NKHANI YOPHUNZILA 6
Kodi Mumakhulupilila Mmene Yehova Amacitila Zinthu?
“Iye ndi Thanthwe, ndipo nchito yake ndi yangwilo, njila zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”—DEUT. 32:4.
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
ZIMENE TIKAMBILANE *
1-2. (a) N’cifukwa ciani anthu ambili cimawavuta kukhulupilila anthu audindo? (b) Nanga tikambilane ciani m’nkhani ino?
MASIKU ano, anthu ambili cimawavuta kukhulupilila anthu audindo. Izi zili conco cifukwa aona kuti a zamalamulo komanso maboma amakondela anthu olemela komanso amphamvu, ndipo amapondeleza osauka. Baibo inakamba zoona kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.” (Mlal. 8:9) Kuwonjezela apo, atsogoleli ena acipembedzo amacita zoipa. Izi zapangitsa kuti anthu ena aleke kukhulupilila Mulungu. Conco, munthu akavomela kuphunzila nafe Baibo, timakhala na nchito yom’thandiza kukhulupilila Yehova, komanso kudalila anthu omuimilako padziko lapansi.
2 Anthu amene timaphunzila nawo Baibo, si ndiwo okha ayenela kuphunzila kukhulupilila Yehova na gulu lake. Ngakhale ife amkhalakale m’coonadi, tiyenela kupitiliza kukhulupilila kuti njila ya Yehova yocitila zinthu imakhala yabwino koposa nthawi zonse. Nthawi zina, kukhulupilila kwathu Mulungu kungayesedwe pa nkhaniyi. M’nkhani ino, tikambilane mbali zitatu zimene zingaike cikhulupililo cathu pa mayeso: (1) tikamaŵelenga nkhani zina m’Baibo, (2) tikalandila malangizo ocokela ku gulu la Yehova, komanso (3) tikadzakumana na zovuta kutsogolo.
KHULUPILILANI YEHOVA PAMENE MUŴELENGA BAIBO
3. Tikamaŵelenga nkhani zina m’Baibo, kodi cikhulupililo cathu mwa Yehova cingayesedwe motani?
3 Pamene tiŵelenga Baibo, tingakhale na mafunso okhudza mmene Yehova anacitila zinthu na anthu ŵena, na zisankho zimene iye anapanga. Mwacitsanzo, m’buku la Numeri, timaŵelenga kuti Yehova anaweluza kuti Mwisiraeli wina aphedwe cifukwa cotola nkhuni pa Sabata. Koma patapita zaka, m’buku la Samueli waciŵili timaphunzila kuti Yehova anakhululukila Mfumu Davide atacita cigololo, komanso kupha munthu. (Num. 15:32, 35; 2 Sam. 12:9, 13) Mwina tingafunse kuti, ‘N’cifukwa ciani Yehova anakhululukila Davide atacita cigololo komanso kupha munthu, koma anaweluza kuti munthu aphedwe pa chimo looneka laling’ono?’ Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione zinthu zitatu zimene tiyenela kukumbukila tikamaŵelenga Baibo.
4. Kodi Genesis 18:20, 21 komanso Deuteronomo 10:17, imatithandiza bwanji kukhulupilila kwambili zigamulo za Yehova?
4 Si nthawi zonse pamene Baibo imafotokoza zonse zokhudza nkhani. Mwacitsanzo, tidziŵa kuti Davide analapa macimo ake mocokela pansi pa mtima. (Sal. 51:2-4) Koma bwanji za munthu amene anaphwanya lamulo la Sabata? Kodi iye anali munthu wotani? Kodi anamva cisoni pa zimene anacita? Kodi anaphwanyapo malamulo a Yehova kumbuyoko? Kodi ananyalanyazapo macenjezo, ngakhale kuwakana? Baibo sikamba. Komabe, ndife otsimikiza za mfundo iyi: Yehova “sacita cosalungama.” (Deut. 32:4) Iye amazika zigamulo zake pa zoona zake za nkhaniyo, osati pa mpekesela, tsankho, kapena zinthu zina zimene nthawi zambili zimapangitsa anthu kupotoza cilungamo. (Ŵelengani Genesis 18:20, 21; Deuteronomo 10:17.) Tikamaphunzila zambili za Yehova na miyezo yake, m’pamenenso timakhulupilila kwambili ziweluzo zake. Ngakhale kuti tingakhale na mafunso pambuyo poŵelenga nkhani ina yake m’Baibo, amene pali pano sitingapeze mayankho ake, tidziŵa kuti Mulungu wathu “ndi wolungama m’njila zake zonse.”—Sal. 145:17.
5. Kodi kupanda ungwilo kumasokoneza bwanji kaonedwe kathu pa nkhani ya cilungamo? (Onaninso bokosi lakuti, “ Kupanda Ungwilo Kungasokoneze Kaonedwe Kathu pa Nkhani ya Cilungamo.”)
5 Nthawi zina, tingaweluze nkhani molakwika cifukwa ca kupanda ungwilo. Popeza Mulungu anatilenga m’cifanizilo cake, timafuna kuti anthu azicitilidwa zinthu mwacilungamo. (Gen. 1:26) Koma cifukwa copanda ungwilo, tingaone zinthu molakwika cifukwa coganiza kuti tikudziŵa zonse pa nkhaniyo. Mwacitsanzo, Yona sanakondwele pamene Yehova anasankha kucitila cifundo anthu a ku Nineve. (Yona 3:10–4:1) Koma onani zinacitika. Cifukwa cowacitila cifundo, Anineve olapa oposa 120,000 anapulumuka. Potsilizila pake, tiona kuti Yona ndiye anaweluza molakwika anthuwo, osati Yehova.
6. N’cifukwa ciani Yehova sayenela kucita kutifotokozela zifukwa zimene wapangila cigamulo?
6 Yehova safunika kucita kufotokozela anthu zifukwa zimene wapangila zisankho. N’zoona kuti kumbuyoko analola atumiki ake kufotokoza mmene iwo anamvelela pa zigamulo zimene iye anapanga, kapena zimene anali kufuna kupanga. (Gen. 18:25; Yona 4:2, 3) Ndipo nthawi zina, anali kufotokoza zifukwa zimene anapangila cigamulo cina cake. (Yona 4:10, 11) Komabe, Yehova safunika kucita kutifotokozela zifukwa zake. Pokhala Mlengi wathu, safunika civomelezo cathu asanacite cina cake, kapena pambuyo pocita cinthuco.—Yes. 40:13, 14; 55:9.
KHULUPILILANI YEHOVA MUKALANDILA MALANGIZO
7. N’ciani cingakhale covuta kwa ife? Nanga n’cifukwa ciani?
7 Timavomeleza na mtima wonse kuti Yehova amacita cilungamo nthawi zonse. Koma cimene cingativute, mwina ni kukhulupilila anthu omuimila. Tingayambe kukaikila ngati aja amene ali na udindo m’gulu la Mulungu, amayendetsadi zinthu motsatila malangizo a Yehova kapena maganizo awo. N’kutheka kuti anthu ena ochulidwa m’Baibo anali kuona zinthu mwanjila imeneyi. Ganizilani zitsanzo zimene tachula m’ndime 3. M’bale wake wa munthu amene anaphwanya lamulo la Sabata, mwina anakaikila ngati Mose anafunsiladi kwa Yehova asanapeleke ciweluzo cakuti munthuyo aphedwe. Ndipo bwenzi la Uriya Mhiti, amene mkazi wake anacita cigololo na Davide, mwina anaganiza kuti Davide anaseŵenzetsa mphamvu zake monga mfumu kupewa cilango cimene anayenela kulandila. Yehova amakhulupilila aja amene wasankha kuti atsogolele m’gulu lake komanso mu mpingo. Conco, ngati sitiwakhulupilila anthuwo, ndiye kuti sitimukhulupilila Yehova.
8. Kodi zimene zachulidwa pa Machitidwe 16:4, 5, zifanana bwanji na mmene mpingo wacikhristu umagwilila nchito masiku ano?
8 Masiku ano, Yehova amatsogolela gulu lake padziko lapansi kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Mofanana na bungwe lolamulila la m’nthawi ya atumwi, kapoloyu amayang’anila anthu a Mulungu padziko lonse, na kupeleka malangizo kwa akulu. (Ŵelengani Machitidwe 16:4, 5.) Naonso akulu amatsatila malangizo amenewo m’mipingo. Ngati timalabadila malangizo a gulu komanso a akulu, timaonetsa kuti timakhulupilila mmene Yehova amacitila zinthu.
9. Ni pa zocitika zotani pamene cingativute kuvomeleza cigamulo ca akulu? Nanga n’cifukwa ciani?
9 Nthawi zina, cingativute kuvomeleza zigamulo za akulu. Mwacitsanzo, m’zaka zaposacedwa, mipingo yambili aiphatikiza pamodzi, ndipo izi zapangitsa kuti mipingo ina iloŵe m’dela lina. Ndipo akulu apempha ofalitsa ena kusamukila ku mpingo wina, kuti Nyumba za Ufumu zizigwilitsidwa nchito mokwanila. Akatipempha kusamukila ku mpingo watsopano, cingativute kusiya mabwenzi athu na acibale. Kodi akulu amalandila malangizo mwacindunji kucokela kwa Mulungu owauza mpingo kumene wofalitsa aliyense ayenela kupitako? Ayi. Pa cifukwa cimeneci, cingakhale covuta kutsatila malangizo amene tapatsidwa. Koma Yehova amawakhulupilila akuluwo kuti adzapanga zigamulo zoyenela. Nafenso tiziwakhulupilila. *
10. Malinga na Aheberi 13:17, n’cifukwa ciani tiyenela kucilikiza akulu pa zigamulo zawo?
10 N’cifukwa ciani tiyenela kugwilizana na akulu, na kucilikiza zigamulo zawo ngakhale kuti sitinazikonde? Cifukwa kucita zimenezo, kumathandiza kusungitsa mtendele pakati pa anthu a Mulungu. (Aef. 4:2, 3) Mpingo umapita bwino patsogolo, ngati onse modzicepetsa amacilikiza zigamulo za bungwe la akulu. (Ŵelengani Aheberi 13:17.) Coposa zonse, timaonetsa Yehova kuti timam’khulupilila tikamagwilizana na aja amene iye wasankha kuti atiyang’anile.—Mac. 20:28.
11. N’ciani cingatithandize kudalila kwambili citsogozo ca akulu?
11 Cimene cingatithandize kudalila kwambili citsogozo ca akulu, ni kukumbukila kuti iwo amapempha mzimu woyela akamakambilana nkhani zokhudza mpingo. Amapendanso mosamala mfundo zothandiza za m’Baibo, na kufufuza malangizo a gulu la Yehova. Iwo amafuna kukondweletsa Yehova, na kupeleka cisamalilo cabwino koposa kwa anthu ake. Amuna okhulupilika amenewa, amadziŵa kuti adzayankha mlandu kwa Mulungu mmene amasamalila maudindo awo. (1 Pet. 5:2, 3) Ganizilani izi: M’dzikoli logaŵikana cifukwa ca mitundu, zipembedzo, komanso ndale, anthu a Yehova ni ogwilizana pa kulambila Mulungu yekha woona. Izi zatheka cifukwa Yehova akudalitsa gulu lake.
12. Kodi akulu amayang’ana ciani kuti adziŵe ngati munthu ni wolapadi?
12 Yehova anapatsa akulu udindo waukulu kwambili wosunga mpingo kukhala woyela. Ngati Mkhristu wacita chimo lalikulu, Yehova amafuna kuti akulu aipende mosamala nkhaniyo, na kuona ngati munthuyo angakhalebe mu mpingo. Mwa zina, ayenela kuona ngati munthuyo ni wolapadi zenizeni pa zimene anacita. Iye angakambe kuti ni wolapa, koma kodi amadanadi na zimene anacitazo? Kodi watsimikiza mtima kuti sadzabwelezanso chimolo? Koma ngati kuyanjana na anthu osayenela ndiko kunam’pangitsa kuti agwele m’chimolo, kodi ni wokonzeka kudula mayanjano ake na anthu amenewo? Akulu amapemphela kwa Yehova, amaganizila zimene Baibo imakamba pa nkhaniyo, ndipo amaona mmene wolakwayo akumvelela pa zimene anacita. Ndiyeno, amagamula ngati iye angakhalebe mu mpingo. Nthawi zina, wolakwayo angafunike kucotsedwa mu mpingo.—1 Akor. 5:11-13.
13. Kodi tingakhale na maganizo otani ngati bwenzi lathu kapena wacibale wathu wacotsedwa mu mpingo?
13 Kodi kukhulupilila kwathu akulu kungayesedwe motani? Ngati amene wacotsedwa si bwenzi lathu la pamtima kapena wacibale wathu, m’posavuta kucilikiza cigamulo ca akulu. Koma bwanji ngati amene wacotsedwa ni bwenzi lathu la pamtima. Mwina tingaganize kuti akulu sanapende mfundo zonse zokhudza mlanduwo, kapena tingaone kuti iwo sanauweluze bwino kusiyana na mmene Yehova akanaweluzila. N’ciani cingatithandize kulemekeza cigamulo cimeneco?
14. N’ciani cingatithandize kuona zinthu moyenela akulu akagamula kuti bwenzi lathu kapena wacibale wathu acotsedwe mu mpingo?
14 Tizikumbukila kuti kucotsa munthu mu mpingo ni makonzedwe a Yehova, ndipo amapindulitsa mpingo, ngakhale wolakwayo. Ngati munthu wosalapa aloledwa kukhalabe mu mpingo, khalidwe lake loipalo lingayambukile ena. (Agal. 5:9) Kuwonjezela apo, sangaone kukula kwa chimo lake. Ndiponso, sadzakhala na comulimbikitsa kuti awongolele maganizo ake na zocita zake kuti Yehova amuyanjenso. (Mlal. 8:11) Tisakaikile konse mfundo yakuti akulu satenga udindo wawo mopepuka akamapenda zakuti munthu ayenela kucotsedwa kapena ayi. Mofanana na oweluza ku Isiraeli wakale, nawonso akulu amadziŵa kuti ‘saweluzila munthu koma amaweluzila Yehova.’—2 Mbiri 19:6, 7.
KUKHULUPILILA YEHOVA PALI PANO KUMATIKONZEKELETSA ZAM’TSOGOLO
15. N’cifukwa ciani tiyenela kudalila malangizo a Yehova pali pano kuposa n’kale lonse?
15 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, tizikhulupilila kwambili mmene Yehova amacitila zinthu kuposa kale lonse. Cifukwa ciani? Cifukwa pa cisautso cacikulu, mwina tingadzalandile malangizo ooneka acilendo, osathandiza, kapena ovuta kuwatsatila. Yehova sadzacita kukamba nafe iye mwini. Mwacionekele, iye adzapeleka malangizowo kupitila mwa anthu osankhidwa omuimilako. Imeneyo sidzakhala nthawi yoyamba kukaikila malangizowo n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi malangizo aya acokeladi kwa Yehova, kapena abale amene akutsogolela angowapanga pa iwo okha?’ Kodi mudzakhulupilila Yehova na gulu lake panthawi yovuta imeneyo? Ngati pali pano timakhulupilila malangizo amene timalandila na kuwatsatila na mtima wonse, tidzakacitanso cimodzi-modzi pa cisautso cacikulu.—Luka 16:10.
16. Kodi posacedwa tingadzayesedwe motani pa nkhani ya kukhulupilila ciweluzo ca Yehova?
16 Palinso mbali ina imene tiyenela kuiganizila. Mbali imeneyo ni yokhudza ciweluzo ca Yehova pamapeto a dzikoli. Pali pano, timakhala na ciyembekezo cakuti anthu amene satumikila Yehova, kuphatikizapo acibale athu, adzalabadila na kusankha kum’tumikila mapeto asanafike. Koma pa Aramagedo, Yehova kupitila mwa Yesu, adzapeleka ciweluzo cimene cidzakhudza tsogolo lawo. (Mat. 25:31-33; 2 Ates. 1:7-9) Sudzakhala udindo wathu kusankha amene ayenela kucitilidwa cifundo na Yehova kapena kuwonongedwa. (Mat. 25:34, 41, 46) Nthawiyo ikadzafika, kodi tidzalemekeza ciweluzo ca Yehova, kapena kodi tidzaleka kum’tumikila cifukwa cosagwilizana na ciweluzo cake? Kunena zoona, ino ndiyo nthawi yolimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova, kuti m’tsogolomu tikam’khulupilile kwathunthu.
17. Kodi tidzapindula bwanji na ciweluzo ca Yehova pamapeto a dzikoli?
17 Ganizilani mmene tidzamvelela kukhala m’dziko latsopano la Mulungu, podzaona zotsatilapo zabwino cifukwa ca ciweluzo ca Yehova. Cipembedzo conyenga, mabungwe a zamalonda adyela, komanso maboma andale amene amapondeleza anthu na kubweletsa mavuto ambili, sizidzakhalakonso. Matenda, ukalamba, na imfa, zidzacotsedwapo. Ndipo Satana na ziŵanda zake adzamangidwa zaka 1,000. Mavuto onse amene iwo abweletsa cifukwa ca kupanduka kwawo adzathetsedwa. (Chiv. 20:2, 3) Tidzakondwela ngako kuti tinakhulupilila mmene Yehova amacitila zinthu!
18. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Aisiraeli pa Numeri 11:4-6 komanso 21:5?
18 Kodi n’kutheka kuti umoyo m’dziko latsopano, ungadzabweletse zovuta zina zimene zingadzayese cikhulupililo cathu pa njila imene Yehova amacitila zinthu? Mwacitsanzo, ganizilani zinacitika Aisiraeli atangomasulidwa mu ukapolo ku Iguputo. Ena anayamba kudandaula cifukwa coyewa zakudya zabwino zimene anasiya ku Iguputo, ndipo anafika ngakhale ponyoza mana amene Yehova anali kuwapatsa. (Ŵelengani Numeri 11:4-6; 21:5.) Kodi nafenso tingadzakhale na mzimu wodandaula pambuyo pa cisautso cacikulu? Sitidziŵa kuti padzakhala nchito yoculuka motani yoyeletsa dziko lapansi, kuti pang’ono-m’pang’ono likhale paladaiso. N’zoonekelatu kuti padzakhala nchito zambili zofunika kugwila, ndipo zina mwa izo zidzakhala zovuta poyamba. Kodi tidzadandaula na zimene Yehova adzatipatse pa nthawiyo? Mfundo pano ni yakuti: Ngati pali pano timayamikila zimene Yehova amatipatsa, tidzayamikila koposa zimene iye adzatipatse panthawiyo.
19. Kodi mwacidule mungafotokoze motani mfundo zazikulu m’nkhani ino?
19 Njila ya Yehova yocitila zinthu imakhala yabwino nthawi zonse. Mfundo imeneyi tisamaiiwale. Tizikhulupililanso aja amene Yehova amawadalila kuti adzacita zimene iye waauza. Ndipo tizikumbukilanso mawu ake mwa mneneli Yesaya akuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.”—Yes. 30:15.
NYIMBO 98 Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu
^ ndime 5 Nkhani ino, itithandiza kuona kufunika kokulitsa cidalilo cathu mwa Yehova, komanso aja omuimilako padziko lapansi. Tionenso mmene kucita zimenezi kungatipindulitsile, na kutikonzekeletsa zovuta za kutsogolo.
^ ndime 9 Nthawi zina, pangakhale zifukwa zomveka kuti wofalitsa kapena banja, lisasamukile ku mpingo watsopano. Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2002, “Bokosi la Mafunso.”