma analapa, ‘amukhululukile na mtima wonse na kum’tonthoza.’ (2 Akor. 2:6, 7; 1 Akor. 5:1-5) N’zolimbikitsa kuti Yehova sanasiye alambili ake cabe cifukwa anam’cimwila. M’malo mwake, mwacikondi anawathandiza, kuwaongolela, na kuwalandilanso m’manja mwake. Iye akulonjeza kuti adzacitanso cimodzi-modzi kwa onse ocimwa amene amalapa masiku ano.—Yak. 4:8-10.

MUZIYAMIKILA “MPHATSO YABWINO” YA MAWU A MULUNGU

17. N’cifukwa ciyani Baibo ni mphatso yapadela?

17 Yehova watipatsa mphatso yabwino ngako. N’cifukwa ciyani Mawu ake ni apadela kwambili? Monga taphunzilila, Baibo imaonetsa nzelu za Mulungu, cilungamo cake, na cikondi cake. Bukuli limatitsimikizila kuti Yehova amafuna kuti tifike pom’dziŵa bwino. Amafuna tikhale mabwenzi ake.

18. Tingaonetse bwanji kuti timamuyamikila Yehova pa “mphatso yabwino” ya Baibo?

18 Tisaione mopepuka “mphatso yabwino” imeneyi ya Mawu a Mulungu. (Yak. 1:17) Tiyeni tipitilize kuyamikila Mulungu kaamba ka mphatso imeneyi. Tingatelo mwa kuŵelenga mawu ake opatulika na kuwasinkhasinkha. Pamene tikucita zimenezi, tingakhale otsimikiza kuti Mwiniwake wa mawuwo adzadalitsa kuyesetsa kwathu, komanso kuti tidzafika ‘pomudziŵadi Mulungu’.—Miy. 2:5.

NYIMBO 98 Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu

a Baibo imatithandiza kumuyandikila Yehova. Kodi tingaphunzile ciyani m’buku lopatulika limenelo zokhudza nzelu za Mulungu, cilungamo cake, na cikondi cake? Zimene timaphunzila zingatithandize kukulitsa ciyamikilo cathu pa Mawu a Mulungu. Zingatithandizenso kuona kuti Baibo ilidi mphatso yocokela kwa Atate wathu wakumwamba.