Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 52

Thandizani Ena Kupilila pa Nthawi Zovuta

Thandizani Ena Kupilila pa Nthawi Zovuta

“Usalephele kucitila zabwino anthu amene akufunikila zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kucita zimenezo.”—MIY. 3:27.

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi Yehova nthawi zambili amayankha bwanji mapemphelo a atumiki ake?

 KODI mudziŵa kuti Yehova angakuseŵenzetseni poyankha pemphelo locokela pansi pa mtima la munthu wina? Angakuseŵenzetseni kaya ndinu mkulu, mtumiki wothandiza, mpainiya, kapena wofalitsa mu mpingo. Inde, mungathandize wina mosasamala kanthu kuti ndinu wacicepele kapena wacikulile, m’bale kapena mlongo. Munthu wokonda Yehova akafuulila kwa iye kuti am’thandize, Mulungu wathu nthawi zambili amagwilitsa nchito atumiki ena okhulupilika kuti ‘athandize ndi kulimbikitsa’ munthuyo. (Akol. 4:11) Ni mwayi wapadela cotani nanga kutumikila Yehova na abale athu mwa njila imeneyi! Tingatelo pa nthawi ya mlili, ya tsoka, kapena ya mazunzo.

THANDIZANI ENA PA NTHAWI YA MLILI

2. N’cifukwa ciyani zingakhale zovuta kuthandiza ena pa nthawi ya mlili?

2 Pakabuka mlili wa matenda, zingativute kuti tithandizane. Mwacitsanzo, tingafune kucezela anzathu, koma kucita zimenezo kungatiike pa ciwopsezo coyambula matenda. Tingafune kuitanila aja amene ali na vuto la zacuma kuti tidzadye nawo cakudya, koma izi zingakhalenso zosatheka. Mwina tingafunenso kuthandiza ena, koma kucita izi nakonso kungakhale kovuta ngati ena m’banja lathu akudwala. Ngakhale n’conco, timafunabe kuthandiza abale athu, ndipo Yehova amakondwela tikacita zimene tingathe kuti tiwathandize. (Miy. 3:27; 19:17) Nanga tingacite ciyani?

3. Tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca akulu a mu mpingo wa mlongo Desi? (Yeremiya 23:4)

3 Zimene akulu angacite. Ngati ndinu mkulu, zidziŵeni bwino nkhosa. (Ŵelengani Yeremiya 23:4.) Mlongo Desi amene tinam’gwila mawu m’nkhani yapita anati, “Akulu a m’kagulu kathu kumbuyoku anali kuyenda nane mu ulaliki komanso na abale ena, ndipo anali kukhala nafe pa maceza.” b Kulimbika kwa akulu amenewo kunapangitsa kuti zikhale zosavuta kwa iwo kum’thandiza mlongo Desi pamene ena a m’banja lake anamwalila na mlili wa COVID-19.

4. Kodi akulu anakwanitsa bwanji kuthandiza Mlongo Desi? Nanga pali phunzilo lotani?

4 Mlongo Desi anafotokoza kuti, “Cifukwa akulu anali kale mabwenzi anga, zinakhala zosavuta kwa ine kuwauza mmene n’nali kumvela ndiponso nkhawa zanga.” Kodi inu akulu muphunzilapo ciyani? Wetani nkhosa zimene zili pansi pa cisamalilo canu vuto lisanabwele. Khalani bwenzi lawo. Ngati kwabuka mlili umene ukulepheletsani kuwayendela ku nyumba kwawo, seŵenzetsani njila zina. Mlongo Desi anati, “Nthawi zina akulu angapo anali kunitumila foni kapena kunilembela mauthenga pa tsiku limodzi. Malemba amene anakambilana nane ananikhudza mtima, ngakhale kuti n’nali kuwadziŵa bwino malembawo.”

5. Kodi akulu angadziŵe bwanji zimene abale na alongo afunikila kuti awathandize?

5 Njila imodzi imene mungadziŵile zimene abale na alongo anu afunikila, ni kuwafunsa mafunso mosamala kuti afotokoze za mu mtima mwawo. (Miy. 20:5) Kodi ali na cakudya cokwanila, mankhwala, na zofunikila zina? Kodi zioneka kuti nchito yawo ingathe kapena akhoza kusoŵa pokhala cifukwa colephela kulipila lendi? Kodi afunikila kuwathandiza kuti alembetse kulandilako mathandizo a boma? Mlongo Desi analandila thandizo la kuthupi kucokela kwa alambili anzake. Koma cinam’thandiza maka-maka kupilila mavuto ake, ni cikondi ca akulu na cilimbikitso cawo cauzimu. Iye anati: “Akulu anali kupemphela nane. Ngakhale kuti sinikumbukila bwino zimene anali kukamba m’pemphelo, nikumbukila mmene n’nali kumvela. N’nali kumva monga Yehova akuniuza kuti, ‘Suli wekha.’”—Yes. 41:10, 13.

M’bale amene akutsogoza msonkhano ni wokondwa kumva ndemanga zolimbikitsa za ambili amene apezekapo, kuphatikizapo m’bale wodwala amene walumikiza kupitila pa vidiyo (Onani ndime 6)

6. N’ciyani cimene ambili mu mpingo angacite kuti athandize ena? (Onani cithunzi.)

6 Zimene ena angacite. Timayembekezela akulu kukhala patsogolo kusamalila abale na alongo mu mpingo. Koma Yehova akupempha tonsefe kulimbikitsa ena na kuwathandiza. (Agal. 6:10) Ngakhale zazing’ono zimene tingacite poonetsa cikondi munthu wodwala, zingam’limbikitse kwambili. Wacicepele angatumizile m’bale kakhadi kapena cithunzi cojambula pa manja kuti am’limbikitse. Wacinyamata angathandizeko mlongo pa zina zake, monga kukamugulilako zinthu ku sitolo. Mwina mungakonze cakudya cimene mungacipeleke ku nyumba kwa munthu wodwala, mosamala kuti musayambule matenda. Komabe, tidziŵa kuti mlili ukabuka, aliyense mu mpingo amafunikila cilimbikitso. Mwina mungakhalileko pang’ono pambuyo pa msonkhano kuti mucezeko na abale na alongo, kaya pamaso-m’pamaso kapena kupitila pavidiyo. Ndipo akulu nawonso amafunikila cilimbikitso. Iwo amakhala otangwanika zedi pa nthawi ya mlili, ndipo Mboni zina zawalembelapo mawu owayamikila. Zimakhala zolimbikitsa kwambili tikacita mbali yathu ‘popitiliza kutonthozana na kulimbikitsana’!—1 Ates. 5:11.

THANDIZANI ENA PA NTHAWI YA TSOKA

7. Kodi pangakhale mavuto otani tsoka likacitika?

7 Tsoka likacitika, umoyo wa anthu ungasokonezeke kothelatu m’kanthawi kocepa. Katundu na nyumba zawo zingawonongeke, ndipo angatayikilidwe ngakhale anthu amene amawakonda. Zocitika zoipa ngati zimenezi zimacitikilanso abale na alongo athu. Nanga tingacite ciyani kuti tiwathandize?

8. N’ciyani cimene akulu na mitu ya mabanja angacite tsoka lisanacitike?

8 Zimene akulu angacite. Inu akulu, thandizani abale anu kukhala okonzeka tsoka lisanacitike. Onetsetsani kuti onse mu mpingo adziŵilatu zoyenela kucita kuti akakhale otetezeka, komanso mmene angadzakambilane na akulu. Mlongo Margaret amene tinam’chula m’nkhani yapita, anati: “Akulu mu mpingo mwathu anakonza nkhani ya zofunikila za mpingo, yoticenjeza kuti nyengo ya moto wa m’nkhalango inali isanathe. Anatiuza kuti ngati a boma angatiuze kuti tisiye nyumba zathu, kapena ngati zinthu zingafike poipa kwambili, tiyenela kucoka mofulumila.” Amenewo anali malangizo a pa nthawi yake, cifukwa patangopita milungu isanu, moto woopsa wa m’nkhalango unabuka. Pa kulambila kwa pa banja, mitu ya mabanja ingakonze zakuti akambilane zimene aliyense m’banja angadzacite. Ngati inu ndi ana anu ndinu okonzeka, mungadzakhalebe odekha tsoka likadzacitika.

9. Kodi akulu angaseŵenzele bwanji pamodzi tsoka lisanacitike komanso likacitika?

9 Ngati ndinu woyang’anila kagulu ka ulaliki, onetsetsani kuti muli na manambala a foni komanso maadresi olondola a aliyense wa m’kagulu kanu tsoka lisanacitike. Lembani zinthu zimenezi, na kumaonetsetsa kuti n’zolondola. Ndiyeno tsoka likacitika, mudzatha kulankhulana na wofalitsa aliyense kuti mupeleke thandizo lofunikila. Mwamsanga dziŵitsani mgwilizanitsi wa bungwe la akulu, amene adzadziŵitsa woyang’anila dela. Abale onsewa akaseŵenza mogwilizana, angathandize kwambili. Pambuyo pa moto uja, woyang’anila dela m’dela la mlongo Margaret sanagone kwa maola 36 cifukwa anali kugwilizanitsa nchito za akulu. Akuluwo anali kuyesetsa kulankhulana komanso kusamalila abale na alongo 450 amene anasiya nyumba zawo. (2 Akor. 11:27) Conco, onse amene analibe kokhala anawapezela malo.

10. N’cifukwa ciyani akulu amaona kucita ubusa kukhala kofunika kwambili? (Yohane 21:15)

10 Akulu ali na udindo wopeleka thandizo lauzimu kwa abale na alongo, komanso kulimbikitsa amene ali na nkhawa. (1 Pet 5:2) Pakagwa tsoka, coyamba akulu ayenela kuonetsetsa kuti m’bale na mlongo aliyense ni wotetezeka, ali na cakudya, zovala komanso pokhala. Koma kwa miyezi ndithu pambuyo pake, opulumuka tsokawo angafunikile kuwalimbikitsa mwauzimu na kuwatonthoza. (Ŵelengani Yohane 21:15.) M’bale Harold wa m’Komiti ya Nthambi, amene anakambilanapo na abale na alongo ambili amene akhudzidwapo na matsoka anati, “Zimatenga nthawi kuti ayambe kuiŵala zimene zinawagwela. Iwo angaiŵale zinthu zina zimene anatayikilidwa. Koma zingatenge nthawi kuti aiŵale wokondedwa wawo amene anafa pa tsokalo, cuma cawo ca mtengo wapatali cimene cinatayika, kapena mmene analipulumukila tsokalo. Pokumbukila zimenezi, angayambenso kumva cisoni. Izi zikacitika n’cibadwa kumva conco, osati kuti alibe cikhulupililo.”

11. Kodi mabanja angafunikilebe cilimbikitso cotani pambuyo pa tsoka?

11 Akulu saiŵala mfundo yakuti ayenela ‘kulila ndi anthu amene akulila.’ (Aroma 12:15) Opulumuka tsoka angafunike kuwatsimikizila kuti Yehova komanso abale na alongo awo sanaleke kuwakonda. Akulu angafunike kuthandiza mabanja kupitiliza na pulogilamu yawo ya zauzimu, imene ingaphatikizepo kupemphela, kuŵelenga, kusonkhana, na kulalikila. Iwo angalimbikitsenso makolo kuthandiza ana awo kuika maganizo pa zinthu zimene sizingawonongeke tsoka likagwa. Inu makolo, kumbutsani ana anu kuti Yehova nthawi zonse adzakhala Bwenzi lawo, ndipo nthawi zonse adzakhala wokonzeka kuwathandiza. Afotokozeleni kuti adzakhalabe m’banja la padziko lonse la abale na alongo amene ni okonzeka kuwathandiza.—1 Pet. 2:17.

Kodi mungadzipeleke kuti muthandize ena m’dela lanu mukacitika tsoka? (Onani ndime 12) e

12. Kodi ena angacite ciyani kuti athandize pa nchito yopeleka thandizo pakagwa tsoka? (Onani cithunzi.)

12 Zimene ena angacite. Tsoka likacitikila kufupi na kwanu, funsani akulu mmene mungathandizile. Mwina mungadzipeleke kuti kwa kanthawi mulandileko aja amene anasiya nyumba zawo kaamba ka tsoka, kapena aja amene akugwila nchito yopeleka thandizo pa tsokalo. Ngati n’zotheka mungapeleke cakudya na zofunikila zina kwa ofalitsa ofunikila thandizo. Ngati tsoka lacitikila kutali kwambili na kwanu, mungathandizebe. Motani? Mwa kupemphelela okhudzidwa na tsokalo. (2 Akor. 1:8-11) Mungacilikize nchito yopeleka thandizo pakagwa tsoka mwa kucita zopeleka zothandizila pa nchito ya padziko lonse. (2 Akor. 8:2-5) Ngati mungathe kupita kumene kwacitika tsoka kuti mukathandize, funsani akulu zimene mungacite. Mukaitanidwa kuti mukathandize, mwacionekele mudzalandila maphunzilo kuti mukathandize bwino kumene mungafunikile kwambili.

THANDIZANI ABALE KUPILILA MAZUNZO

13. Ni mavuto otani amene abale athu amakumana nawo m’maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa?

13 M’maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa, umoyo umakhala wovuta kwambili cifukwa mumakhalanso kuzunzidwa. Kuwonjezela pa zimenezi, abale amenewo amakumananso na mavuto a zacuma, kudwala, na kutayikilidwa okondedwa awo mu imfa. Ndipo cifukwa ca ciletso, zingakhale zovuta kwa akulu kuyendela abale ofunikila cilimbikitso, kapena kulankhulana nawo. Ili ndilo vuto limene m’bale Andrei nayenso, mkulu amene tinam’chula m’nkhani yapita anakumana nalo. Mlongo wina m’kagulu kake ka ulaliki anali na mavuto a zacuma. Mwatsoka lanji, mlongoyo anapezekanso m’ngozi ya galimoto. Iye anafunikila maopaleshoni angapo, moti sakanathanso kugwila nchito. Mosasamala kanthu za ziletso na mlili, abale anacita zimene akanatha pofuna kuthandiza, ndipo Yehova anali kuona kuyesetsa kwawo.

14. Kodi akulu angapeleke bwanji citsanzo codalila Yehova?

14 Zimene akulu angacite. M’bale Andrei anali kupemphela na kucita zimene akanakwanitsa. Kodi Yehova anawayankha bwanji mapemphelo ake? Iye anagwilitsa nchito abale na alongo amene anali na ufulu woyendela abale ena. Ena anali kupeleka mlongoyo ku cipatala na magalimoto awo. Ndipo ena anam’patsa ndalama zom’thandiza. Yehova ndiye anawalimbikitsa kucita zinthu mogwilizana komanso molimba mtima, kuti mlongoyo athandizike. (Aheb. 13:16) Inu akulu, nchito yathu ikaletsedwa pemphani ena kuti akuthandizeni. (Yer. 36:5, 6) Koposa zonse, dalilani Yehova. Iye adzakuthandizani kukwanilitsa zosoŵa za abale na alongo athu.

15. Kodi tingasunge bwanji mgwilizano wathu monga Akhristu pa nthawi ya mazunzo?

15 Zimene ena angacite. Pa nthawi ya ciletso, tingafunike kumakumana m’tumagulu. Conco kuposa kale lonse, m’pofunika kwambili kukhalabe mwamtendele na abale athu. Muzilimbana na Satana, osati abale anu. Nyalanyazani zolakwa za abale anu, kapena yesetsani kuthetsa mwamsanga kusamvana kulikonse kumene kungakhalepo. (Miy. 19:11; Aef. 4:26) Khalani wokonzeka kuthandizana wina na mnzake. (Tito 3:14) Thandizo limene ena anapeleka kwa mlongo wofunikila thandizo uja linakhala na zotulukapo zabwino ku kagulu kawo ka ulaliki. Iwo anakhala ogwilizana kwambili monga banja.—Sal. 133:1.

16. Malinga na Akolose 4:3, 18, kodi tingawathandize bwanji abale na alongo athu amene akuzunzidwa?

16 Abale na alongo athu ofika m’masauzande akutumikilabe Yehova ngakhale kuti boma linaika ziletso pa nchito yathu. Ena a iwo ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. Tiziwapemphelela, na kupemphelela mabanja awo, komanso aja amene amapeleka thandizo lauzimu, lakuthupi, na kuwakhalila kumbuyo m’makhoti. c (Ŵelengani Akolose 4:3, 18.) Musapeputse mphamvu ya mapemphelo anu.—2 Ates. 3:1, 2; 1 Tim. 2:1, 2.

Kodi mungakonzekele bwanji mazunzo palipano? (Onani ndime 17)

17. Kodi mungakonzekele bwanji mazunzo palipano?

17 Inu na banja lanu yambani tsopano kukonzekela mazunzo. (Mac. 14:22) Musamaganizile zoipa zonse zimene mungadzakumane nazo. M’malo mwake, limbitsani ubwenzi wanu na Yehova, ndipo thandizani ana anu kucita cimodzimodzi. Mukakhala na nkhawa, mukhuthulileni nkhawa zanuzo Mulungu. (Sal. 62:7, 8) Ndipo kambilanani monga banja cifukwa cake mungam’dalile Mulungu. d Kukonzekela kwanu matsoka pasadakhale na kudalila Yehova, kudzathandiza ana anu kukhala olimba mtima komanso kukhala na mtendele pokumana na mazunzo.

18. Kodi tikuyembekezela tsogolo lotani?

18 Mtendele wa Mulungu umatipangitsa kumva kukhala otetezeka. (Afil. 4:6, 7) Yehova amagwilitsa nchito mtendele umenewu potonthoza mtima yathu, mosasamala kanthu za matenda, matsoka, komanso mazunzo amene tingakumane nawo. Amagwilitsa nchito akulu olimbikila kuti azitiŵeta. Ndipo tonsefe watipatsa mwayi wothandizana wina na mnzake. Mtendele umene tingakhale nawo palipano ungatipatse mpata wokonzekela mayeso aakulu kutsogolo, ngakhale “cisautso cacikulu.” (Mat. 24:21) Pa nthawi ya cisautsoco, tidzafunika kusungabe mtendele wathu, na kuthandiza ena kutelo. Koma cisautsoco cikadzatha, sitidzakumananso na mavuto amene amatibweletsela nkhawa. Ndipo pamapeto pake, tidzasangalala na mtendele wosatha umene Yehova amafunitsitsa kuti tikakhale nawo.—Yes. 26:3, 4.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

a Nthawi zambili, Yehova amagwilitsa nchito atumiki ake okhulupilika kuti athandize aja amene akukumana na mavuto. Angaseŵenzetse inu kuti mulimbikitse abale na alongo anu. Tiyeni tione mmene tingathandizile ena akafunikila thandizo.

b Maina ena asinthidwa.

c Ofesi ya nthambi kapena a kulikulu salola kulandila makalata ocokela kwa abale kuti awatumizile kwa abale na alongo ali m’ndende.

d Onani nkhani yakuti “Konzekelani Cizunzo Pali Pano,” mu Nsanja ya Mlonda ya July 2019.

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Banja labweletsela cakudya banja limene lili mu msasa woyembekezela pambuyo pa tsoka.